Miy. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mkazi wanzeru amamanga banja lake,

koma wopusa amalipasula ndi zochita zake zomwe.

2Woyenda molungama amaopa Chauta,

koma woyenda mokhotakhota amanyoza Chauta.

3Kulankhula kwa chitsiru kumamuitanira ndodo pa msana,

koma mau a munthu wanzeru amamteteza.

4Kopanda ng'ombe, kumakhalanso kopanda dzinthu,

koma kwa ng'ombe zamphamvu, dzinthu dzimachuluka.

5Mboni yokhulupirika siinama,

koma mboni yonyenga imalankhula zabodza.

6Wonyoza anzake amafunafuna nzeru osaipeza,

koma munthu womvetsa amadziŵa bwino zinthu msanga.

7Usayandikirepo pamene pali chitsiru,

paja pamenepo supezapo mau anzeru.

8Nzeru za munthu wochenjera

zagona pa kuzindikira bwino njira zake,

koma zitsiru zimanyengedwa nkupusa kwao komwe.

9Zitsiru sizilabadako za kulapa machimo ao,

kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.

10Mtima umadziŵa wokha zoŵaŵa zake,

ndipo palibe wina angadziŵe kukondwa kwake.

11Nyumba ya munthu woipa idzapasuka,

koma hema la munthu wolungama lidzakhazikika.

12 Miy. 16.25 Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu,

koma kopherezera kwake nku imfa.

13Ngakhale poseka, mtima nkumvabe chisoni,

ndipo mathero a chimwemwe ndi chisoni.

14Munthu wosalungama

adzalandira zoyenerera ntchito zake,

koma munthu wabwino

adzalandira mphotho ya ntchito zake.

15Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse,

koma wochenjera amayang'ana m'mene akuyendera.

16Munthu wanzeru ngwochenjera, ndipo amalewa choipa,

koma chitsiru chimadudukira zinthu mosasamalako.

17Munthu wopsa mtima msanga amachita zauchitsiru,

wa khalidwe lonyenga, anthu amadana naye.

18Anthu opusa wao ndi uchitsiru,

koma ochenjera yao ndi mphotho ya kudziŵa zinthu.

19Anthu ochimwa adzaŵeramira anthu abwino,

anthu oipawo adzapempha thandizo kwa abwinowo.

20Mmphaŵi ngakhale anzake omwe samukonda,

koma wolemera amakhala ndi abwenzi ambiri.

21Amene amanyoza mnzake ngwochimwa,

koma ngwodala amene amachitira chifundo amphaŵi.

22Kodi amene amakonzekera zoipa sachimwa?

Koma amene amakonzekera zabwino

anthu amaŵaonetsa chifundo ndi kukhulupirika.

23Pa ntchito iliyonse pali phindu lake,

koma kumangolakatika kumabweretsa umphaŵi.

24Mphotho ya anthu anzeru ndi nzeru zao zomwe,

koma anthu opusa malipiro ao ndi uchitsiru wao.

25Mboni yokhulupirika imapulumutsa anthu,

koma mboni yonama imaphetsa.

26Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba,

ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.

27Kuwopa Chauta ndiye kasupe wa moyo,

kumapewetsa misampha ya imfa.

28Chinamtindi cha anthu ndiye ulemerero wake wa mfumu,

koma anthu akasoŵa, ufumu wake umasanduka wachabechabe.

29Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri,

koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.

30Mtima wodekha umapatsa thupi moyo,

koma nsanje imaoletsa mafupa.

31Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake,

koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.

32Anthu ochita zoipa amatayika,

koma ochita zabwino amatetezedwa.

33Nzeru zimakhala mumtima mwa anthu omvetsa zinthu,

koma mumtima mwa zitsiru sizipezeka.

34Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,

koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.

35Mfumu imakondwa ndi mtumiki wochita zinthu mwanzeru,

koma imakwiyira wochita zinthu mochititsa manyazi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help