Mphu. 38 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za matenda ndi mankhwala

1Sing'anga uzimpatsa ulemu woyenerera,

chifukwa cha ntchito zimene amakuchitira,

paja nayenso adamlenga ndi Ambuye.

2Nzeru zake zochizira zimachokera kwa Mulungu

Wopambanazonse,

ndipo mafumu amamulipira.

3Sing'anga nzeru zake zimamsandutsa wokwera,

ndipo akuluakulu amamulemekeza.

4Ambuye adalenga mankhwala kuchokera m'nthaka,

ndipo munthu wanzeru saŵanyoza.

5 Eks. 15.23-25 Kodi suja kamtengo kadakometsa madzi nthaŵi ija,

kuti mphamvu za Ambuye zidziŵike?

6Ambuye amapatsa anthu nzeru

kuti aŵayamike chifukwa cha ntchito zao zodabwitsa.

7Sing'anga amachiza zoŵaŵa ndi mankhwala amenewo.

Katswiri wa mankhwala ndiye amene amasakaniza

mankhwalawo mwa nzeru zake.

8Choncho ntchito za Ambuye nzosatha,

amapereka moyo pa dziko lonse lapansi.

9Mwana wanga, ngati ukudwala, usadzilekerere,

koma upemphere kwa Ambuye ndipo adzakuchiritsa.

10Leka zolakwa zako, usaipitse manja ako,

ndipo ulapiretu mu mtima machimo ako onse.

11Pereka nsembe zofukiza lubani

ndi za ufa wosalala,

uthire mafuta pa zopereka zako

monga ungathere.

12Tsono uitane sing'anga,

poti nayenso adamulenga ndi Ambuye.

Usamufulatire,

chifukwa ukumusoŵadi.

13Ilipo nthaŵi pamene kuchira kwako

kumakhala m'manja mwa asing'anga.

14Paja iwonso amachita kupempha Ambuye

kuti aŵathandize pa ntchito yao

yochepetsa zoŵaŵa ndi yochiza,

kuti apulumutse moyo wa anthu.

15Munthu akachimwira Mlengi wake,

adzipereke m'manja mwa sing'anga.

16 Mphu. 22.11, 12 Mwana wanga, umkhetsere misozi munthu wakufa.

Poti uli ndi chisoni chachikulu,

uyambe ndiwe kulira kwambiri.

Uike mtembo wake m'manda potsata mwambo,

usaleke kuŵalemekeza manda akewo.

17Misozi yako ikhale yambiri

kulira kwako kukhale kwakukulu,

monga kuyenera munthuyo.

Ulire masiku angapo, kuwopa kuti anthu angakunene,

ndipo uthuze mtima ndi kuleka chisoni.

18Paja chisoni chimafikitsa munthu ku imfa,

ndipo mtima wachisoni umathetsa mphamvu.

19Pa mazunzo chisoni chimapitirira,

moyo wongokhala ndi chisoni

umapsinja mtima.

20Tsono usalekerere mtima wako

kukhala wa chisoni chonyanya.

Uleke chisonicho,

ukumbukire kuti nawenso udzafa.

21Usaiŵale kuti wakufa sadzabwereranso.

Sungathe kumthandiza,

ndiye ungodzipweteka.

22Kumbukira kuti zimene zachitikira iye,

iwenso zidzakuchitikira.

“Ladzulo linali lake, lalero nlako.”

23Wakufa ataikidwa, usamkumbukirenso,

iye atakusiya, iwe ukhazike mtima pansi.

Za ntchito zina

24Nzeru za mlembi zimapezeka

munthu akaona mpata wokwanira wophunzira,

amene satanganidwa ndi zambiri

angathe kukhala wanzeru.

25Kodi angakhale bwanji ndi nzeru

munthu wongoyendetsa pulao,

amene amangonyadira kukhala ndi mkwapulo m'manja?

Amangoyendetsa ng'ombe zake nkuzama m'ntchito za ng'ombezo,

nkhani zokamba ndi za ng'ombe basi.

26Amangolimbikira kulima mizere,

nkumagwira ntchito mpaka usiku

kuti adyetse anaang'ombe.

27Chimodzimodzinso anthu aluso ndi amisiri

amene amagwira ntchito usana ndi usiku.

Ena amazokota zosindikizira,

namayesayesa kusiyanitsa zithunzi zolembapo.

Amaika mtima pa za kulemba bwino

chithunzi cholingana ndi chifanizo.

Ndipo amachezera usiku

kuti aitsirize ntchito yaoyo.

28Chimodzimodzinso mmisiri wosula,

amene amakhala pafupi ndi mwala wosulirapo.

Iye amangoganiza zosula bwino chitsulo chake.

Mpweya wotentha wa moto umakhwinyatitsa khungu lake.

Iye uja amalimbanadi ndi moto wam'ng'anjo.

Kulira kwa nyundo kumamgonthetsa makutu,

maso ake amangokhala pa chinthu chimene akusulacho.

Amangofuna kumaliza ntchito yake,

ndipo amaigwira mpaka usiku kuti aitsirize bwino.

29Chimodzimodzinso munthu woumba mbiya,

amene ali pa ntchito yake,

amazunguza mkombero ndi mapazi ake.

Amatanganidwa kwambiri ndi ntchito yake

kuti akwaniritse chiŵerengero

cha mbiya zofunika.

30Amakumba dothi ndi dzanja lake,

nalipondaponda ndi mapazi yake.

Amalimbikira kuti aikulungize bwino,

ndipo amachezera kuti atsuke uvuni bwino lomwe.

31Amisiri onsewo amadalira manja ao,

ndipo aliyense ali ndi luso pa ntchito yake.

32Popanda anthu otereŵa, mzinda sungamangike,

ndipo anthu sangathe kukhalamo,

alendo sangadzereko.

33Koma anthu otere simuŵapeza pa bwalo lokambirana,

kapena pa malo aulemu pa msonkhano.

Sakhala pa mipando ya oweruza,

samvetsa zogamula za pa bwalo la milandu.

Sadziŵa kufotokoza za mwambo ndi za kuweruza,

ndipo sapezeka pakati pa anthu onena miyambi.

34Komabe ntchito zao nzothandiza zedi kutukula

dziko lino lapansi.

Pa mapemphero ao amangoganiza za ntchito yao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help