1 Sam. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adani alanda Bokosi lachipangano.

1Tsiku lina Aisraele adatuluka kukamenyana nkhondo ndi Afilisti. Adamanga zithando zankhondo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti adamanga zithando zao ku Afeki.

2Afilisti adandanda kuyang'ana Aisraele, ndipo adayamba kumenyana. Nkhondo itakula, Afilisti adagonjetsa Aisraele napha Aisraele 4,000 pomenyaniranapo.

3Pamene magulu ankhondo adafika ku zithando, atsogoleri a Aisraele adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani Chauta walola kuti Afilisti atigonjetse? Tiyeni tikatenge Bokosi lachipangano la Chauta ku Silo, kuti Chautayo abwere pakati pathu ndipo atipulumutse kwa adani athu.”

4Eks. 25.22Choncho adatuma anthu ku Silo kukatenga Bokosi lachipangano la Chauta Wamphamvuzonse wokhala pa akerubi. Ana aŵiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, adapita nao pamodzi ndi Bokosi lachipanganolo ku zithando zankhondo zija.

5Pamene Bokosi lachipangano la Chauta lidafika kuzithandoko, Aisraele onse adayamba kufuula kwambiri, kotero kuti nthaka idagwedezeka.

6Afilisti atamva phokoso la kufuulako adati, “Kodi kufuula kwakukulu kotere ku zithando za Ahebriku nkwa chiyani?” Atamva kuti Bokosi lachipangano la Chauta lafika kuzithandoko,

7Afilistiwo adachita mantha poti ankati, “Kwafika milungu kumeneko.” Ndipo adati, “Tsoka ife! Chinthu choterechi sichidachitikepo nkale lonse.

8Tili m'mavuto! Angathe ndani kutipulumutsa kwa milungu yamphamvuyi? Imeneyitu ndi milungu ija idapha Aejipito ndi miliri ya mtundu uliwonse m'chipululu muja.

9Limbani mtima, chitani chamuna, inu Afilisti, kuwopa kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga momwe iwowo analiri akapolo anu. Chitani chamuna, menyani nkhondo.”

10Motero Afilisti adamenya nkhondo ndipo Aisraele adagonjetsedwa kotheratu, nathaŵira kwao. Nthaŵiyo kudaphedwa Aisraele okwanira 30,000, ankhondo oyenda pansi.

11Ndipo Bokosi lachipangano la Chauta lidalandidwa. Ana aŵiri aja a Eli, Hofeni ndi Finehasi, nawonso adaphedwa.

Imfa ya Eli.

12Munthu wina wa fuko la Benjamini adathaŵa kunkhondoko nakafika ku Silo tsiku lomwelo. Anali atang'amba zovala zake ndi kudzithira dothi kumutu, kuwonetsa chisoni.

13Atafika, adapeza Eli atakhala pa mpando pambali pa mseu akungoyang'ana, poti ankadera nkhaŵa Bokosi lachipangano la Chauta lija. Pamene Mbenjamini uja adaloŵa mumzindamo, nayamba kusimba zimene zidaachitika kunkhondoko, anthu onse amumzinda adalira kwambiri.

14Eli atamva kulirako, adafunsa kuti, “Kodi kulira kumeneku ndiye kuti kwachitika chiyani?” Tsono munthu uja adapita msanga kwa Eli, nayamba kumufotokozera.

15Nthaŵiyo nkuti Eli ali nkhalamba ya zaka 98, maso ake atachita khungu, kotero kuti sankathanso kupenya.

16Munthuyo adauza Eli kuti, “Ine ndine amene ndachoka ku nkhondo. Ndathaŵa kumeneko lero lomwe.” Eli adamufunsa kuti, “Nanga nkhondo yayenda bwanji, mwana wanga?”

17Iye adayankha kuti, “Aisraele athaŵa Afilisti ndipo anthu ophedwa pakati pathu ngambirimbiri. Ana anu onse aŵiri aja, Hofeni ndi Finehasi, aphedwa, nalonso Bokosi lachipangano la Chauta lalandidwa.”

18Pamene adangotchula za Bokosi lachipangano la Chauta, Eli adagwa chankhongo, kuchoka pa mpando wake pafupi ndi chipata. Adathyoka khosi naafa, poti adaali wokalamba ndiponso wonenepa kwambiri. Anali atatsogolera Aisraele zaka makumi anai.

Imfa ya mkazi wa Finehasi.

19Nthaŵiyo mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali ndi pathupi ndipo anali pafupi kuchira. Pamene adamva zakuti Bokosi lachipangano la Chauta lidalandidwa, ndiponso kuti Eli, mpongozi wake, pamodzi ndi mwamuna wake adafa, zoŵaŵa za pobala mwana zidamfikira mwadzidzidzi, mwana nkumabadwa.

20Popeza kuti mkaziyo anali pafupi kufa, akazi omuthandiza adamuuza kuti, “Limba mtima, wabala mwana wamwamuna.” Koma iye sadayankhe ngakhale kusamalako ai.

21Tsono mwanayo adamutchula dzina loti Ikabodi, ndiye kuti, “Ulemerero wachoka kwa Aisraele!” Adatero chifukwa chakuti Bokosi lachipangano la Mulungu linali litalandidwa, ndiponso chifukwa cha imfa ya Eli mpongozi wake ndi ya mwamuna wake.

22Mau ake anali omwewo akuti, “Ulemerero wachoka kwa Aisraele poti Bokosi lachipangano la Chauta lalandidwa.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help