Mik. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za anthu ozunza osauka

1Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu,

amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa.

Akadzuka m'maŵa amakazichitadi,

pakuti mphamvu zake ali nazo.

2Akasirira minda, amailanda.

Akakhumbira nyumba, amazilanda.

Amavutitsa munthu ndi banja lake,

naŵatengera zonse zimene ali nazo.

3Nchifukwa chake zimene akunena Chauta ndi izi:

“Imvani, ndidzakufitsirani tsoka

chifukwa cha zoipa zonsezi.

Ndidzakuvekani goli m'khosi mwanu,

limene simungathe kulivula.

Apo simudzayendanso monyada,

chifukwa nthaŵi imeneyo idzakhala yoipa.

4Tsiku limenelo anthu adzakupekerani

nthano yokunyodolani,

adzakuimbani nyimbo yamaliro,

adzati,

‘Taonongeka kotheratu.

Dziko limene Chauta adatigaŵira,

bwanji afuna kutilanda!

Minda yathu aigaŵira amene atigwira ukapolo.’ ”

5Tsono pa nthaŵi imene Chauta

adzabwezeranso dziko kwa anthu ake,

inuyo simudzalandirako gawo lililonse.

6Anthu amandiwuza kuti,

“Musatilalikire,

munthu asalalike zimenezi.

Manyazi sadzatigwera ai.

7Monga zoterezi nzoyenera kuzinena,

inu a banja la Yakobe?

Kodi kuleza mtima kwa Chauta kwatheratu?

Kodi zimenezi nzimene adachita?

Kodi mau ake sadzetsa zabwino

kwa munthu woyenda molungama?”

8Chauta akuti,

“Koma inu mumaukira anthu anga ngati mdani.

Mumaŵavula mkanjo anthu amtendere,

amene amangoyenda ndi mtima wokhazikika,

osaganizako za nkhondo.

9Akazi a anthu anga mumaŵatulutsa

m'nyumba zao zokoma.

Ndipo ana ao mumaŵalanda madalitso anga kosalekeza.

10Nyamukani, chokani,

ano simalo opumulirapo.

Zonyansa zanu zaŵaipitsa,

zadzetsapo chiwonongeko choopsa.

11Munthu wina atamapita uku ndi uku

akulalika zabodza kuti,

‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo

ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’

mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde.

12“Koma inu banja lonse la Yakobe,

ndidzakusonkhanitsani.

Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi

ngati nkhosa m'khola,

ngati gulu la zoŵeta pa busa lake.

Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.”

13Woŵapulumutsa adzaŵatsogolera,

ndipo onse adzathyola pa chipata nathaŵa.

Idzayambira ndi mfumu yao kudutsa,

Chauta adzakhala patsogolo pao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help