Yud. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yuditi akhulupirika ndithu ku chipembedzo chake

1Pamenepo Holofernesi adalamula atumiki ake kuti aloŵetse Yuditi m'hema m'mene munali mbale zake zasiliva. Tsono adaitanitsa chakudya cha m'hema mwake, pamodzi ndi vinyo kuti apatse Yuditi.

2Koma Yuditi adati, “Chakudya chimenechi sindidya, chifukwa ndikuwopa kuphwanya malamulo athu.

3Chakudya chimene ndabwera nacho chindikwanira.” Holofernesi adamuuza kuti, “Ukadya chakudya chonse chimene uli nacho, nanga china tikupezera kuti? Pakati pathu pano palibe wina wa mtundu wako.”

4Yuditi adayankha kuti, “Pepani, pali inu mbuye wanga, chakudya chimene ndili nacho sichitha, Ambuye asanachite zimene akufuna kuchita kudzera mwa ine.”

5Atumiki a Holofernesi adamloŵetsa m'hema, ndipo Yuditi adagona mpaka pakati pa usiku.

6M'maŵa kusanache adadzuka natumiza uthenga kwa Holofernesi kuti, “Mbuye wanga, ndapota nanu, mundilole ndituluke tsopano, ndikapemphere.”

7Holofernesi adalamula alonda ake kuti alole Yuditi kutuluka. Motero adakhala masiku atatu m'mahemamo, namatuluka usiku uliwonse kumapita ku chigwa cha Betuliya, kukasamba ku kasupe.

8Ankati akabwera kuchokera kumadziko, ankapemphera kwa Ambuye, Mulungu wa Israele, kuti adalitse ntchito yake yopulumutsa anthu ake.

9Choncho ankabwerera ku zithando ali woyeretsedwa pa za chipembedzo, ndipo ankakhala m'hemamo mpaka nthaŵi yakudya chakudya chamadzulo.

Holofernesi akonza phwando

10Pa tsiku lachinai lake Holofernesi adakonzera phwando atumiki ake akuluakulu okhaokha, osaitana ndi mmodzi yemwe mwa atsogoleri ake ena ankhondo.

11Adauza Bagowasi, mdindo wofulidwa woyang'anira zinthu zake zonse kuti, “Pita kwa mkazi Wachihebri uja amene umamsamala, ukamnyengerere kuti abwere adzadye ndi kumwa nafe.

12Nzochititsa manyazi kuti mai wotereyu nkupanda kukhala naye malo amodzi. Ndikalephera kumkumbatira, adzandiseka.”

13Bagowasi adachoka pamaso pa Holofernesi, napita kwa Yuditi kukamuuza kuti, “Iwo achiphadzuŵa asachite manyazi, abwere kwa mbuye wanga, ndi kudzalandira ulemu pokhala nawo pa phwando. Adzamwe nafe ndi kusangalala. Ndipo lero akhale ngati mmodzi mwa akazi a ku Asiriya, amene amatumikira ku nyumba ya Nebukadinezara.”

14Yuditi adayankha kuti, “Ndine yani ine, kuti ndingamkanire mbuye wanga? Ndidzachita zonse zimene iye akufuna, ndipo zidzandipatsa chimwemwe mpaka tsiku la kufa kwanga.”

15Atatero Yuditi adavala zovala zake zokongola. Mdzakazi wake adatsogolako, ndipo zikopa zankhosa zimene Bagowasi adampatsa kuti azipumulirapo tsiku ndi tsiku, adakaziyala pamaso pa Holofernesi, kuti Yuditi akhalepo pakudya.

16Yuditi ataloŵa, nakhala pamalo pake, Holofernesi adatengeka mtima pomuwona. Adanyamuka mtima mpaka kuyamba kulakalaka kwambiri kuti amnyenge. Ndithudi, ankafunitsa kumnyenga kuyambira tsiku limene adamuwona koyamba.

17Motero adamuuza kuti “Imwa ndipo usangalale nafe.”

18Yuditi adayankha kuti, “Chabwino, mbuye wanga, ndimwa ndi kusangalala nanu. Lero ndi tsiku lalikulu kwambiri pa moyo wanga.”

19Tsono adatenga zimene mdzakazi wake adakonza, ndipo adadya ndi kumwa zomwezo pamaso pake.

20Holofernesi adasangalala kwambiri pompenya, ndipo adamwa vinyo kupambana tsiku lina lililonse pa moyo wake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help