1 Sam. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yonatani athandiza Davide kuti abwerenso.

1Tsono Davide adathaŵa ku Nayoti ku Rama, nabwera kwa Yonatani. Ndipo adafunsa Yonatani kuti, “Kodi ndidachita chiyani? Ndidalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndidaŵachimwira chiyani, kuti azifuna kundipha?”

2Yonatani adamuuza kuti, “Sizingatero, suufa ai. Abambo anga sachita chilichonse, chachikulu kapena chaching'ono, osandiwuza. Tsono abambo anga angandibisire bwanji zimenezi? Si choncho ai.”

3Koma Davide adalumbira kuti, “Abambo ako akudziŵa bwino lomwe kuti umandikonda, ndipo adati, ‘Yonatani asadziŵe zimenezi kuwopa kuti angamve chisoni.’ Koma ndithu, Mulungudi, iwe Yonatani uli apa, imfa sili nane kutali.”

4Apo Yonatani adauza Davide kuti, “Chilichonse chimene unene, ndidzakuchitira.”

5 Num. 28.11 Davide adati, “Paja maŵa kuli phwando la mwezi wokhala chatsopano, ndipo sindiyenera kulephera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite kuti ndikabisale ku thengo mpaka mkucha madzulo.

6Abambo ako akandifuna, uŵauze kuti, ‘Davide adandiwumiriza kuti ndimlole kuti athamangire ku mzinda wakwao ku Betelehemu. Akuti kumeneko kuli nsembe yapachaka ya banja lonse.’

7Akati, ‘Chabwino’, zinthu zidzandiyendera bwino, ine kapolo wako. Koma akakhala wokwiyabe, udziŵe kuti watsimikiza mtima kuti andichita choipa.

8Nchifukwa chake undikomere mtima, poti udachita chipangano ndi ine kapolo wako pamaso pa Chauta. Koma ngati ndalakwa, undiphe ndiwe osati ukanditule kwa abambo ako.”

9Yonatani adati, “Ai, bwanawe, nchosatheka! Ndikadadziŵa kuti abambo anga adatsimikiza zoti akuchite choipa, kodi sindikadakuuza?”

10Apo Davide adafunsa Yonatani kuti, “Kodi ndani amene adzandiwuze, abambo ako akakuyankha mokalipa?”

11Yonatani adayankha kuti, “Tiye tikayende chakumindaku.” Choncho onse aŵiriwo adapita kumeneko.

12Kumindako Yonatani adauza Davide kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akhale mboni. Nditaŵafunsa abambo anga nthaŵi yonga yomwe ino maŵa, ngakhale mkucha, ndipo ndikapeza kuti akufuna kukuchitira chinthu chabwino, ndidzatumiza mau kuti udziŵe.

13Koma akakafunitsitsa kukuchita choipa, Chauta adzandilange kwambiri ndikapanda kukuululira ndi kukuthandiza kuti upulumuke. Chauta akhale nawe, monga momwe adakhalira ndi abambo anga.

14Ndikakhala ndili moyobe, udzandiwonetse kukoma mtima konga kwa Chauta. Koma ndikafa, usadzaleke kuchitira chifundo banja langa mpaka muyaya.

152Sam. 9.1 Pamene Chauta adzaŵatha adani onse a Davide pa dziko lapansi,

16banja la ine Yonatani lisadzafafanizike nao. Ndithu Chauta alipsire pa adani ake a Davide.”

17Apo Yonatani adalumbiritsanso Davide kuti asaleke kumkonda, pakuti Yonatani ankakonda Davide monga momwe ankadzikondera iye mwini.

18Tsono Yonatani adatinso, “Maŵa mwezi ukhala, ndipo pa phwando adzazindikira kuti iwe palibe, popeza kuti pampando pako padzakhala popanda munthu.

19Mkucha adzakufunanso kwambiri. Tsono udzapite ku malo amene udaabisala tsiku lijali, ndipo ukakhale pa mbali ina ya mulu wa miyala uli apowo.

20Ine ndidzaponya mivi itatu ku mbali ina ya muluwo, ngati ndikuchita chandamale.

21Tsono ndidzatuma mnyamata wanga kuti akatole miviyo. Mnyamatayo ndikamuuza kuti, ‘Mivi ili chakuno, kaitole!’ Pomwepo iweyo udzatuluke, chifukwa ndikulumbira, pali Chauta wamoyo, kuti kuli mtendere, iwe sudzakhala pa zoopsa.

