3Mfumu idamufunsa kuti, “Kodi kwagwanji, iwe mfumukazi Estere? Wadzapempha chiyani? Ndidzakupatsa ngakhale likhale hafu la ufumu wanga.”
4Apo Estere adayankha kuti, “Ngati zingakukomereni amfumu, inuyo mubwere pamodzi ndi Hamani lero lino ku chakudya chamadzulo chimene ndakonzera inu amfumu.”
5Apo mfumu idati, “Bwera nayeni msanga Hamaniyo, kuti tichite zimene akufuna Estere.” Choncho mfumu idafika pamodzi ndi Hamani ku chakudya chamadzulo chimene adaakonza Estere.
6Pamene ankamwa vinyo, mfumu idafunsa Estere kuti, “Kodi ukupempha chiyani? Chopempha chakocho ndidzakupatsa. Tanena, ukupempha chiyani? Ngakhale likhale hafu la ufumu wanga, ndidzakupatsa ndithu.”
7Koma Estere adayankha kuti, “Chopempha changa ndiponso chimene ndikukhumba ndi ichi:
8Ngati mwakondwera nane inu amfumu, ndipo chikakukomerani kuti mundipatse zimene ndapempha, ndi kundininkhadi chimene ndikukhumba, mubwere inuyo pamodzi ndi Hamani maŵa ku chakudya chamadzulo chimene ndidzakukonzereni. Maŵalo ndidzachita monga momwe mwanenera amfumu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.