Yud. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yuditi atsogolera nyimbo yotamanda

1Yuditi adaimba nyimbo iyi yotamanda ndi yothokoza, imene Aisraele adaimba nawo mokondwa kuti,

2“Muimbireni Mulungu wanga nyimbo ndi ting'oma,

aimbireni Ambuye anga ndi ziwaya zamalipenga.

Muimbireni nyimbo yotamanda,

mutamande dzina lake ndi kumalitchula mopemba.

3“Mulungu ndiye Ambuye othetsa nkhondo zonse.

Wandipulumutsa kwa adani anga,

wandibwezera m'zithando zake pakati pa anthu ake.

4Aasiriya adachokera ku mapiri akumpoto,

ankhondo ao adabwera mu unyinji wao,

kotero kuti magulu ao ankhondo

adachita kuti fwa m'zigwa,

ndipo ankhondo ao a pa akavalo adaphimba mapiri onse.

5Adayamba kuwopseza kuti adzatentha dziko langa,

adzapha anyamata anga ndi lupanga

ndi kukankhanthitsa pansi ana anga akhanda,

nkudzagwira ana anga ndi anamwali anga.

6“Koma Ambuye amphamvuzonse athetsa zolinga zao

ndi dzanja la munthu wamkazi.

7Ngwazi yao sidaphedwe ndi anyamata

kapena ndi anthu a nyonga zoopsa.

Sidaphedwe ndi ziphona zakale,

koma Yuditi, mwana wa Merari,

ndiye adaigwetsa pansi nkukongola kwake.

8Adavula zaumasiye

kuti apulumutse ozunzika a ku Israele.

Adadzola mafuta onunkhira kumaso kwake,

namanga tsitsi lake ndi nduŵira,

nkuvala nsalu yabafuta kuti amtenge mtima.

9Nsapato zake zidamkoka maso,

kukongola kwake kudamutenga mtima,

lupanga nkumdula pakhosi.

10“Apersiya adachita mantha kwambiri poona

kulimba mtima kwake.

Amedi adadabwa poona kusaopa kwake.

11Tsono anthu anga ozunzidwa adafuula mokondwa.

Anthu anga ofooka adafuula,

pamene mdani adanjenjemera.

Anthu angawo adakweza mau,

adani nkuthaŵa.

12Adaŵabaya ngati ana a adzakazi,

adaŵapweteka ngati ana a anthu othaŵa ku nkhondo.

Adaonongedwa ndi gulu lankhondo la Ambuye anga.

13 Mas. 144.9 “Ndimuimbira nyimbo iyi yatsopano

Mulungu wanga:

Inu Ambuye, ndinu aakulu ndi olemekezeka.

Mphamvu zanu nzodabwitsa ndi zosagonjetseka.

14Dziko lonse lapansi likutumikireni,

chifukwa Inu mudalankhula,

ndipo zonse zidalengedwa.

Mudatumiza mzimu wanu ndipo udalenga zonse,

Palibe ndi mmodzi yemwe

amene angathe kukana lamulo lanu.

15“Mapiri ndi nyanja zimagwedezeka,

matanthwe amasungunuka ngati sera pamaso panu,

koma amene amakuwopani,

mumaŵachitira chifundo.

16 1Sam. 15.22; Mas. 51.16, 17; Hos. 6.6 “Palibe nsembe yotha kukukondweretsani

ndi fungo lake.

Mafuta onse a nsembe zopsereza

si kanthu pamaso panu.

Koma amene amaopa Ambuye,

ameneyo ndiye wamkulu nthaŵi zonse.

17“Tsoka kwa mitundu yonse ya anthu

olimbana ndi anthu anga.

Ambuye amphamvuzonse adzaŵalanga

pa tsiku la chiweruzo.

Mitembo yao idzatenthedwa ndi moto,

idzadyedwa ndi mphutsi.

Adzalira ndi zoŵaŵa mpaka muyaya.”

Kuthokoza kwa Yuditi

18Yuditi ndi anthuwo atafika ku Yerusalemu, adapembedza Mulungu. Atadziyeretsa potsata mwambo, adapereka nsembe zao zopsereza ndi zaufulu ndiponso mphatso zao.

19Yuditi adapereka kwa Mulungu chuma chonse cha Holofernesi chimene anthu adampatsa. Ndipo nsalu zochingira zimene adatenga kubedi kwa Holofernesi, adazipereka kuti zikhale nsembe yotamandira.

20Tsono anthu adakondwera ku Yerusalemu pa khomo la Nyumba ya Mulungu miyezi itatu, ndipo Yuditi anali nawo.

21Zimenezi zitatha, onse adabwerera kwao. Yuditi adabwerera ku Betuliya nakakhala pa dziko lake. Pa nthaŵi ya moyo wake anali wotchuka m'dziko lonse.

22Panali amuna ambiri ofuna kumukwatira, koma sadakwatiwenso moyo wake wonse, kuchokera pamene mwamuna wake Manase adzafa naikidwa pafupi ndi makolo ake.

23Mbiri ya Yuditi idanka nikulirakulira, ndipo adakalambira m'nyumba ya mwamuna wake, mpaka adafika zaka 105 za moyo wake. Adapatsa mdzakazi wake ufulu. Ndipo adafera ku Betuliya, naikidwa m'manda a mwamuna wake Manase.

24Aisraele adalira maliro ake masiku asanu ndi aŵiri. Yuditi asanafe adaagaŵira chuma chake abale a mwamuna wake Manase ndi abale a iye mwini.

25Palibe ndi mmodzi yemwe amene adaopsezanso Aisraele, Yuditi akali moyo. Ngakhale atafa, padapita nthaŵi yaitalinso kuli mtendere wokhawokha.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help