Nyi. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Akazi

1Iwe wokongola koposa akazi onsewe,

kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti?

Kodi wokondedwa wakoyo waloŵera potani,

kuti tichite kukuthandiza kumfunafuna?

Mkazi

2Wokondedwa wanga watsikira kumunda kwakeku,

ku timinda ta mbeu zokometsera chakudya.

Akukadyetsa ziŵeto zake ku minda

ndiponso akukathyola akakombo.

3Wokondedwa wangayo ine ndine wake,

ndipo iyeyo ndi wangawanga.

Amadyetsa ziŵeto zake pakati pa akakombo.

Nyimbo Yachisanu

Mwamuna

4Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola ngati Tiriza,

wa maonekedwe abwino ngati Yerusalemu,

ndiwe wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo

mbendera zili m'manja.

5Usandipenyetsetse,

pakuti maso ako amanditenga mtima.

Tsitsi lako likuchita pekupeku ngati mbuzi,

zoti zikutsetsereka pa mapiri a ku Giliyadi.

6Mano ako ali mbee ngati nkhosa zometa,

zoti angozisambitsa kumene.

Mano onsewo ngoyang'anana bwino,

palibe chigwelu nchimodzi chomwe.

7Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo,

masaya ako akuwoneka ngati mabandu a makangaza.

8Mfumu ili ndi akazi enieni

makumi asanu ndi limodzi,

ili ndi akazi aang'ono

makumi asanu ndi atatu,

ilinso ndi anamwali tayetaye!

9Koma ine nkhunda yanga, wangwiro wanga,

ndi mmodzi yekha basi,

mwana mmodzi yekha wa amai ake,

mwana wapamtima wa amai ake.

Anamwali atamuwona, adamutcha wodala.

Akazi enieni a mfumu

ndi akazi onse aang'ono adamtamanda.

10Ndani uyu wooneka ngati mbandakuchayu,

wokongola ngati mwezi,

woŵala ngati dzuŵa,

wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo

mbendera zili m'manja?

11Ndidatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi,

kuti ndikayang'ane maluŵa akuchigwa,

kuti ndikaone ngati mipesa idaphukira,

ngati makangaza adachita maluŵa.

12Ndisanazindikireko kanthu,

ndidakhala ngati ndikulota

kuti ndili m'galeta pambali pa mfumu yanga.

Akazi

13Bwerera, bwerera,

iwe namwali wa ku Sulami,

bwerera kuti tidzakupenyetsetse.

Mkazi

Chifukwa chiyani mukuti

mudzandipenyetsetse ine Msulamine,

pamene ndikuvina pakati pa magulu aŵiri?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help