1Tsono ndidaona Chauta ataima pambali pa guwa.
Adati,
“Gwetsani makapotolosi a Nyumba ya Mulungu,
kuti maziko ake agwedezeke.
Muŵagwetsere pamitu pa anthu.
Onse otsalira Ine ndidzaŵapha pa nkhondo.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathaŵe.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumukepo.
2“Ngakhale akakumbe pansi mpaka ku malo a anthu akufa,
dzanja langa lidzaŵadukhululako kumeneko.
Ngakhale akakwere mpaka kumwamba,
ndidzaŵatsakamutsako.
3Ngakhale akabisale pamwamba pa phiri la Karimele,
ndidzaŵaunguza nkuŵagwira.
Ngakhale akabisale pansi pa nyanja yaikulu,
ndidzalamula chilombo cham'nyanjamo kuti chiŵalume.
4Ngakhale adani ao aŵakusire ku ukapolo,
komweko ndidzalamula kuti aphedwe pa nkhondo.
Ndidzaŵayang'anitsitsa kuti ziŵagwere zoipa
osati zabwino.”
5Ambuye Chauta Wamphamvuzonse, akakhudza dziko,
limanyenyeka,
ndipo zonse zokhala m'menemo zimalira.
Apo dziko lonse limafufuma ngati mtsinje wa Nailo
ndipo limateranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.
6Ndiwo amene amamanga malo ao okhalamo kumwamba,
naika thambo ngati denga la dziko lapansi,
amaitana madzi akunyanja
naŵakhuthulira pa dziko lapansi.
Iwowo dzina lao ndi Chauta.
7“Kwa Ine, Aisraelenu muli ngati Aetiopiya.”
Akuterotu Chauta.
“Kodi sindine uja ndidatulutsa Aisraele ku Ejipito?
Kodi sindine uja ndidatulutsa Afilisti
ku Kafitori ndi Asiriya ku Kiri?
8Ine, Ambuye Chauta,
maso anga ali pa dziko lochimwalo,
ndipo ndidzalifafaniza pa dziko lapansi.
Komabe banja la Yakobe lokha
sindidzaliwononga kotheratu.”
Akuterotu Chauta.
9“Ai, ndidzalamula,
ndipo ndidzagwedeza Aisraele uku ndi uku
pakati pa mitundu yonse ya anthu
monga momwe amagwedezera sefa uku ndi uku,
popanda kamwala nkamodzi komwe kogwa pansi.
10Adzafera pa nkhondo anthu anga onse ochimwa,
iwo amene amati,
‘Chilango sichidzatifika,
kapena kutipambana.’ ”
Otsalira apulumuka11 Ntc. 15.16-18 Chauta akuti,
“Nthaŵi imeneyo ndidzakwezanso ufumu wa Davide
umene udagwa ngati nyumba.
Ndidzakonzanso makoma ake ogumuka
ndi kumanganso mabwinja ake.
Ndidzaubwezeranso mwake mwakale.
12Nthaŵi imeneyo Aisraele otsala adzagonjetsa
zimene zatsala za ku Edomu,
pamodzi ndi maiko onse
amene amadziŵika ndi dzina langa.”
Akuterotu Chauta,
amene adzachitedi zimene wanenazi.
13Chauta akunena kuti,
“Nthaŵi ikubwera pamene mlimi adzabzola wokolola,
ndipo woponda mphesa adzabzola wobzala mbeu.
M'mapiri mudzatuluka vinyo wokoma,
azidzachita kuyenderera pa zitunda zonse.
14“Ndidzaŵabwezeranso pabwino anthu anga Aisraele.
Adzamanganso mizinda yamabwinja ndi kumakhalamo.
Adzalima minda ya mphesa ndipo adzamwa vinyo wake.
Adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
15Ndidzaŵakhazikanso m'dziko mwao,
ndipo palibe amene adzaŵachotsemo
m'dziko limene ndidzaŵapatsalo.”
Akuterotu Chauta, Mulungu wanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.