22Koma ndikamuuza mnyamatayo kuti, ‘Mivi ili patsogolo pako,’ pomwepo iweyo uchoke, pakuti Chauta ndiye wati uchokepo.

23Tsono pa zimene tapanganazi, Chauta ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe mpaka muyaya.”

24Choncho Davide adakabisala ku minda. Ndipo pamene mwezi udaoneka, mfumu Saulo adabwera ku phwando.

25Adakhala pa mpando wake pafupi ndi khoma, monga m'mene ankachitira nthaŵi zonse. Yonatani adakhala popenyana naye, ndipo Abinere adakhala pambali pa mfumu Saulo, koma pa malo a Davide panalibe munthu.

26Koma Saulo sadanene kanthu kalikonse tsiku limenelo. Ankaganiza kuti, “Chinthu china chamgwera Davide, mwina mwake ngwosayenera zachipembedzo.”

27Koma pa tsiku lachiŵiri la phwandolo, pa malo a Davide panalibenso munthu. Ndiye Saulo adafunsa Yonatani kuti, “Chifukwa chiyani Davide mwana wa Yese sadabwere ku phwando dzulo ngakhalenso lero?”

28Yonatani adayankha kuti, “Davide adandipempha mondiwumiriza kuti ndimlole apite ku Betelehemu.

29Adati, ‘Undilole ndipite, popeza kuti banja lathu likupereka nsembe mumzindamo, ndipo mbale wanga adandikakamiza kuti ndikakhale nao kumeneko. Tsono ngati wandikomera mtima, undilole ndipite, kuti ndikaone abale anga.’ Nchifukwa chake sadabwere ku chakudya cha mfumu.”

30Apo Saulo adapsera mtima Yonatani kwambiri, ndipo adamuuza kuti, “Iwe mwana wobadwa kwa chimkazi chapakamwa, kodi ukuyesa kuti sindikudziŵa ine kuti ukugwirizana ndi mwana wa Yese, amene afuna kukuchititsa manyazi iwe ndi mai wakoyo?

31Kodi sukudziŵa kuti mwana wa Yese akakhalabe ndi moyo pa dziko lapansi, iweyo sudzakhala mfumu? Nchifukwa chake tsono, tuma anthu kuti akamtenge, abwere naye kuno, pakuti ndithudi adzafa.”

32Yonatani adafunsa bambo wake kuti, “Kodi chifukwa chiyani mufuna kumupha Davide? Kodi walakwa chiyani?”

33Atamva zimenezi Saulo adamponyera mkondo Yonataniyo kuti amuphe. Pamenepo Yonatani adadziŵa kuti bambo wake watsimikizadi mtima kuti aphe Davide.

34Tsono Yonatani adanyamuka pa tebulo atakwiya koopsa, ndipo pa tsiku lachiŵiri la phwandolo sadadye. Adaavutika kwambiri mumtima mwake, chifukwa choti bambo wake adaachita Davide chipongwe.

35M'maŵa mwake Yonatani ndi mnyamata wake adapita kuminda kuja kumene adaapangana ndi Davide.

36Adauza mnyamata wake kuti, “Thamanga, ukatole mivi imene nditi ndiponye.” Mnyamata uja akuthamanga, Yonatani adaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo.

37Ndipo mnyamatayo atafika pamalo pomwe padaagwa muviwo, Yonatani adanena chokweza kuti, “Muvi uli patsogolo pakopo.”

38Apo Yonatani adaitananso mnyamatayo nati, “Fulumira, yenda msanga, usachedwe.” Motero mnyamata uja adatola muviwo, nabwera kwa mbuyake.

39Koma mnyamatayo sadadziŵe kanthu ai, Yonatani yekha ndi Davide ndiwo amene ankadziŵa zimene zinkachitika.

40Choncho Yonatani adapereka zida zake kwa mnyamata wake uja, namuuza kuti, “Pita, kazitule ku mzinda.”

41Tsono mnyamatayo atapita, Davide adatulukira ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, ndipo adadzigwetsa pansi nagunditsa nkhope yake pansi katatu. Adampsompsonana, nayamba kulira onse aŵiriwo, koma Davide adalira koposa.

42Pamenepo Yonatani adauza Davide kuti, “Pita ndi mtendere, pakuti aŵirife tidalonjezana molumbira m'dzina la Chauta kuti, ‘Chauta ndiye adzakhale mboni pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa zidzukulu zanga ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.’ ” Pompo Davide adanyamuka nachokapo, ndipo Yonatani adabwerera kumzinda kuja.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help