1Anthu a Mulungu okhulupirira amafa,
ndipo palibe amene amasamalako.
Anthu okhulupirika amatengedwa,
ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake.
Anthu olungama amachotsedwa, kuti tsoka lisaŵagwere,
2ndipo amafa mwamtendere.
Amene ali olungama amapumula bwino pogona pao.
3Senderani kuno, inu anthu ochita zoipa,
pakuti muli ngati zidzukulu zam'chigololo,
zochokera m'zadama.
4Kodi inu mukuseŵera ndi yani?
Kodi mukunena yani?
Mukunyoza yani?
Kodi ochimwa sindinu?
Onyenga sindinu?
5Mumapembedza mafano pa mitengo ya thundu,
patsinde pa mtengo wogudira uliwonse.
Mumapereka ana anu ngati nsembe m'zigwa,
m'ming'alu yam'mathanthwe.
6Mumatenga miyala yosalala kumadamboko,
ndi kumaipembedza ngati milungu.
Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa iyo,
ndi kuperekanso chopereka cha chakudya.
Kodi zimenezi zingandikondweretse?
7Pa phiri lalitali ndi looneka kutali
mudakaika bedi kukachita zadama,
komwekonso mudakapereka nsembe.
8M'nyumba mwanu mwaika mafano ku
chitseko ndiponso pa mphuthu.
Ine mwandisiya, mwavula zovala zanu,
mwakwera pa bedi lanu lalikulu ndi zibwenzi zanu
zimene mwazilipira kuti mugone nazo.
Kumeneko mwakwaniritsa zilakolako zanu zoipa.
9Mudadzola mafuta ndi zonunkhira zochuluka,
ndipo mudapita kukapembedza fano lija la Moleki.
Mudachita kutuma nthumwi kutali,
mudazituma ngakhale kumanda komwe.
10Mudatopa nawo mtunda wouyenda,
koma osanena kuti, “Ndingoleka!”
Mudapezera zina mphamvu,
mwakuti simudalefuke konse.
11“Kodi ndi milungu yanji imene mudaiwona
nkuchita nayo mantha,
kotero kuti mudandinamiza nkundiiŵaliratu,
osalabada konse za Ine?
Kodi mwaleka kundiwopa
chifukwa choti ndakhala chete pa nthaŵi yaitali?
12Mukuganiza kuti zimene mumachita nzolungama,
koma makhalidwe anu ndidzaŵaonetsa poyera,
ndipo mafano sadzakuthandizani.
13Mukamafuula kufuna chithandizo,
mafano anuwo akupulumutseni!
Mphepo idzaiyalula milunguyo, mpweya udzaiwulutsa.
Koma amene amakhulupirira Ine,
adzalandira dziko lokhalamo,
ndi kumapembedza pa phiri langa loyera.”
Mulungu alonjeza chipulumutso14Padzamveka mau akuti,
“Lambulani, lambulani ndi kukonza mseu.
Chotsani chitsa chilichonse pa njira yodzeramo
anthu anga.”
15Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse,
amene alipo nthaŵi zonse,
ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti,
“Ndimakhala pa malo aulemu, oyera.
Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa
ndi olapa mu mtima,
kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha,
olapawo ndiŵalimbitse mtima.
16“Ndine amene ndidalenga anthu anga
ndi kuŵapatsa mpweya wa moyo,
motero sindidzapitirira kukangana nawo
kapena kuŵakwiyira mpaka muyaya.
17“Ndidaŵakwiyira chifukwa anali okonda chuma dziŵi.
Tsono ndidaŵalanga, ndi kuŵafulatira mokwiya.
Koma iwowo adakhalabe ouma mitu,
ndipo adapitirira kuchita ntchito zao zoipa.
18“Ndidaona m'mene ankachitira,
komabe ndidzaŵachiritsa.
Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza.
Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao.
19 Aef. 2.17 Anthu onse akutali ndi apafupi,
ndidzaŵapatsa mtendere.
Ndidzachiritsa anthu anga.
20Koma anthu oipa ali ngati nyanja yoŵinduka,
yosatha kukhala bata,
ndipo mafunde ake amangoponya matope ndi ndere.
21 Yes. 48.22 Palibe mtendere kwa oipa,”
akutero Mulungu wanga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.