1 Num. 21.21-35; Deut. 2.26—3.11 Aisraele anali atagonjetsa dziko lonse la kuvuma kwa Yordani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni m'chigwa cha Yordani, mpaka kumpoto ku phiri la Heremoni ndi dera lonse la kuvuma kwa Araba, ndipo adakhazikika pa dziko lonselo. Mafumu amene adaŵagonjetsawo ndi aŵa,
2Sihoni mfumu ya Aamori amene ankakhala ku Hesiboni. Iyeyu ankalamulira kuyambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki ku malire a dziko la Aamoni, ndiponso kuphatikizapo theka la dera la Giliyadi.
3Dzikolo lidaphatikizaponso chigwa cha Yordani, kuyambira kumwera kwa nyanja ya Galilea, kumapita cha ku Beteyesimoti, mzinda umene uli pafupi pa Nyanja Yakufa, mpaka kumwera ndithu, patsinde pa phiri la Pisiga.
4Aisraele adagonjetsanso Ogi, mfumu ya ku Basani, amene anali mmodzi mwa otsala a Arefaimu. Iyeyu ankakhala ku Asitaroti ndi ku Ederei.
5Ufumu wake unkafika mpaka ku phiri la Heremoni ndi ku Saleka, ndi ku Basani yense, mpaka ku malire a Agesuri ndi a Amakati. Ufumuwo unkaphatikizanso theka la Giliyadi, kufikira ku dziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni.
6Num. 32.33; Deut. 3.12 Mose pamodzi ndi Aisraele adaaŵagonjetsa onsewo, ndipo Mose mtumiki wa Chauta adaapereka maiko aoŵa kwa fuko la Rubeni ndi la Gadi, ndiponso kwa theka la fuko la Manase, kuti akhale choloŵa chao.
Mafumu ogonjetsedwa ndi Yoswa.7Yoswa ndi Aisraele anali atagonjetsa mafumu onse okhala m'dziko la kuzambwe kwa Yordani, kuyambira ku Bala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni, mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa adagaŵira mafuko a Aisraele dziko limenelo, kuti likhale choloŵa chao.
8Dziko limenelo lidaali lamapiri, lachipululu, ndiponso dziko louma lakumwera. M'dziko limeneli ndimo m'mene munkakhala Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
9Mafumu amene adagonjetsedwawo ndi aŵa: mafumu a ku Yeriko, Ai pafupi ndi Betele,
10Yerusalemu, Hebroni,
11Yaramuti, Lakisi,
12Egiloni, Gazere,
13Debiri, Gederi,
14Horoma, Aradi,
15Libina, Adulamu,
16Makeda, Betele,
17Tapuwa, Hefere,
18Afeki, Lasaroni,
19Madoni, Hazori,
20Simironi-Meroni, Akisafu,
21Tanaki, Megido,
22Kedesi, Yokoneamu (m'Karimele),
23Dori (m'mbali mwa nyanja), Goimu (m'Galilea),
24ndi Tiriza. Mafumu onse analipo 31.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.