1 Maf. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Abwera ndi Bokosi lachipangano ku Nyumba ya Chauta(2 Mbi. 5.2—6.2)

1 2Sam. 6.12-16; 1Mbi. 15.25-29 Pambuyo pake Solomoni adasonkhanitsa akuluakulu Aisraele, ndi atsogoleri onse a mafuko, akuluakulu a mabanja a Aisraele. Onsewo adasonkhana kwa mfumu Solomoni ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta, kulitulutsa m'Ziyoni, mzinda wa Davide.

2Lev. 23.34 Ndipo Aisraele onse adasonkhana pamaso pa mfumu Solomoni nthaŵi ya chikondwerero cha mwezi wa Etanimu, mwezi wachisanu ndi chiŵiri.

3Tsono atsogoleri onse a Aisraele atabwera, ansembe adanyamula Bokosi lachipangano lija.

4Adabwera nalo Bokosi la Chautalo, pamodzi ndi chihema chamsonkhano ndiponso ziŵiya zonse zopatulika zimene zinali m'chihemamo. Ansembe ndi Alevi ndiwo amene adabwera nazo zimenezo.

5Pamenepo mfumu Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la Aisraele amene adaasonkhana pamaso pake, ataima patsogolo pa Bokosi lachipanganolo, ankapereka nsembe za nkhosa ndi ng'ombe zosaŵerengeka.

6Tsono ansembe adafika nalo ndi Bokosi lachipangano la Chauta ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana, naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.

7Choncho akerubiwo ankatambasula mapiko ao pamwamba pa Bokosilo, kotero kuti ankaliphimba pamodzi ndi mphiko zake zonyamulira.

8Mphikozo zinali zazitali kwambiri, kotero kuti nsonga zake zinkaonekera kukhalira ku malo opatulika, patsogolo pa malo opatulika kopambana a m'kati aja. Koma kukhalira kunja sizinkaonekera. Ndipo zili komweko mpaka pano.

9Deut. 10.5 M'Bokosimo munalibe kanthu kena kalikonse, kupatula miyala iŵiri yokha ija imene Mose adaaikamo ku Horebu, kumene Chauta adaachita chipangano ndi Aisraele, iwowo atatuluka ku dziko la Ejipito.

10Eks. 40.34, 35 Tsono pamene ansembewo adatulukamo m'malo opatulikawo, mtambo udadzaza Nyumba ya Chauta.

11Ndipo ansembe sankatha kutumikira chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta udaadzaza Nyumba yake ija.

12Mas. 18.11; 97.2 Tsono Solomoni adapemphera nati, “Inu Chauta mudanena kuti mudzakhala mu mdima waukulu.

13Koma tsopano ndakumangirani Inuyo nyumba yaulemerero, malo oti muzikhalamo mpaka muyaya.”

Mau a Solomoni kwa anthu ake(2 Mbi. 6.3-11)

14Tsono mfumuyo idatembenukira anthu aja, nidalitsa msonkhano wonse wa Aisraele, onsewo ali chachilili.

15Ndipo mfumuyo idati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene wachitadi ndi dzanja lake zimene adaalonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide bambo wanga.

162Sam. 7.4-11; 1Mbi. 17.3-10 Paja adaati, ‘Kuyambira tsiku limene ndidatulutsa anthu anga Aisraele ku Ejipito, sindidasankhepo mzinda pakati pa mafuko onse a Aisraele woti anthu amangeko nyumba m'mene dzina langa lizimvekamo. Koma ndidasankha Davide kuti azilamulira anthu anga Aisraele.’

172Sam. 7.1-3; 1Mbi. 17.1, 2 Tsono maganizo adaalipo mumtima mwa bambo wanga Davide oti amange nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele.

18Koma Chautayo adauza Davide bambo wanga kuti, ‘Popeza unkaganiza mumtima mwako zoti undimangire nyumba, udachita bwino kumaganiza zimenezo.

192Sam. 7.12, 13; 1Mbi. 17.11, 12 Komabe si ndiwe udzamange nyumbayo, koma mwana wako amene udzabale, ndiye amene adzandimangire nyumba yomveketsa dzina langa.’

20Tsopano Chauta wachitadi zimene adaalonjeza zija. Pakuti ine ndi amene ndaloŵa ufumu m'malo mwa Davide bambo wanga, ndipo ndikulamulira Aisraele pa mpando wa bambo wanga, monga momwe Chauta adaalonjezera. Ndipo ndinedi amene ndamanga Nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele.

21Tsono m'menemo ndalikonzera malo Bokosi lija, m'mene muli mau a chipangano cha Chauta chimene adachita ndi makolo athu, pamene adaŵatulutsa ku Ejipito.”

Pemphero la Solomoni(2 Mbi. 6.12-42)

22Pambuyo pake Solomoni adaimirira patsogolo pa guwa la Chauta, msonkhano wonse wa Aisraele ukuwona, ndipo adakweza manja ake kumwamba.

23Tsono adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, palibe Mulungu wina wonga Inu, kumwamba kapena pa dziko lapansi. Mumasunga chipangano ndi kuwonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtimi wao wonse.

