2 Am. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Chaka cha 149, Yudasi ndi anthu ake adamva kuti Antioko Eupatore akubwera ku Yudeya ndi ankhondo ake ochuluka.

2Adamvanso kuti nkhoswe yake Lisiyasi amene anali nduna yake ndi mkulu wa boma, anali naye pamodzi. Anali ndi gulu lankhondo Lachigriki la oyenda pansi 110,000, okwera pa akavalo 1,300, njovu 22, ndi magaleta 300 a mikombero yokhala ndi mipeni yakuthwa.

3Menelasi adaphatikana nawo, ndipo iyeyo mwa nzeru zake zonama ndi zonyenga ankamulimbitsa mtima Antioko, osati chifukwa cholifunira zabwino dziko lake ai, koma chifukwa chokhulupirira kuti mfumu idzamkhazikitsa pa udindo wa mkulu wa ansembe.

4Koma Mulungu, Mfumu ya mafumu, adautsa mkwiyo wa Antioko pa munthu woipayo. Tsiku lina Lisiyasi adatsimikizira mfumu kuti zovuta zonsezo zidabwera chifukwa cha Menelasi. Ndiye mfumu idalamula kuti amtenge Menelasi, apite naye ku Berea kukamphera kumeneko potsata njira imene adazoloŵera komweko.

5Ndiye kuti ku Bereako kunali nsanja ya msinkhu wa mamita 22, yodzaza ndi phulusa; inali ndi chipupa chotsetsereka m'kati monsemo.

6M'menemo ndi m'mene ankakankhira munthu wonyozera mafano kapena wochita choipa china chachikulu, kuti afere momwemo.

7Menelasi adafa motero, munthu amene ankanyoza Malamulo. Panalibe wina aliyense womuika m'manda.

8Zimenezi zinali zomuyenera, popeza kuti adaachimwira guwa lansembe la Mulungu, limene moto wake ndi phulusa lake zonsezo nzopatulika. Choncho iyenso adafa pakumponya m'phulusa.

9Tsono mfumu Antioko ankabwera mumtima mutadzaza kunyada ndi nkhalwe, namafuna kuŵachita Ayuda zoipa zoposa zimene bambo wake adaaŵachita.

10Yudasi atamva zimenezi, adalamula anthu ake kuti azipemphera kwa Ambuye usana ndi usiku, poti tsopano mpamene ankasoŵa chithandizo koposa kale, chifukwa adani anali pafupi kuŵalanda Malamulo ao, dziko lao ndi Nyumba ya Mulungu.

11Azipempha Mulungu kuti asalole anthu ake amene adaangoyamba kumene kukhalanso ndi moyo kuti agwe m'manja mwa anthu olalatira Mulunguwo.

12Tsono onse pamodzi adapemphera motero ndi kupepesa Ambuye achifundo, ndi kulira misozi, ndi kusala zakudya, ndi kudzigwetsa pansi chafufumimba masiku atatu athunthu. Pambuyo pake Yudasi adaŵalimbitsa mtima, naŵalamula kuti akonzekere nkhondo.

13Atapangana paseri ndi akuluakulu, adatsimikiza zokamenyana ndi mfumuyo mokhulupirira thandizo la Mulungu, ankhondo ake a mfumu asanaloŵe ku Yudeya ndi kulanda mzinda wa Yerusalemu.

14Tsono pokhulupirira Mlengi wa dziko lapansi, adalangiza anthu ake kuti amenye nkhondo molimba mtima, ndi kuvomera kufera Malamulo, Nyumba ya Mulungu, mzinda wao, dziko lao ndi miyambo yake. Atatero adakhazika gulu lake lankhondo pafupi ndi Modini.

15Kenaka adadziŵitsa anthu ake mfuu wankhondo wakuti, “Kupambana kuchokera kwa Mulungu.” Tsono adasankha anyamata ena olimba mtima nkupita nawo usiku womwewo kukathira nkhondo zithando za mfumu, kumeneko adapha adani ngati 2,000. Anthu ake adabaya njovu yotsogolera zinzake pamodzi ndi wokwerapo wake.

16Motero m'zithando za adani mudadzaza chisokonezo ndi nkhaŵa, ndipo Yudasi ndi anthu ake adapita atapambana ndithu.

17Zimenezo zidachitika nthaŵi ya mbandakucha, ndipo zidatheka chifukwa cha chithandizo cha Ambuye.

18Mfumu Antioko ataziwonera pafupi kuti Ayuda ngolimba mtima kwabasi, adayesa kuŵagonjetsa monyenga.

19Adadzalimbana nawo ku Betizure, mzinda wina wamphamvu wa Ayuda, koma Ayuda adaŵabweza anthu ake. Adayesanso kachiŵiri, koma Ayuda adamgonjetsa.

20Tsono Yudasi adatumizira anthu amumzindamo zinthu zofunikira.

21Koma Rodoko, wa m'gulu la Ayuda, adadziŵitsa adani zinsinsi za abale ake. Choncho Yudasi adamfunafuna namgwira, nkumkonza.

22Mfumu idakambirana kachiŵiri ndi anthu a ku Betizure, ndipo atavomerezana onse, iyo idachokapo. Kenaka adadzathiranso nkhondo Yudasi ndi anthu ake, koma iwowo adaigonjetsa.

23Pambuyo pake mfumu Antioko adamva kuti Filipo, amene adaamsiyira ntchito za boma ku Antiokeya, adamgalukira, motero adavutika kwambiri. Tsono adakambirana nawo Ayuda, naŵavomereza zimene iwo adaanena, nkulumbira kuti adzaŵachitira zachilungamo. Adayanjana nawonso, nkupereka nsembe; adalemekeza Nyumba ya Mulungu, napereka mphatso zambiri.

24Adamlandira bwino Makabeo, ndipo adasankhula Hegemonide kuti akhale bwanamkubwa kuyambira ku Ptolemaisi mpaka ku Gerari.

25Pambuyo pake mfumu Antioko adapita ku Ptolemaisi, koma anthu akumeneko adamkwiyira chifukwa cha chipangano chimene adaachita ndi Ayuda, iwo nkukana kuchivomera.

26Lisiyasi adakwera pa chiwundo cha pa bwalo lamilandu, nafotokoza zifukwa zake za chipanganocho. Apo mitima ya anthuwo idakhululuka, ndipo mfumu ndi Lisiyasi adabwerera ku Antiokeya. Ndi m'mene zidaakhalira pamene mfumu Antioko adaapita kukathira nkhondo Ayuda, nkubwerako chabe.

Chipongwe cha Alikimo
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help