Ezek. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ezekiele atsutsa za mafano

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, uyang'ane ku mapiri a ku Israele, ndipo uŵadzudzule ndi mau aŵa akuti,

3Inu mapiri a ku Israele, imvani mau a Ambuye Chauta. Akuuza mapiri ndi magomo, mitsinje ndi zigwa kuti, ‘Ine weniweniyo ndidzakuthirani nkhondo, ndipo ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano.

4Maguwa anu ansembe adzaonongedwa, ndipo maguwa anu ofukizirapo lubani adzaphwanyidwa. Anthu anu odzapembedza pamenepo ndidzaŵaphera pafupi ndi mafano anu.

5Tsono mitembo ya Aisraele ndidzaimwaza patsogolo pa mafano ao. Ndidzamwaza mafupa anu pozungulira maguwa anu onse.

6Konse kumene mukakhale, mizinda yanu idzasanduka mabwinja. Akachisi onse adzaonongedwa, kotero kuti maguwa anu onse pamodzi ndi mafano anu omwe adzaphwanyidwa. Maguwa anu ofukizirapo lubani adzagwetsedwa, ndipo zonse zimene mudapanga zidzatheratu.

7Anthu anu adzaphedwa pakati panu, motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ ”

8“Komabe ena mwa inu ndidzaŵasiya amoyo. Adzapulumuka ku nkhondo, ndipo ndidzaŵamwazira ku maiko ena, pakati pa anthu a mitundu ina.

9Tsono opulumuka mwa inu adzandikumbuka pakati pa anthu a mitundu inayo, kumene adatengedwa ukapolo. Ndidzaŵamvetsa chisoni ndi manyazi chifukwa cha kusakhulupirika kuja ndi kundipandukira kuja, ndiponso chifukwa cha kuika mtima kwao pa mafano. Tsono adzachita nyansi ndi iwo eniakewo poona zoipa zonse zimene adachita, pamodzi ndi zochita zao zonyansa.

10Pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndipo sindinkaŵaopseza chabe pamene ndinkanena kuti ndidzaŵalanga.”

11“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Omba m'manja mwako, ndipo uponde phazi lako pansi kwamphamvu. Tsono unene kuti, ‘Tsokalo!’ chifukwa cha zonyansa zonse zimene banja la Israele lachita. Adzafa ndi nkhondo, njala ndi mliri.

12Amene ali kutali adzafa ndi mliri. Amene ali pafupi adzafa ndi nkhondo. Aliyense wotsala adzafa ndi njala. Ndimo m'mene mkwiyo wanga udzagwere pa iwo.

13Apo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene mudzaona ophedwa ao ali vuu pakati pa mafano, kuzungulira maguwa ao, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndi wa thundu uliwonse wa masamba ambiri, ku malo onse kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano ao onse.

14Motero ndidzaŵakantha ndi mkono wanga, ndipo dziko lao lonse ndidzalisandutsa chipululu ku malo ao onse kumene akukhala. Ndidzalisandutsa bwinja kuchokera ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula. Pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help