Esr. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Phwando kwa mfumu Ahasuwero

1 ankalamulira zigawo 127 za dziko lonse, kuyambira ku Indiya mpaka ku Etiopiya.

2Pa nthaŵi imene mfumu Ahasuweroyo anali pa mpando wa ufumu wake mu mzinda waukulu wa ku Susa,

3pa chaka chachitatu cha ufumu wake, adachitira phwando akuluakulu ake onse, antchito ake, atsogoleri ankhondo a ku Persiya ndi a ku Mediya, ndiponso akuluakulu ndi abwanamkubwa a m'zigawo, amene adaadzasonkhana kwa iye.

4Nthaŵi imeneyo mfumu inkaonetsa chuma cha ulemerero wa ufumu wake, ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake, pa masiku ambiri okwanira 180.

5Tsono masiku amenewo atatha, mfumu idachitira phwando anthu onse amene anali ku Susa, likulu la dzikolo. Idachita phwandolo ku bwalo la ku nyumba ya mfumu, kuchitira anthu apamwamba ndi otsika omwe, phwando lake la masiku asanu ndi aŵiri.

6Panali makatani oyera athonje, ndiponso nsalu zolenjeka zobiriŵira, zimene adaazimanga ndi zingwe za nsalu yabafuta ndi nsalu ina yofiirira. Zingwezo adaazikoloŵeka ndi mphete zasiliva ku nsanamira zamarabulo. Panalinso mabedi agolide ndi asiliva oikidwa pa miyala yoyala bwino yofiira, yamarabulo, yonyezimira ndi yamtengowapatali.

7Ankapatsira anthu zakumwa m'zikho zagolide, zikho zake zamitundumitundu, ndipo vinyo wa kwa mfumu anali wochuluka kwambiri malinga ndi ufulu wa mfumu.

8Potsata lamulo la mfumu, kumwa kwake kunali malinga nkukonda, panalibe munthu amene ankakakamizidwa. Pakuti mfumu idaalamula atsogoleri onse a kunyumba kwake kuti munthu aliyense azimwa monga m'mene angafunire.

9Nthaŵi yomweyo mfumukazi Vasiti nayenso adaachita lake phwando, kuchitira akazi a ku nyumba ya mfumu Ahasuwero.

10Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, pamene mfumu idaakondwa itamwa vinyo, idaitana Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, Abagita, Zetara ndi Karikasi, adindo ake ofulidwa asanu ndi aŵiri aja amene ankamutumikira,

11Idaŵalamula kuti abwere ndi Vasiti pamaso pake. Adati mfumukaziyo abwere atavala zovala zaufumu, kuti anthu ndi atsogoleri onsewo adzaone kukongola kwake, pakuti analidi wokongola zedi.

12Koma mfumukazi Vasiti adakana kubwera, mfumu italamula adindowo kuti abwere naye. Mfumu idapsa nazo mtima kwambiri zimenezi, ndipo mkwiyo wake udayaka ngati moto mumtima mwake.

13Motero mfumu idaitana anthu anzeru amene ankadziŵa malamulo, pakuti ndi m'mene mfumu inkachitira, kufunsa anthu odziŵa malamulo ndi chiweruzo.

14Anthu amene ankakhala pambali pake anali aŵa: Karisena, Setara, Adimata, Tariso, Meresi, Marisena ndi Memukana, atsogoleri asanu ndi aŵiri a ku Persiya ndi ku Mediya amene ankaloledwa kuwona nkhope ya mfumu, ndipo anali atsogoleri apamwamba mu ufumuwo.

15Mfumu idaŵafunsa kuti, “Potsata lamulo, kodi mfumukazi Vasiti timtani, poti sadachite zimene ine mfumu Ahasuwero ndidaalamula kudzera mwa adindo anga aja?”

16Apo Memukana adanena pamaso pa mfumu ndi pa atsogoleri anzake kuti, “Sikutitu mfumukazi Vasitiyu walakwira amfumu okha ai, komanso walakwira atsogoleri onse ndiponso mitundu yonse ya anthu amene ali m'maiko onse a mfumu Ahasuwero.

17Pakuti zimene wachita mfumukazizi zidzamveka pakati pa akazi onse, ndipo azidzanyoza amuna ao. Azidzanena kuti, ‘Mfumu Ahasuwero adaalamula mkazi wake Vasiti kuti abwere kwa iye, koma sadapite ai.’

18Eza. 4.6Lero lomwe lino akazi a atsogoleri onse a ku Persiya ndi a ku Mediya amene amva za makhalidwe oipa a mfumukaziŵa, adzayamba kunyoza amuna ao, ndipo kunyozana ndi kukwiyitsana kudzachuluka kwambiri.

19Chikakukomerani amfumu, mulamule kuti Vasiti asadzabwerenso pamaso panu, ndipo lamulolo lilembedwe m'buku la malamulo a Apersiya ndi Amedi, kuti lisasinthike. Ndiye pamalo pa Vasitiyo paloŵe wina wabwino koposa iyeyo.

20Tsono lamulo limene inu amfumu mupange, akalilengeza m'dziko lanu lonse lalikululi monga momwe liliri, akazi onse azidzachitira ulemu amuna ao, okwera ndi otsika omwe.”

21Mau ameneŵa adakondwetsa mfumu ndi atsogoleri, ndipo mfumuyo idachitadi zimene Memukana adaanena.

22Mfumuyo idatumiza makalata ku madera onse a mu ufumu wake, dera lililonse kalata yakeyake, ndiponso kwa mtundu uliwonse m'chilankhulo chaochao, kuti mwamuna aliyense akhale wamkulu panyumba pake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help