1 Sam. 25 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Imfa ya Samuele.

1Samuele adamwalira. Ndipo Aisraele onse adasonkhana kudzalira maliro ake, namuika kumudzi kwao ku Lama.

Davide ndi Abigaile.

Masiku amenewo Davide adanyamuka, napita ku chipululu cha Parani.

2Tsono panali munthu wina ku Maoni amene anali ndi kadziko ku dera la mudzi wa Karimele. Munthuyo anali wolemera kwambiri. Anali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Tsiku lina adayamba kumeta nkhosa zake ku Karimele.

3Munthuyo anali Nabala, wa fuko la Kalebe, ndipo mkazi wake anali Abigaile. Mkaziyo anali wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wakeyo anali wouma mtima ndi wankhanza. Anali wa fuko la Kalebe.

4Davide anali atamva kuchipululu kuja kuti Nabala akumeta nkhosa zake.

5Choncho adatuma anyamata khumi kuti, “Pitani ku phiri la Karimele kwa Nabala, mukandiperekere moni.

6Mukamulonjere motere: mukati mbuye wathu akuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu ndi banja lanu ndi zinthu zonse zimene muli nazo.

7Ndikumva kuti muli ndi anthu ometa nkhosa. Pamene abusa anu anali nafe kuno, sitidaŵachite choipa chilichonse, ndipo sadasoŵe kanthu pa nthaŵi yonse pamene adakhala ku Karimele.

8Muŵafunse antchito anuwo, adzakuuzani. Nchifukwa chake muŵakomere mtima anyamata anga, pakuti tabwera nthaŵi ino yachikondwerero. Chonde muŵapatse anyamata angaŵa ndi ine bwenzi lanu Davide, chilichonse chimene mungakhale nacho.’ ”

9Tsono anyamata a Davide aja atafika, adafotokozera Nabala zonse zimene Davide adaaŵauza. Ndipo iwowo adayembekeza.

10Nabala adayankha anyamata a Davide aja poŵafunsa kuti, “Kodi Davide mwana wa Yese ndani? Ha! Masiku ano pali anthu antchito ambiri amene akuthaŵa kwa ambuyao.

11Kodi ndingatenge chakudya changa, madzi anga, nyama yanga imene ndaphera anyamata anga ometa nkhosa, kuti ndipatse anthu omwe sindikudziŵa kumene akuchokera?”

12Choncho anyamata a Davide adapotoloka, nabwerera kukauza Davide zonsezo.

13Apo Davide adauza ankhondo ake kuti, “Munthu aliyense amangirire lupanga lake.” Choncho aliyense adamangirira lupanga lake. Davide nayenso adamangirira lake. Anthu amene adapita ndi Davide analipo ngati 400. Koma anthu 200 adatsalira kuti azisunga katundu.

14Tsono wanchito wina adauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, “Davide adatuma amithenga kuchokera ku chipululu kuti adzalonjere mbuyathu, koma iwo adaŵakalipira.

15Komabe anthu amenewo adatichitira zabwino osati zoipa, poti sitidasoŵe kanthu nthaŵi zonse pamene tinali ndi iwowo ku busa.

16Ankatichinjiriza ngati linga usana ndi usiku, nthaŵi zonse pamene tinali ndi iwowo poŵeta nkhosa ku Rama.

17Tsono ndati mudziŵe zimenezi, ndipo muganizirepo zoti muchite, pakuti zimenezi zidzaonongetsa mbuyathu pamodzi ndi banja lao lonse. Chinanso nchakuti mbuyathu aja ndi a khalidwe lovuta, kotero kuti wina aliyense sangathe kulankhula nawo.”

18Tsono mwamsanga Abigaile adatenga mitanda yabuledi 200, matumba achikopa aŵiri a vinyo, nkhosa zisanu zootcheratu, makilogramu 17 a tirigu wokazinga, nchinchi za mphesa zoumika 100, ndiponso makeke ankhuyu 200. Zonsezo adazisenzetsa abulu.

19Kenaka adauza anyamata ake antchito kuti, “Batsogolani, ine ndikudza pambuyo panu.” Koma sadauze Nabala mwamuna wake.

20Tsono mkaziyo atakwera pa bulu ndi kufika patsinde pa phiri lina, adangoona Davide ndi ankhondo ake akubwera kwa iye. Ndipo mkaziyo adakumana nawo.

21Nthaŵiyo nkuti Davide atanena kuti, “Ndithudi ndidavutika pachabe kutchinjiriza zinthu zonse za munthu ameneyu, zimene anali nazo ku chipululu, kotero kuti palibe kanthu nkamodzi komwe pa zinthu zakezo kamene kadasoŵa. Koma iye wandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.

22Mulungu andilange ndithu ngati m'maŵa ndikhale nditasiyapo ngakhale munthu wamwamuna mmodzi mwa anthu onse amene ali nawo.”

