1Patapita nthaŵi pang'ono, mfumu idatuma mkulu wina wa ku Atene kuti akaumirize Ayuda kusiya malamulo a makolo ao, ndipo kaŵaletse kutsata ndi Malamulo a Mulungu omwe.
2Adamlamulanso kuti aipitse Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, pakuitchula nyumba yachipembedzo ya Zeusi wa ku Olimpiya, ndipo kaipitsenso Nyumba ya Mulungu ya ku Gerizimu pakuitchula nyumba yachipembedzo ya Zeusi, Bwenzi la Mlendo, monga momwe ankafunira anthu akumeneko.
3Pamenepo zinthu zidaaipadi.
4Akunja adadzazamo zadama ndi zonyansa m'Nyumba ya Mulungumo. Ankaseŵera ndi akazi adama momwemo, nkumachimwa nawo m'mabwalo a malo oyera. Adaloŵetsamo zinthu zinanso zoletsedwa.
5Paguwanso padadzaza nsembe zosayenera, zimene Malamulo ankaletsa.
6Ayuda sankaloledwanso kusunga masiku a Sabata ndi achikondwerero a makolo ao. Ngakhale kudzitchula kuti, “Ndife Ayuda,” ankaŵaletsanso.
7Mwezi uliwonse, pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa mfumu, ankaumiriza Ayuda kudya nawo nsembe zachikunja. Ndipo pa tsiku la chikondwerero cha Dionizioyo, ankaŵaumiriza kuyenda pa mdipiti wolemekeza Dionizio, kumutuku atavala nsangamutu zamasamba.
8Potsata malangizo a Ptolemeyo, mfumu idalamula mizinda Yachigriki imene inali pafupi, kuti m'menemonso akakamize Ayuda kutsata miyambo Yachigrikiyo ndi kudya nawo zansembe zao.
9Adalamulanso kuti aphe onse okana kutsata miyambo Yachigrikiyo. Chinali chapafupi kuzindikira kuti zoopsa zazikulu zili pafupi.
10 1Am. 1.60, 61 Mwa chitsanzo: Akazi aŵiri adaŵagwira chifukwa cha kuumbalitsa ana ao. Adaŵayendetsa mumzinda monse, ana aowo ataŵamangirira ku maŵere ao. Kenaka adapita nawo pa linga la mzinda, nkuŵaponya pansi.
111Am. 2.32-38Nthaŵi inanso anthu ena adaasonkhana pamodzi m'mapanga pafupi, kuti asunge tsiku la Sabata mwachinsinsi. Ena adakaŵaneneza kwa Filipo. Onsewo adaŵatenthera pamodzi ali moyo. Chifukwa chofuna kulemekeza tsiku la Sabata, sadachite nkhondo kuti adziteteze.
Ambuye amalanga, amachitanso chifundo12Ndikupempha onse amene adzaŵerenge bukuli kuti asataye mtima pakumva zovutazo, koma alingalire kuti chilangocho chidatigwera, osati kuti chitiwononge, koma kuti chikonze mtundu wathu.
13Nchizindikiro cha chifundo chachikulu kumulanga msanga munthu wochimwa, osamlekerera nthaŵi yaitali.
14Ambuye akafuna kulanga anthu a mitundu ina, amayamba adikira mpaka zoipa zao zitafika poti zadzaza. Koma ifeyo satichita zimenezo ai.
15Zimatero chifukwa safuna kudikira kuti adzalipsire, zoipa zathu zikadzaza.
16Nchifukwa chake saleka kutimvera chisoni. Ngakhale atilange ndi zosautsa, satisiya konse.
17Zimene ndanenazi zikhale ngati chikumbutso. Tsopano ndikupitirira kukamba nkhani yathu.
Kuphedwa kwa Eleazara18 Lev. 11.7, 8; Ahe. 11.35 Eleazara anali mmodzi mwa aphunzitsi a Malamulo, munthu wokalamba zedi, munthu wotchuka kwambiri. Adamkanula kukamwa kuti amdyetse nyama yankhumba.
19Koma iye adasankhula kufa mwaulemu, osati kukhala ndi moyo wamanyazi. Motero adailavula nyamayo, napita yekha ku malo ozunzira anthu.
20Adaonetsa m'mene anthu olimba mtima ayenera kuchitira: kukana kudya zosaloledwa kupambana kupulumutsa moyo wao.
21Akapitao oyang'anira zakudya za nsembe yonyansayo amene kale ankayanjana ndi Eleazara, adamtengera paseri namuuza kuti abwere nayo nyama yake yololedwa, ndipo pakudya imeneyo achite ngati akudya nyama yosaloledwa ija, monga momwe mfumu idaalamulira.
22Adamuuza zimenezo kuti pakutero asaphedwe, koma apulumuke chifukwa cha chibwenzi chao chakale.
23Koma iye adatsimikiza kutsata njira yaulemu, poona kuti anali munthu wa zaka zambiri ndi wa ukalamba wolemekezeka ndi wa imvi zake, wa ntchito zokoma zokhazokha kuyambira pa ubwana wake, ndi wosunga Malamulo oyera a Mulungu. Tsono adayankha msanga kuti, “Iyai, mundiphe basi.”
24Ndipo adaonjeza kuti, “Ife anthu a zaka zochuluka sitingathe kunyenga ena. Nkosayenera kuti anyamata ambiri aziganiza kuti Eleazara munthu wa zaka 90, adapatuka ndi kutsata chipembedzo chachilendo.
25Chifukwa cha kunyenga kwanga, kuti nditalikitseko kamoyo kanditsaliraka, ndidzachititsa manyazi ukalamba wanga, ndipo achinyamata ambiri ndidzaŵasokeza.
26Inetu ngakhale ndipulumuke tsopano ku mazunzo a anthu, sindingalewe manja a Wamphamvuzonse, ngakhale ndikhale ndi moyo kapena ndife.
27Nchifukwa chake, ngati tsopano ndisiyana nawo moyo uno ndi mtima wolimba, ndidzakhala nkhalamba yaulemu.
28Ndipo ndidzasiyira achinyamata chitsanzo cha imfa yaulemu, yoifuna ndi yoivomera ndekha, chifukwa cha Malamulo athu oyera ndi olemekezeka.”
Atanena mau ameneŵa, adapita yekha ku malo ozunzira anthu.
29Anthu amene adaamchitira chifundo poyamba paja, adasanduka adani ake, chifukwa iwowo adaaganiza kuti mau akewo anali opusa.
30Ali pafupi kufa ndi mazunzowo, iye adadzuma nati, “Ambuye a nzeru zoyera aona poyera pano kuti ine, ngakhale ndidakatha kupulumuka ku imfa, ndikupirirabe zoŵaŵa m'thupi mwanga pondimenya ndi zikoti, ndipo ndikuzipirira ndi chimwemwe mumtima mwanga, chifukwa cha kuwopa Ambuyewo.”
31Munthuyo adafa motero, ndipo pakufapo adapereka chitsanzo, osati kwa achinyamata okha, komanso kwa anthu onse a mtundu wake. Adaŵapatsa chitsanzo cha kulimba mtima ndi cha makhalidwe abwino.
Kuphedwa kwa anyamata asanu ndi aŵiri a mimba imodziWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.