Deut. 31 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yoswa asankhidwa kuti aloŵe m'malo mwa Mose

1Mose adapitirira kulankhula ndi Aisraele aja kuti:

2Num. 20.12 Tsopano ndili ndi zaka 120, ndipo sindingathenso kukhala mtsogoleri wanu. China nchakuti Chauta adandiwuza kuti Yordaniyu sindimuwoloka.

3Mwini wake Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakuperekezeni ndi kuwononga mitundu ina yonseyi, kuti inu mukhale m'dziko mwao. Yoswa adzakhala mtsogoleri wanu, monga momwe Chauta wanenera.

4Num. 21.21-35 Chauta adzaŵaononga anthu ameneŵa monga momwe adaonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, pamodzi ndi dziko lao.

5Chauta adzakupambanitsani, ndipo adaniwo muzikaŵachita zomwe ndakulamulanizi.

6Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.

7Pomwepo Mose adaitana Yoswa pamaso pa Aisraele onse ndipo adamuuza kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Ndi iweyo amene udzatsogolere anthu aŵa ku dziko limene Chauta adalonjeza makolo ao. Ndiwe amene udzakhazikitsa anthu m'dzikomo.

8Yos. 1.5; Ahe. 13.5 Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”

Za kuŵerenga lamulo zaka zisanu ndi ziŵiri zilizonse

9Pamenepo Mose adalemba malamulo a Mulungu ndi kuŵapatsa ansembe, ana a Levi, amene ankanyamula Bokosi lachipangano la Chauta. Adaŵapatsanso atsogoleri a Aisraele.

10Deut. 15.1, 2; Deut. 16.13-15 Adaŵalamula onsewo kuti, “Kamodzi pa zaka zisanu ndi ziŵiri zilizonse, pamene chaka cha kumasulidwa chafika, muŵerenge malamuloŵa pa chikondwerero cha misasa.

11Muŵaŵerenge kwa Aisraele onse, pamene adzabwere kudzapembedza Chauta pa malo oŵasankha Iyeyo.

12Mudzaitane amuna onse, akazi, ana ndi alendo amene ali m'mizinda mwanu, kuti aliyense adzimvere yekha, ndipo aphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamvera mau ake mosamala.

13Mwa njira imeneyi zidzukulu zanu zimene sizidamve malamulo a Chauta nkale lomwe, zidzamva, ndipo zidzaphunzira kuwopa Chauta nthaŵi yonse imene zidzakhale m'dziko limene mukukakhalamolo patsidya pa Yordani.”

Chauta alangiza Mose kotsiriza

14Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Nthaŵi ya moyo wako yatsala yochepa. Itana Yoswa, ubwere naye ku chihema chamsonkhano kuti ndimulangize.” Mose pamodzi ndi Yoswa adapita ku chihema chamsonkhano,

15ndipo Chauta adaŵaonekera iwowo mu mtambo wonga chipilala umene udaaima pakhomo pa chihemacho.

16Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Patsala pang'ono kuti iwe umwalire. Ndiye iwe ukapita, anthuŵa adzaphwanya chipangano chomwe ndidachita nawo. Adzandisiya Ine, nkumapembedza milungu ya dziko limene akukakhalamolo.

17Zikadzangotero, ndidzaŵakwiyira ndi kuŵasiya, ndipo adzatheratu. Masoka ndi zoipa zina zambiri zidzaŵagwera. Tsono masiku amenewo azidzanena kuti, ‘Kodi zoipazi sizikutigwera chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wathu, sali nafenso?’

18Ndithudi pa nthaŵi imeneyo ndidzaŵafulatira chifukwa cha machimo onse amene iwo adachita popembedza milungu ina.

19“Tsopano talemba nyimbo iyi. Uŵaphunzitse ndi kuŵalimbitsa Aisraele kuti idzakhale mboni yanga yoŵatsutsa.

20Ndidzaŵaloŵetsa m'dziko lamwanaalirenji, monga momwe ndidalonjezera makolo ao. Kumeneko adzapeza chakudya chonse chomwe angachifune, ndipo adzakhala mosangalala. Komabe adzatembenukira ku milungu ina ndi kumaipembedza. Adzandikana Ine, ndipo adzaphwanya chipangano changa.

21Choncho masoka oopsa adzaŵagwera. Nyimbo imeneyi idzakhala mboni yanga yoŵatsutsa, chifukwa zidzukulu zao zizidzaiimba. Ngakhale tsopano lino ndisanaŵaloŵetse m'dziko limene ndidalumbira kuti ndidzaŵapatsa, ndikudziŵa zimene iwo akulingalira.”

22Tsiku lomwelo Mose adalemba nyimbo naphunzitsa Aisraele.

23 Num. 27.23; Yos. 1.6 Tsono Chauta adauza Yoswa, mwana wa Nuni, kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Udzaŵatsogolera Aisraele kukaloŵa m'dziko lomwe ndidaŵalonjeza. Ndipo ndidzakhala nawe.”

24Tsono Mose adalemba malamulo a Mulungu m'buku, osasiya kanthu.

25Atamaliza, adauza Alevi amene ankanyamula Bokosi lachipangano kuti,

26“Tengani buku ili la malamulo a Mulungu, ndipo muliike pambali pa Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu, kuti likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani.

27Ndikudziŵa kukanika kwanu ndiponso uchigaŵenga wanu. Ngati mugalukira Chauta, ndikadali moyo, nanji ndikadzafa, ndiye mudzaposa kugaluka kwake.

28Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko pamodzi ndi akuluakulu omwe, kuti ndiŵauze zimenezi. Kumwamba ndi dziko lapansi ndizo zidzakhale mboni zoŵatsutsa.

29Ndikudziŵa kuti ine ndikadzafa, nonse mudzaipa ndipo mudzakana zimene ndakuuzanizi. Koma pambuyo pake kutsogoloko, mudzakomana ndi masoka, chifukwa chochita zoipa pamaso pa Chauta ndi kuputa mkwiyo wake pakuchulukitsa machimo anu. Mwakwiyitsa Chauta pochita zimene Iyeyo amakana.”

30Tsono Mose adanena mau a nyimbo yonseyi, kuyambira poyamba mpaka potsiriza, Aisraele onse alikumva:

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help