1Yesu atatsiriza kulankhula nkhani zonsezi, adauza ophunzira ake kuti,
2 Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima.
38Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, komatu mukhale maso pamodzi nane.”
39Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
40Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Mongadi nonsenu mwalephera kukhala maso pamodzi nane ngakhale pa kanthaŵi kochepa?
41Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
42Adachokanso kachiŵiri nakapemphera kuti, “Atate, ngati chikho chamasautsochi sichingandichoke, mpaka nditamwa ndithu, chabwino, zimene mukufuna zichitike.”
43Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera.
44Yesu adaŵasiyanso, napita kukapemphera kachitatu, akunena mau amodzimodzi omwe aja.
45Pambuyo pake adabwera kwa ophunzira ake nati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Ndipotu nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa anthu ochimwa.
46Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.”
Yesu agwidwa(Mk. 14.43-50; Lk. 22.47-53; Yoh. 18.3-12)47Yesu akulankhula choncho, wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda.
48Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo, mukamugwire.”
49Tsono Yudasi adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Moni Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona.
50Yesu adamuuza kuti, “Bwenzi langa, chita zimene wadzera.” Apo anthu aja adabwera namugwira Yesu.
51Koma wina mwa amene anali limodzi ndi Yesu, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu.
52Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga.
53Kodi ukuyesa kuti Ine sindingapemphe Atate, Iwo nthaŵi yomweyo nkunditumizira magulu ankhondo a angelo oposa khumi ndi aŵiri?
54Koma ndikadatero, nanga zikadachitika bwanji zimene Malembo adaneneratu kuti ziyenera kuchitika?”
55 Lk. 19.47; 21.37 Pamenepo Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kudzandigwira muli ndi malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira.
56Koma zonsezi zachitika kuti ziwonekedi zimene aneneri adalemba.”
Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumusiya yekha.
Yesu ku Bwalo Lalikulu la Ayuda(Mk. 14.53-65; Lk. 22.54-56, 63-71; Yoh. 18.12-14, 19-24)57Tsono anthu amene adagwira Yesu aja adapita naye kunyumba kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda.
58Koma Petro ankamutsatira chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adaloŵa m'kati, nakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu kuti aone m'mene zithere.
59Akulu a ansembe aja ndi onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni wonama woneneza Yesu kuti amuphe.
60Koma sadaupeze ngakhale padaabwera mboni zambiri zabodza. Potsiriza padabwera anthu aŵiri.
61Yoh. 2.19Adati, “Munthu uyu ankati, ‘Ine ndingathe kupasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu.’ ”
62Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?”
63Koma Yesu adangokhala chete. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adauza Yesu kuti, “Ndikukulamula m'dzina la Mulungu wamoyo kuti utiwuze molumbira ngati ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu.”
64Dan. 7.13Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha. Komanso ndikukuuzani kuti kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.”
65Lev. 24.16Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake nati, “Kunyoza Mulungu koopsatu kumeneku! Kodi pamenepa nkufunanso mboni zina ngati? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku.
66Ndiye inu mukuganiza bwanji?” Iwo aja adayankha kuti, “Ayenera kuphedwa.”
67 Yes. 50.6 Pomwepo iwo adayamba kumthira malovu kumaso nkumamumenya, ena kumamuwomba makofi,
68nkumanena kuti, “Iwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, nanga sindiwe mneneri? Lota, wakumenya ndani?”
Petro akana Yesu(Mk. 14.66-72; Lk. 22.56-62; Yoh. 18.15-18, 25-27)69Petro adaakhala kunja m'bwalo la nyumba ija. Mtsikana wina wantchito adabwera namuuza kuti, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.”
70Koma iye adakana pamaso pa anthu onse, adati, “Sindikuzidziŵa zimenezo ine.”
71Pamene Petro ankatuluka kumapita ku chipata, mtsikana winanso wantchito adamuwona, nayamba kuuza amene anali pamenepo kuti, “Akulu ameneŵa anali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.”
72Petro adakananso molumbira kuti, “Ndithudi sindikumdziŵa munthu ameneyo.”
73Ndipo patangopita kanthaŵi, anthu amene anali pamenepo adadza nauza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli, tadziŵira kalankhulidwe kakoka.”
74Apo Petro adayamba kulumbira nkumanena kuti, “Mulungu andilange, munthu mukunenayu ine sindimdziŵa konse.” Nthaŵi yomweyo tambala adalira.
75Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo adatuluka, nakalira misozi ndi chisoni chachikulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.