23Abigaile ataona Davide, adatsika pa bulu msangamsanga, nadzigwetsa chafufumimba pamaso pake.

24Ali chigonere choncho ku mapazi a Davide adati, “Mbuyanga, mlandu ugwere ine ndekha basi. Chonde mulole mdzakazi wanune kuti ndilankhule nanu, ndipo mumve mau anga.

25Mbuyanga asasamale za amuna anga, munthu wa mkhalidwe wovuta uja. Monga momwe dzina lake liliri, iyenso ali choncho. Monga dzina lake limatanthauzira kuti chitsiru, zake zonse nzauchitsiru basi. Koma ine mdzakazi wanu, sindidaŵaone anyamata anu amene mudaaŵatumawo.

26Tsono mbuyanga, ndi Chauta yemwe amene wakuletsani kuti musaphe munthu ndi kulipsira ndi manja anu. Inu muli apa, pali Chauta wamoyo, ndikulonjeza molumbira kuti onse amene afuna kukuchitani choipa, adzalangidwa ngati Nabala.

27Pepani, nazi mphatsozi zimene mdzakazi wanune ndabwera nazo kwa inu mbuyanga, kuti zipatsidwe kwa anthu muli nawoŵa.

28Chonde, mukhululukire cholakwa cha ine mdzakazi wanu. Zoonadi, Chauta adzakhazikitsa banja lanu mu ufumu, poti mukummenyera nkhondo. Motero choipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu.

29Ngati anthu akuukirani namakulondolani kuti akupheni, Chauta Mulungu wanu adzakusungani, monga m'mene munthu amasungira chuma m'phukusi. Koma moyo wa adani anu, Iye adzautaya kutali, monga m'mene munthu amaponyera mwala ndi khwenengwe.

30Inu mbuyanga, Chauta adzakuchitirani zabwino zonse zimene adakulonjezani, ndipo adzakuikani kuti mukhale mfumu yolamulira Aisraele.

31Nthaŵi imeneyo inu simudzamva chisoni kapena kuvutika mu mtima kuti mudakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Ndipo pamene Chauta adzakuchitirani zabwino zonsezi, musadzandiiŵale ine mdzakazi wanu.”

32Apo Davide adauza Abigaile kuti, “Inu mai, atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, amene wakutumani kuti mukumane nane lero.

33Mulungu akudalitseni chifukwa cha nzeru zimene mwaonetsa lero pondiletsa kuti ndisakhetse magazi ndi kulipsira ndi manja anga.

34Chauta, Mulungu wa Israele, ndiye wandiletsa kuti ndisakupwetekeni. Zoonadi, pali Chauta, Mulungu wamoyo, mukadapanda kudzakumana nane msanga, ndithu sipakadamtsalira Nabala munthu wamwamuna ndi mmodzi yemwe maŵa m'maŵa.”

35Motero Davide adalandira kwa mkaziyo zimene adaamtengera, namuuza kuti, “Pitani kunyumba kwanu ndi mtendere. Mau anu ndaŵamva ndipo zopempha ndavomera.”

36Abigaile adabwerera kwa Nabala nampeza m'nyumba mwake akuchita phwando lalikulu ngati la mfumu. Nabala anali wosangalala mumtima mwakwe, poti anali ataledzera kwambiri. Tsono mkazi wakeyo sadamuuze kanthu kalikonse mpaka m'maŵa kutacha.

37M'maŵa mwake, m'maso mwa Nabala mutayera, mkazi wakeyo adamuuza zonse. Pomwepo Nabala mtima wake udaima, ndipo thupi lidangoti gwa ngati mwala.

38Patapita masiku khumi, Chauta adakantha Nabala naafa.

39Tsono Davide atamva kuti Nabala wafa, adati, “Atamandike Chauta amene walipsira chipongwe chimene adandichita Nabala, ndipo wandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choipa. Chauta wabwezera pamutu pa Nabala ntchito zake zoipa.” Tsono Davide adatuma anyamata ake kukafunsira mbeta Abigaile kuti akhale mkazi wake.

40Anyamata a Davide atafika kwa Abigaile ku Karimele, adamuuza kuti “Mfumu Davide watituma kuti tikutengeni, mukakhale mkazi wake.”

41Mkaziyo adagwada nagunditsa nkhope yake pansi, nati, “Ine mdzakazi wa mbuyanga Davide, ndili wokonzeka ngakhale kusambitsa mapazi a anyamata ake.”

42Motero Abigaile adanyamuka mofulumira nakwera pa bulu, ndipo pamodzi ndi anamwali ake asanu amene ankamtumikira, adatsata amithenga a Davide aja, nakakhala mkazi wake wa Davide.

43Davide anali atakwatira Ahinowamu wa ku Yezireele, ndipo aŵiri onsewo adakhala akazi ake.

442Sam. 3.14-16Paja Saulo anali atakwatitsa mwana wake Mikala, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Laisi wa ku Galimu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help