1Nkosafunikira kuti ndikulembereni za zopereka zothandizira anthu a Mulungu a ku Yudeya.
2Ndikudziŵa kuti mumafunadi kuthandiza, ndipo ndimakunyadirani kwa anthu a ku Masedoniya chifukwa cha chimenechi. Ndimaŵauza kuti, “Abale a ku Akaiya adakonzeka kale chaka chatha kuti athandize.” Ndipo changu chanu chautsa ena ambiri.
3Koma ndikutuma abale athuŵa, kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kusakhale kwachabe, koma kuti mukhaledi okonzeka monga momwe ndidaanenera.
4Ngati anthu ena a ku Masedoniya adzandiperekeze ndi kukupezani muli osakonzeka, tidzachita manyazi kwambiri kuti tinkakunyadirani pachabe, koma makamaka inuyo ndiye mudzachite manyazi kwambiri.
5Nchifukwa chake ndidaganiza kuti ndiyenera kupempha abale ameneŵa kuti abwere kwa inu ndisanafike ineyo, ndipo kuti akonzeretu mphatso imene mudalonjeza kale. Pamenepo mphatsoyo idzakhala yokonzekeratu, ndipo idzakhaladi mphatso yeniyeni, osati kanthu kamene mwapereka mokakamizidwa.
6Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.
7Mphu. 20.10-15Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.
8Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
9Mas. 112.9 Za munthu wotere paja Malembo akuti,
“Wapereka mphatso zake moolowa manja kwa anthu osauka.
Chilungamo chake nchamuyaya.”
10 Yes. 55.10 Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu.
11Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko.
12Zoonadi ntchito imeneyi yomwe mukuchitira anthu a Mulungu, siingoŵathandiza pa zosoŵa zao, komanso chotsatira chake china nchakuti anthu ochuluka adzathokoza Mulungu kwambiri.
13Pakuti ntchito imeneyi ikuŵatsimikizira kuti chifundo chanu nchoona, iwo adzatamanda Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu povomereza Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Adzatero chifukwanso cha ufulu wanu poŵagaŵirako iwowo ndi anthu ena onse zinthu zimene muli nazo.
14Tsono adzakuwonetsani chikondi chao ndi kukupemphererani, chifukwa Mulungu wakukomerani mtima kopitirira.
15Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso yake yosaneneka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.