1Imvani izi, inu anthu a mitundu yonse.
Tcherani khutu, inu nonse okhala pa dziko lapansi,
2anthu otsika ndi okwera omwe,
olemera ndi osauka omwe.
3Zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zakuya,
ndipo ndidzalankhula zanzeru.
4Ndidzakupherani mwambi,
ndidzamasulira tanthauzo lake poimba pangwe.
5Ndichitirenji mantha pa nthaŵi yamavuto
pamene anthu ondizunza akundizinga.
6Anthu otero amangokhulupirira chuma chao,
amanyada chifukwa ali ndi chuma chambiri.
7Zoonadi, palibe munthu amene angadziwombole,
kapena kupatsa Mulungu mtengo wa moyo wake.
8Popeza kuti choombolera moyo wa munthu
ndi chamtengowapatali,
ndipo sangathe kuchikwanitsa,
9kuti azikhalabe ndi moyo mpaka muyaya
osapita ku manda.
10 Mphu. 11.19 Zoonadi, aliyense atha kuwona
kuti ngakhale anthu anzeru amafa.
Chimodzimodzi, anthu opusa ndi opulukira ayenera kufa
ndi kusiyira ena chuma chao.
11Manda ao ndiye kwao mpaka muyaya,
ndi malo odzakhalako pa mibadwo yonse,
ngakhale akadali moyo ankatcha maiko maina ao.
12Ngakhale munthu akhale wolemera chotani,
komabe adzafa chabe ngati nyama zakuthengo.
13Zimenezi ndizo zimene zimaŵagwera
anthu amene ali ndi chikhulupiriro chopusa,
ndiwo mathero ake a onse
amene amatsata maganizo otere.
14Ayenera kupita ku dziko la akufa ngati nkhosa,
ndipo imfa idzakhala mbusa wao.
Anthu olungama adzaŵapambana.
Adzatsika kulunjika ku manda,
matupi ao adzaola,
kwao kudzakhala kumanda.
15Koma Mulungu adzaombola moyo wanga
ku ulamuliro wa manda,
sindidzaopa, pakuti Iye adzandilandira.
16Usavutike munthu wina akamalemera,
pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira.
17Chifukwa pamene munthuyu amwalira,
sadzatengapo kanthu.
Chuma chake sichidzapita naye limodzi.
18Ngakhale pamene munthuyo ali moyo,
amadziyesa wodala,
ndipo ngakhale atamandidwe
pamene zinthu zikumuyendera bwino,
19adzafabe nkukakumana ndi makolo ake onse kumanda,
kumene sadzaona kuŵala mpaka muyaya.
20Ngakhale munthu akhale wolemera chotani,
komabe akasoŵa nzeru,
adzafa chabe ngati nyama zakuthengo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.