1Tsiku lina akuluakulu ena a Aisraele adadza kwa ine nadzakhala pansi pamaso panga.
2Tsono Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
3“Iwe mwana wa munthu, anthu ameneŵa aika mtima pa mafano ao, aikanso maso ao pa zinthu zina zophunthwitsa. Kodi iwoŵa akuganiza kuti ndidzaŵayankha akadzapempha nzeru kwa Ine?
4Tsono uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ngati Mwisraele wina aliyense aika mtima pa mafano ake, naikanso maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, kenaka nkupita kwa mneneri, Ineyo Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha moyenerana ndi kuchuluka kwa mafano ake.
5Ndidzatero kuti mwina mwake nkukopanso mitima ya Aisraele amene andisiya chifukwa cha mafano ao.
6“Nchifukwa chake uŵauze Aisraele kuti Ineyo Ambuye Chauta ndikunena kuti, ‘Lapani, mulekane nawo mafano anu. Muzisiye zonyansa zanu zonse.’
7Ngati munthu wina aliyense, Mwisraele kapena mlendo wongokhala nao, andikana Ine, naika mtima pa mafano ake, ndi kuika maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, munthu woteroyo akabwera kudzapempha nzeru kwa Ine, kudzera mwa mneneri, Ine Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha.
8Ndiye kuti ndidzalimbana naye munthu ameneyo. Ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anga. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
9“Ngati mneneri anyengedwa nalosa, ndine Chauta amene ndamnyenga. Ndipo ndidzamkantha ndi dzanja langa ndi kumchotsa pakati pa anthu anga Aisraele.
10Chilango cha mneneriyo ndi cha munthu amene adadzapempha nzeru kwa iyeyo, chidzalingana.
11Ndidzachita zimenezi kuti Aisraele asandithaŵenso, ndipo kuti asiye machimo ao. Pamenepo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Munthu aliyense adzafera zake12Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
13“Iwe mwana wa munthu, dziko likandichimwira, posandikhulupirira Ine, ndidzalikantha ndi dzanja langa ndi kuchepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala m'dzikomo, ndipo ndidzaononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe.
14Ngakhale anthu atatu aŵa, Nowa, Daniele ndi Yobe, akadakhala kumeneko, akadangopulumutsa moyo wao wokha chifukwa cha kukhulupirika kwao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
15Mwina ndikadatumiza zilombo kuti ziyende m'dzikomo ndi kuwononga anthu ake, mpaka dzikolo kusanduka chipululu chakuti munthu sangadutsemo chifukwa cha zilombo.
16Apo ngakhale anthu atatu aja akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja sakadatha kupulumutsa ngakhale ana ao omwe. Akadangopulumutsa moyo wao wokha, koma dzikolo likadasanduka chipululu ndithu.
17“Mwina ndikadatumiza nkhondo ku dziko limenelo ndi kulamula kuti ipite m'dzikomo ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe.
18Apo ngakhale anthu atatu aja akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja sakadapulumutsa ngakhale ana ao, akadangodzipulumutsa iwo okha.
19“Mwina ndikadatumiza mliri m'dziko limenelo, ndi kuwonetsa ukali wanga pokhetsa magazi ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe.
20Apo ngakhale Nowa, Daniele ndi Yobe akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja akadadzipulumutsa iwo okha chifukwa cha kulungama kwao, koma ana ao ai.
21 Chiv. 6.8 “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzagwetsa pa Yerusalemu zilango zanga zinai izi: nkhondo, njala, zilombo ndi mliri, kuti ziwononge anthu ndi nyama.
22Koma ena adzatsalako m'dzikomo odzatulutsa ana aamuna ndi aakazi, muŵapenyetsetse akadza kwa inu, muwone m'mene akhalire ndi zimene achite. Mitima yanu idzakhazikika pansi, mukakumbukira zoipa zimene ndachita ku Yerusalemu, chilango chonse chimene ndalanga nacho mzindawo.
23Mitima yanu idzakhaladi pansi, poona m'mene iwo akhalira ndi zimene akuchita, ndipo mudzamvetsa kuti Yerusalemu sindidamchite zimenezi popanda chifukwa. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.