1 Mbi. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide adzozedwa kuti akhale mfumu(2 Sam. 5.1-10)

1Aisraele onse adadzasonkhana kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi.

2Kale, ngakhale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo, nkumabwera nawonso. Ndipo Chauta, Mulungu wanu, adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya anthu anga Aisraele.’ ”

3Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse, potsata mau a Chauta ochokera m'kamwa mwa Samuele.

4 Yos. 15.63; Owe. 1.21 Pambuyo pake Davide pamodzi ndi Aisraele onse adapita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, ndiye kuti Yebusi, kumene kunkakhala Ayebusi nzika za dzikolo.

5Ayebusiwo adauza Davide kuti, “Kuno sudzaloŵako ai.” Komabe Davideyo adalanda linga la Ziyoni, ndiye kuti Mzinda wa Davide.

6Davide anali atanena kuti, “Aliyense amene ayambe kukantha Ayebusi, adzakhala mkulu wolamulira gulu lankhondo.” Tsono Yowabu mwana wa Zeruya ndiye adayamba kupitako, motero adakhala mtsogoleri wankhondo woyamba.

7Popeza kuti Davide ankakhala m'lingamo, lingalo linkatchedwa Mzinda wa Davide.

8Ndipo adamanga mzinda kuzungulira deralo kuyambira ku linga la Milo mpaka m'kati mwake. Yowabu ndiye adakonza mbali ina ya mzindawo.

9Motero mphamvu za Davide zidanka zikulirakulira, chifukwa Chauta wamphamvuzonse anali naye.

Asilikali omveka a Davide(2 Sam. 23.8-39)

10Tsono aŵa ndiwo atsogoleri a nkhondo a Davide, amene ankamthandiza pamodzi ndi Aisraele onse, kuti akhale mfumu potsata mau a Chauta onena za Israele.

11Mndandanda wa anthu amphamvu a Davide ndi uwu: Yasobeamu Muhakimoni ndiye amene anali wamkulu mwa atsogoleri a anthu aja. Tsiku lina adapha ndi mkondo wake anthu 300 nthaŵi imodzi.

12Mnzake wotsatana naye mwa anthu atatu amphamvu aja anali Eleazara, mwana wa Dodo, Mwahohi.

13Iyeyo anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu pamene Afilisti adaasonkhana kumeneko kuti amenyane naye nkhondo. Kumeneko kudaali munda wodzaza ndi barele ndipo anthu a Davide adathaŵa kuwopa Afilistiwo.

14Koma Eleazara ndi anzake adakaima m'kati mwa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo. Motero Chauta adaŵapulumutsa ndi kuŵapambanitsa kwambiri.

15Tsiku lina atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja adatsikira ku thanthwe mpaka kwa Davide ku phanga la Adulamu. Kufupi nkumeneko ankhondo a Afilisti anali atamanga zithando zankhondo ku chigwa cha Refaimu.

16Pamenepo nkuti Davide ali m'phanga muja, ndipo kagulu kankhondo ka Afilisti kanali ku Betelehemu.

17Ndiye Davide atamva ludzu kwambiri adati, “Ha, wina akadandipatsa madzi a m'chitsime chimene chili pafupi ndi chipata ku Betelehemu kuti ndimwe!”

18Pomwepo anthu atatu amphamvu aja adapita akubzola zithando za Afilisti, nakatunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo, adangoŵathira pansi kuŵapereka kwa Chauta.

19Ndipo adati, “Ndithu, pali Mulungu, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao pa minga, pang'ono akadataya moyo wao pokabwera nawo madzi ameneŵa.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja.

20Abisai, mbale wake wa Yowabu, anali mkulu wa atsogoleri makumi atatu aja. Ndiye adapha ndi mkondo wake anthu 300, nakhala wotchuka ngati anthu atatu aja.

21Iye anali womveka kwambiri mwa atsogoleri makumi atatu aja, ndipo adasanduka mkulu wao, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja.

22Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima, amene ankachita ntchito zazikulu. Iyeyo adapha ngwazi ziŵiri za ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa adatsikira m'chitsime, naphamo mkango.

23Adaphanso Mwejipito wina wamkulu thupi, kutalika kwake ngati mamita aŵiri ndi theka. Mwejipitoyo anali ndi mkondo m'manja wofanafana ndi mtanda wa munthu woomba nsalu. Koma Benaya adapita kwa iyeyo atatenga ndodo, nalanda mkondowo kumanja kwa Mwejipito uja, nkumupha ndi mkondo wake womwewo.

24Zimenezi ndizo adachita Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo adatchuka ngati atsogoleri makumi atatu amphamvu aja.

25Iyeyu anali womveka mwa atsogoleri makumi atatuwo, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Davide adamuika kuti azilamulira asilikali ake omuteteza.

26Anthu amphamvu a m'magulu ankhondowo anali aŵa: Asahele mbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

27Samoti wa ku Harodi, Helezi Mpeloni,

28Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiyezere wa ku Anatoti,

29Sibekai Muhusati, Ilai Mwahohi,

30Maharai wa ku Netofa, Heledi mwana wa Baana wa ku Netofa,

31Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea, Mbenjamini. Panalinso Benaya wa ku Piratoni,

32Hurai wa ku mitsinje ya ku Gaasi, Abiyele Mwarabati,

33Azimaveti wa ku Baharumi, Eliyaba wa ku Saaliboni,

34Hasemu Mgizoni, Yonatani mwana wa Sage Muharari,

35Ahiyamu mwana wa Sakara Muharari, Elifala mwana wa Uri,

36Hefere Mmekerati, Ahiya Mpeloni,

37Heziro wa ku Karimele, Naarai mwana wa Ezibai,

38Yowele mbale wake wa Natani, Mibara mwana wa Hagiri,

39Zeloki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,

40Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,

41Uriya Muhiti, Zabadi mwana wa Alai,

42Adina mwana wa Siza Mrubeni, mtsogoleri wa Arubeni, ndi anthu makumi atatu pamodzi naye,

43Hanani mwana wa Maaka, ndiponso Yosafati Mmitini,

44Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyele ana a Hotamu Mweroeri,

45Yediyaele mwana wa Simiri, ndi Yoha mbale wake Mtizi,

46Eliyele Mmahavi, ndiponso Yeribai ndi Yosaviya, ana a Elinamu, kudzanso Itima Mmowabu,

47Eliyele, Obede ndi Yaasiyele Mmezobai.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help