1Chauta ndiye Mfumu,
anthu a pa dziko lapansi akondwere,
anthu onse a m'mbali mwa nyanja asangalale.
2Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta.
Amalamulira molungama,
mu ufumu wake mulibe tsankho.
3Moto umapita patsogolo pake,
umapsereza adani ake omzinga kulikonse.
4Zing'aning'ani zake zimaŵalitsa dziko lonse lapansi,
dziko lonse limapenya nkugwedezeka.
5Mapiri amasungunuka ngati sera pamaso pa Chauta,
ndiye wolamulira dziko lonse lapansi.
6Zakumwamba zimalalika za kulungama kwake,
ndipo anthu a mitundu yonse amaona ulemerero wake.
7Onse opembedza milungu yonama,
amene amanyadira mafano achabechabe,
amachititsidwa manyazi,
pakuti milungu ina yonse imagonjera Chauta.
8Anthu a ku Ziyoni akumva,
ndipo akusangalala,
midzi ya ku Yuda nayonso ikukondwera
chifukwa cha kaweruzidwe kanu, Inu Chauta.
9Pakuti Inu Chauta ndinu Wopambanazonse,
wolamulira dziko lonse lapansi.
Ndinu amphamvu kupambana milungu yonse.
10Chauta amakonda anthu odana ndi zoipa.
Iye amasunga moyo wa anthu ake oyera mtima.
Amaŵapulumutsa kwa anthu oipa.
11Amaŵalira anthu amene amamumvera,
ndipo anthuwo amakhaladi ndi chimwemwe.
12Inu ndi anthu a Chauta, kondwerani mwa iye,
ndipo mumthokoze potchula dzina lake loyera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.