1 2Maf. 24.17; 2Mbi. 36.10 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adakhazika Zedekiya pa mpando waufumu wa ku Yuda, kuloŵa m'malo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu.
2Koma Zedekiyayo ndi aphungu ake, pamodzi ndi anthu onse a m'dzikomo, sadamvere mau amene Chauta adalankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya.
3Tsono mfumu Zedekiya adatuma Yehukala, mwana wa Semaliya ndi wansembe Zefaniya, mwana wa Maseiya, kwa mneneri Yeremiya kukamuuza kuti, “Mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wathu.”
4Pa nthaŵi imeneyo nkuti Yeremiya asanaponyedwe m'ndende, choncho anali ndi ufulu wotha kuyenda pakati pa anthu.
5M'menemonso nkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka ku Ejipito. Ndipo pamene Ababiloni ozinga mzinda wa Yerusalemu ndi zithando zankhondo adamva zimenezo, adachokako ku Yerusalemuko.
6Tsono Chauta adauza mneneri Yeremiya kuti,
7“Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti mfumu ya ku Yuda imene idakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa Ine, uiwuze kuti, ‘Gulu lankhondo la Farao limene lidaabwera kuti lidzakuthandize, posachedwa libwerera kwao ku Ejipito, dziko lake.
8Ndipo Ababiloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Adzaugonjetsa ndi kuutentha.’
9Zimene akunena Chauta ndi izi, akuti musadzinyenge ndi kumaganiza kuti Ababiloni adzachoka ndi kukusiyani. Pepani sadzachoka ai.
10Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse la Ababiloni limene mukumenyana nalo nkhondo, ngakhalenso mwa iwowo mutatsala ovulala okhaokha m'mahema mwao, iwo omwewo adzadzambatuka nkuutentha mzindawu.”
11Pamene gulu lankhondo la Ababiloni lidaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao,
12Yeremiya adanyamuka kuchoka ku Yerusalemu kupita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake.
13Pamene adafika pa Chipata cha Benjamini, mlonda wina wapamenepo, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, adagwira Yeremiya, nati, “Iwetu ukuthaŵira kwa Ababiloni ati!”
14Yeremiya adati, “Zimenezo ai, si zoona. Ine sindikuthaŵira kwa Ababiloni.” Koma Iriyayo sadamumvere ndipo adamgwira nabwera naye kwa akuluakulu.
15Akuluakulu aja adamkwiyira Yeremiya. Adamkwapula, namtsekera m'nyumba ya mlembi Yonatani imene adaaisandutsa ndende.
16Yeremiya adaikidwa m'ndende ya pansi pa nthaka, nakhala m'menemo nthaŵi yaitali.
17Tsiku lina mfumu idatuma anthu kuti akaitane Yeremiya, ndipo idamlandira. Idamufunsa paseri m'nyumba mwake kuti, “Kodi pali mau amene Chauta wakuuza?” Yeremiya adayankha kuti, “Inde, alipo. Inu amfumu mudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya ku Babiloni.”
18Ndipo adafunsa mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo, aphungu anu, kapena anthu anu kuti mundiponye m'ndende?
19Kodi ali kuti aneneri anu aja amene adakuloserani kuti mfumu ya ku Babiloni sidzakuthirani nkhondo inuyo ndi dziko lanu?
20Tsono ndikukupemphani inu mfumu mbuyanga, kuti mumve pempho langa. Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuwopa kuti ndingakafereko.”
21Pamenepo mfumu Zedekiya adalamula kuti Yeremiya asungidwe ku bwalo la alonda. Tsono ankamupatsa chakudya tsiku ndi tsiku, mtanda umodzi wa buledi. Ankamugula kwa anthu opanga buledi, mpaka buledi yense mumzindamo adatha. Motero Yeremiya adakhala m'bwalo la alonda.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.