Lun. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kupembedza zolengedwa nkwachabe

1Anthu onse okhala osadziŵa Mulungu,

kupusa kwao nkwachibadwa.

Anthuwo sadathe kumudziŵa Iye uja

amene alipo poona ntchito zake zokoma,

adalephera kuzindikira mmisiri poona ntchito zake.

2Koma moto, mphepo, mpweya wopepuka,

magulu a nyenyezi, madzi othamanga,

kapena miyuni yamumlengalenga,

ndizo ankaziyesa milungu

yolamulira dziko lapansi.

3Ngati zolengedwa zina ankaziyesa milungu

chifukwa cha kukongola kwake,

azindikire m'mene Mwini wake amaziposera,

chifukwa Mlengi wa kukongola konseko

ndi amene adazilenga.

4Ngati anthu adadabwa ndi mphamvu za zinthuzo

ndi ntchito zake,

amvetse m'mene wozilenga wake

amazipambanira pa mphamvu.

5Pajatu ukulu ndi ubwino wa zolengedwa

umatithandiza kumvetsa

za m'mene aliri Mlengi wake.

6Komabe anthu otereŵa kulakwa kwao nkochepa,

chifukwa mwina amangosokera

pofunafuna Mulungu ndi kuyesa kumpeza.

7Pamene akukhala pakati pa ntchito zake,

amazifufuzafufuza,

nkumakopeka ndi maonekedwe ake,

popeza kuti zimene akuwonazo

zimakhala zokongoladi.

8Komabe anthu otereŵa ngopalamula ndithu,

9chifukwa adalandira nzeru zokwanira

zoti nkumvetsako zinthu zapansipanozi,

komabe sadathe kumudziŵa mwamsanga

Mwiniwake wa zinthu zimenezi.

Kupembedza mafano nkupusa

10 Yes. 44.9-20; Yer. 10.1-16; Yere. 1.8-73 Tsoka kwa amene amakhulupirira

zinthu zopanda moyo,

amene amatchula zinthu zopangidwa

ndi manja a anthu kuti ndi milungu,

monga golide ndi siliva wozokotedwa bwino,

kapenanso zithunzi za nyama,

kapena mwala wopandapake

umene udazokotedwa kale ndi munthu wina.

11Mmisiri wamatabwa angathe kudula mtengo

wogwirika bwino,

nakungunula bwino khungwa lake.

Mwa luso lake mtengowo amapanga nawo chiŵiya

chimene chili chothandiza pa moyo wa munthu.

12Tsono zotsala za ntchito yake

amaphikira chakudya kuti akhute.

13Koma pakati pa zotsala zomwezo,

china chopandapake, chokhotakhota

ndi chamagonyamagonya,

amachitenga nachisema mochenjera ndi mwaluso,

pamene alibe ntchito zina,

mpaka chimakhala chithunzi cha munthu.

14Kapenanso amapanga nacho chithunzi cha nyama yachabe,

amachipaka utoto wofiira kuti chifiire,

naphimba maanga ake onse ndi utoto womwewo.

15Kenaka amachikonzera malo ake pa khoma nkuchiikapo,

nachikhomera misomali yachitsulo.

16Amachita choncho kuti chingagwe pansi,

chifukwa amadziŵa kuti pa chokha

sichingachite kanthu,

poti ndi chithunzi chabe chofunika kuchigwirira.

17Komabe akafuna kupempherera zinthu zake,

ukwati wake ndi ana ake,

sachita manyazi kucheza ndi chinthu chopanda moyo.

18Amapempha moyo wolimba kwa chinthu chofooka,

amapempha moyo umene kwa chinthu chakufa,

amapempha chithandizo kwa chinthu chopanda mphamvu konse,

amapempha ulendo wabwino kwa chinthu chosayenda.

19Akafuna kupata ndalama, kupeza ntchito,

ndi kukhoza pa ntchito zake,

amapempha kwa chinthu

chimene manja ake sangathe kuchita kanthu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help