24Inu mwachitadi zimene mudaauza Davide bambo wanga, mtumiki wanu. Zimene zija mudaalankhula ndi pakamwa panu, dzanja lanu lazichitadi monga onse akuwoneramu lero lino.

251Maf. 2.4 Tsono, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, mukumbukire zimene zija mudalonjeza Davide bambo wanga, mtumiki wanu, pamene mudati, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa dziko la Israele, malinga ana ako akamasamala mkhalidwe wao, ndi kumayenda pamaso panga anga monga momwe iweyo wayendera pamaso panga.’

26Nchifukwa chake tsono, Inu Mulungu wa Aisraele, zimene mudalankhula ndi bambo wanga Davide, mtumiki wanu, zichitikedi.

27 2Mbi. 2.6 “Kodi Mulungu angakhale nawodi pa dziko lapansi? Onani, kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi!

28Komabe Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani pemphero la ine mtumiki wanu ndi kupemba kwanga. Mverani kulira kwanga ndiponso pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu lero lino.

29Deut. 12.11Usana ndi usiku maso anu azikhala otsekuka kuyang'ana Nyumba imeneyi, malo amene Inu mudanena kuti, ‘Dzina langa lidzamveka m'menemo.’

30Imvani pemphero lopemba la mtumiki wanu ndiponso la anthu anu Aisraele, pamene akupemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mukhululuke.

31“Tsono munthu akachimwira mnzake, nauzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lanu m'Nyumba muno,

32pamenepo Inu mumve kumwambako, ndipo muchitepo kanthu ndi kuŵaweruza atumiki anuwo. Wochimwa mugamule kuti ngwolakwa ndipo mumlange molingana ndi zolakwa zakezo. Koma wosachimwayo mugamule kuti ngwopanda mlandu, ndipo mumpatse mphotho zoyenera makhalidwe akewo.

33“Anthu anu Aisraele atagonjetsedwa ndi adani ao chifukwa chakuti adakuchimwirani, pambuyo pake nkubwerera kwa Inu ndi kutamanda dzina lanu, napemphera ndi kupemba kwa Inu m'Nyumba muno,

34pamenepo Inuyo mumve kumwambako, ndipo mukhululukire tchimo la anthu anu Aisraele, kenaka muŵabwezenso ku dziko limene Inu mudapatsa makolo ao.

35“Kumwamba kukatsekeka, mvula nkupanda kugwa chifukwa chakuti anthuwo adakuchimwirani, pambuyo pake nkupemphera choyang'ana ku malo ano ndi kutamanda dzina lanu, natembenuka nkusiya tchimo laolo Inu mukuŵazunza,

36pamenepo Inuyo mumve kumwambako, mukhululukire tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisraele. Inu muziŵaphunzitsa njira yabwino yoti aziyendamo, ndipo muzigwetsa mvula pa dziko lanu limene mudapatsa anthu anu kuti likhale choloŵa chao.

37“Mwina mwake m'dzikomo mudzaloŵa njala, mliri, dzimbiri lapambeu kapena chinoni, dzombe kapena kapuchi. Mwina adani ao adzaŵazinga ku mzinda wao wina uliwonse. Mwina padzakhala mliri wa mtundu wina, kapena matenda a mtundu uliwonse.

38Tsono, chodandaula chake chingakhale chotani, wina aliyense mwa anthu anu Aisraele akapemphera mopemba, akuzindikira zovuta za mumtima mwake, natambalitsa manja choloza ku Nyumba ino,

39pamenepo Inuyo mumve kumwambako kumene mumakhala. Mukhululuke, ndipo muchitepo kanthu. Mumchitire aliyense potsata makhalidwe ake onse, pakuti Inu mukudziŵa mtima wake. Inu nokha ndinu amene mumadziŵa mitima ya anthu.

40Motero anthu anu Aisraele azikuwopani masiku onse a moyo wao, pomakhala m'dziko limene Inu mudapatsa makolo athu.

41“Chimodzimodzinso mwina mlendo amene sali mmodzi wa Aisraele anthu anu, adzabwera kuchokera ku dziko lakutali atamva za dzina lanu.

42Zoonadi anthu adzamva ndithu za dzina lanu lotchuka ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu. Iyeyo akabwera kudzapemphera ku Nyumba ino,

43Inu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mumchitire mlendoyo zonse zimene wakupemphani. Muchite zimenezi kuti anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi adziŵe dzina lanu ndipo azikumverani, monga m'mene amachitira Aisraele anthu anu, ndipo adziŵe kuti Nyumba imene ndaimangayi imadziŵika ndi dzina lanu.

44“Anthu anu akamapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani ao, kulikonse kumene mungaŵatume, akapemphera kwa Inu Chauta choyang'ana ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ndakumangiraniyi, yomveketsa dzina lanu,

45pamenepo Inuyo mumve kumwambako pemphero lao ndi kupemba kwao ndipo muŵapambanitse.

