1“Koma tsopano inu aYobe, mverani mau anga,
mutchere khutu ku zonse zimene ndinene.
2Tsopano ndiyamba kulankhula,
ndikuuzani za mumtima mwanga.
3Mau anga akusonyeza kulungama kwa mtima wanga,
zimene ndimazidziŵa ndimalankhula moona.
4Mzimu wa Mulungu udandiwumba.
Mpweya wa Mphambe udandipatsa moyo.
5Mundiyankhe ngati mungathe.
Mulankhule mau anu tsatanetsatane pamaso panga,
konzekani tsono.
6Kunena zoona, ine ndine mnzanu pamaso pa Mulungu,
poti inenso adandiwumba ndi dothi.
7Musachite mantha ndi kuwopsedwa nane,
chifukwa sindikupanikizani koopsa ai.
8“Zoonadi, ndamva zimene mwalankhula,
mau anu ndaŵatsata bwino.
9Inu mukuti, ‘Ndine woyera mtima, ndilibe cholakwa.
Ndine wolungama, ndilibe tchimo.
10Mulungu wandipeza zifukwa zoti anditsutse nazo,
Iye akundiyesa mdani wake.
11 Yob. 13.27 Akumanga mapazi anga m'zigologolo,
akulonda mayendedwe anga onse.’
12“Inu aYobe simukukhoza pa zimenezi,
popeza kuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu.
13Chifukwa chiyani mukulimbana
ndi Mulungu nkumanena kuti,
‘Pa mau angaŵa sadzayankhapo ndi amodzi omwe?’
14Pajatu Mulungu amalankhula mwa njira zosiyanasiyana,
koma anthu sazindikira zimenezo.
15 Yob. 4.13 M'maloto, m'masomphenya usiku,
pamene anthu ali m'tulo tofa nato,
pamene akungosinza chabe pa bedi,
16pamenepo amaŵatsekula makutu anthuwo,
naŵaopsa ndi machenjezo.
17Mulungu amachita izi kuti
amletse munthu zoipa zimene amachita,
amafuna kuthetseratu kunyada kwake.
18Amalanditsa munthu ku manda,
amapulumutsa moyo wake kuti
ungaonongeke ndi lupanga.
19“Mwina Mulungu amalanganso
munthu ndi matenda kuti akonzeke,
nthaŵiyo thupi lake lonse limangophwanya.
20Choncho moyo wake umanyansidwa ndi chakudya chomwe,
sangadye ngakhale zakudya zabwino.
21Thupi lake limaonda, osatha kulithira m'maso,
ndipo mafupa ake amene kale sankaoneka,
amaonekera poyera.
22Munthuyo akutsikira ku manda,
ali pafupi kupita ku malo a anthu akufa.
23Koma pataoneka mngelo, ngati mthandizi,
mmodzi mwa ambirimbiri otere,
wodzamkumbutsa zimene zili zoyenera,
24ngati mngeloyo amkomera mtima, nati,
‘Mpulumutseni kuti asapite ku manda, dipo lake nali,’
25pamenepo thupi lake lisanduke lasee ngati lapaubwana,
ndipo iye abwerere ku masiku a unyamata wake,
26Tsono munthu amapemphera kwa Mulungu,
Iyeyo nkumulandira.
Amabwera pamaso pa Mulungu mokondwa,
ndipo Mulungu amamchitira zolungama.
27Apo adzavomera pamaso pa anthu kuti,
‘Ndidachimwa, sindidachite zolungama.
Koma Mulungu sadandilange koyenerana
ndi kuchimwa kwanga.
28Iye adandipulumutsa kuti ndisapite ku manda,
ndidzaonanso kuŵala kwa dzuŵa!’
29“Zoonadi, Mulungu amachita zonsezi
kaŵirikaŵiri ndi anthu.
30Amapulumutsa moyo wa munthu ku malo a imfa,
kuti athe kuwonanso kuŵala kwa moyo.
31“Inu aYobe, mutchere khutu, mundimvere ine.
Mukhale chete, kuti ine ndilankhule.
32Ngati muli ndi mau, mundiyankhe.
Mulankhule, chifukwa ndifuna kuti mupezeke wolungama.
33Ngati si choncho, mumvere ine,
khalani chete, ndipo ine
ndikuphunzitsani nzeru.”
Mulungu ndiyedi wolungama.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.