Eks. 33 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta alamula Aisraele kuchoka ku phiri la Sinai

1 Gen. 12.7; Gen. 26.3; Gen. 28.13 Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Uchokeko kuno pamodzi ndi anthu amene udabwera nawo kuchokera ku Ejipito, ndipo upite ku dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Pa nthaŵi imeneyo ndidaŵauza iwowo kuti, ‘Dziko limeneli ndidzalipatsa kwa zidzukulu zanu.’

2Ndidzatuma mngelo patsogolo pako, ndipo ndidzapirikitsa Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.

3Pitani ku dziko lamwanaalirenji. Koma Ine sindidzapita nanu chifukwa ndinu anthu okanika, ndipo ndingathe kukuwonongani panjira.”

4Tsono anthu atamva mau oopsaŵa, adayamba kulira, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adavala zovala zokongola.

5Ndiye kuti Chauta anali atauza Mose kuti, “Uza Aisraelewo kuti, ‘Ndinu anthu okanika. Ndikadapita nanu pamodzi, ngakhale kamphindi kakang'ono kokha, bwenzi nditakuwonongani kwathunthu. Tsopano vulani zokongoletsa zanu, ndipo ndidzadziŵa choti ndingathe kukuchitani.’ ”

6Motero kuyambira ku phiri lija la Horebu, Aisraele sadavalenso zokongoletsa.

Chihema chokumaniranako Chauta ndi anthu ake

7Mose ankatenga chihema chija ndi kukachimanga kunja kwake kwa mahema, chapatali ndithu. Tsono adachitcha chihemacho dzina loti, “Chihema chamsonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Chauta ankatuluka kumahemako, napita ku chihema chamsonkhanocho.

8Nthaŵi zonse Mose akamapita kuchihemako, anthu onse ankaimirira. Tsono aliyense ankangoimirira pakhomo pa hema lake, namayang'ana Moseyo mpaka ataloŵa m'chihema chokumaniranako ndi Chauta chija.

9Mose ataloŵa m'chihema muja, mtambo unkatsika nuphimba pakhomo pa chihemacho, ndipo Chauta ankalankhula ndi Mose kuchokera mumtambomo.

10Ndipo anthu ankati akaona mtambowo pa khomo la chihemacho, ankaimirira ndi kupembedza, aliyense pa khomo la hema lake.

11Choncho Chauta ankalankhula ndi Mose pamasompamaso, monga momwe munthu amalankhulira ndi bwenzi lake. Tsono pambuyo pake Mose ankabwerera kumahema komweko. Koma mnyamata wina, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, amene anali mtumiki wa Mose, sankachoka kuchihemako.

Lonjezo lakuti Chauta adzakhalapo

12Mose adauza Chauta kuti, “Mwakhala mukundiwuza kuti ndiŵatsogolere anthuŵa ku dzikolo, koma simudandiwuze amene mudzamtuma kuti apite nane. Komabe mwanena kale kuti, ‘Ndikukudziŵa bwino iwe, ndipo ndakondwa nawe.’

13Nchifukwa chake tsono ndikukupemphani kuti ngati mwandikomera mtima, mundilangize njira zanu kuti ndikudziŵeni ndipo mupitirize kundikomera mtima. Kumbukiraninso kuti mtundu wa anthu uwu ndi wanu ndithu.”

14Ndipo Mulungu adati, “Ine ndemwe ndidzapita nawe pamodzi, ndipo ndidzakupatsa mtendere.”

15Apo Mose adauza Chauta kuti, “Mukapanda kupita nafe limodzi, musatilole kuti tichoke pano.

16Nanga zidzadziŵika bwanji kuti mwandikomera mtima ine pamodzi ndi anthu anu? Kodi si chifukwa chakuti mumapita nafe, ine pamodzi ndi anthu anu, kuti tizikhala osiyana ndi anthu ena onse a pa dziko lapansi?”

17Tsono Chauta adauza Moseyo kuti, “Ndidzachita monga wanena, chifukwa ndakukomera mtima, ndipo ndikukudziŵa bwino.”

18Apo Mose adapempha Chauta kuti, “Chonde mundiwonetse ulemerero wanu.”

19Aro. 9.15 Pamenepo Chauta adayankha kuti, “Ndikudzakuwonetsa ulemerero wanga wonse, ndipo ndidzatchula dzina langa loti Chauta pamaso pako. Ndidzakomera mtima amene nditi ndimkomere mtima, ndipo ndidzachitira chifundo amene nditi ndimchitire chifundo.”

20Chauta adaonjeza kuti, “Koma sungathe kuwona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu angathe kundiwona Ine, nakhala moyo.”

21Adapitirira kunenanso kuti, “Pafupi ndi Ine pano pali thanthwe, iwe uimirire pathanthwepo.

22Tsono ulemerero wanga ukamapita, ndikuika mu mng'alu wa thanthwe, ndipo ndikuphimba ndi dzanja langa mpaka nditabzola.

23Kenaka ndichotsa dzanja langa, ndipo undiwona kumsana, koma nkhope yanga suiwona ai.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help