46“Mwina Aisraelewo adzakuchimwirani, poti palibe munthu amene sachimwa, ndiye Inuyo nkudzaŵakwiyira ndi kuŵapereka kwa adani, kuti aŵatenge ukapolo kupita nawo ku dziko lakutali kapena lakufupi.

47Tsono, ali akapolo kuchilendoko, akazindikira kuchimwa kwao natembenuka mtima ndi kupemphera kwa Inu modzichepetsa m'dziko la anthu amene adaŵagwira ukapolowo, nkumanena kuti, ‘Tachimwa, tachita zosayenera, tapalamula ndithu’.

48Anthuwo akabwerera kwa Inu ndi nzeru zao zonse ndi mtima wao wonse, m'dziko la adani ao kumene adaŵatengera ukapolo, ndipo akapemphera kwa Inu choyang'ana ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,

49pamenepo Inuyo kumwambako kumene mumakhala, mumve pemphero lao ndi kupemba kwao ndipo muŵachitire zolungama.

50Tsono muŵakhululukire anthu anu okuchimwiraniwo, mukhululukire machimo ao onse okupandukirani. Ndipo mufeŵetse mitima ya anthu amene adaŵagwira ukapolo aja, kuti nawonso aŵachitire chifundo.

51Pakutitu iwoŵa ndi anthu anuanu ndi choloŵa chanu, omwe aja mudaŵatulutsa ku Ejipito kuŵachotsa m'ng'anjo ya moto.

52“Yang'anani mwa chikondi chanu anthu anu Aisraele pamodzi ndi mfumu yao, ndipo muzitchera khutu nthaŵi zonse pamene akupemphani kuti muŵathandize.

53Pakuti Inu mudaŵasiyanitsa ndi anthu onse a pa dziko lapansi, kuti akhale anthu anuanu, monga momwe Inu mudanenera kudzera mwa Mose mtumiki wanu, pamene munkatulutsa makolo athu ku Ejipito, Inu Chauta Mulungu.”

54Tsono Solomoni atamaliza kupemphera mopemba kwa Chauta, adadzuka ku guwa la Chauta kumene anali atagwada, manja atakweza kumwamba.

55Ndipo adaimirira nadalitsa msonkhano wonse wa Aisraele mokweza mau nati,

56Deut. 12.10; Yos. 21.44, 45 “Atamandike Chauta amene adaŵapatsa mtendere anthu ake Aisraele potsata zimene adaalonjeza. Palibe mau ndi amodzi omwe amene adapita pachabe pa zinthu zonse zabwino zimene adaalonjeza, polankhula kudzera mwa Mose mtumiki wake.

57Chauta Mulungu wathu akhale nafe monga momwe adaakhalira ndi makolo athu. Asatisiye kapena kutitaya.

58Atembenuzire mitima yathu kwa Iye, kuti tiziyenda m'njira zake ndi kusunga mau ake, malamulo ake ndi malangizo ake, amene adapatsa makolo athu.

59Mau angaŵa amene ndanena mopemba pamaso pa Chauta, Mulungu wathu, asaŵaiŵale mauwo masana ndi usiku. Chauta Mulungu wathu alimbikitse mtumiki wakene ndiponso athandize Aisraele anthu ake, poŵapatsa zosoŵa zao zatsikunditsiku.

60Choncho anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi adziŵe kuti Chauta ndiye Mulungu, palibenso wina.

61Nchifukwa chake inu Aisraele, mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Mulungu wathu, ndipo mumvere bwino mau ake, ndi kutsata malamulo ake monga lero lino.”

Apereka Nyumba ya Chauta(2 Mbi. 7.4-10)

62Pambuyo pake mfumu Solomoni, pamodzi ndi Aisraele onse, adapereka nsembe kwa Chauta.

63Solomoni adapereka nsembe zachiyanjano kwa Chauta pakupha ng'ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraele onsewo adaipereka Nyumba ya Chauta ija.

64Tsiku lomwelo mfumuyo idapatulanso malo am'kati a bwalo limene linali kumaso kwa Nyumba ya Chauta. Paja kumeneko nkumene adaperekerako nsembe yopsereza, ndiponso chopereka cha chakudya, kudzanso nthuli zamafuta za nsembe zachiyanjano zija. Adaachita izi chifukwa choti guwa lamkuŵa limene linali m'malo opatulika a Chauta linali lochepa kwambiri, kotero kuti sikudatheke kuperekerapo nsembe zonse zopsereza ndi zaufa ndiponso nthuli zamafuta za nsembe zachiyanjano.

65Choncho nthaŵi imeneyo Solomoni adachita chikondwerero, pamodzi ndi Aisraele onse. Unali msonkhano waukulu kwambiri, kuyambira ku chipata cha Hamati mpaka ku kamtsinje ka Ejipito. Adachita chikondwerero chimenechi chopembedza Chauta Mulungu wathu, masiku asanu ndi aŵiri.

66Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu, Solomoni adauza anthuwo kuti azipita. Pompo anthuwo adathokoza mfumuyo, ndipo adapita kwao ndi mtima wokondwa ndi wosangalala, chifukwa cha zokoma zonse zimene Chauta adaachitira Davide mtumiki wake, ndi anthu ake Aisraele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help