1Pa chaka cha khumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio, mfumu ya ku Roma, Ponsio Pilato anali bwanamkubwa ku Yudeya. Herode ankalamulira ku dera la Galileya. Filipo, mbale wake, ankalamulira ku dera la Itureya ndi ku dera la Trakoniti. Lisaniasi ankalamulira ku dera la Abilene,
2ndipo Anasi ndi Kayafa anali akulu a ansembe onse. Pa nthaŵi imeneyo Mulungu adampatsira uthenga Yohane uja, mwana wa Zakariya, m'chipululu.
3Choncho Yohaneyo adayendera dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yordani, akulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima ndi kubatizidwa, kuti Mulungu akukhululukireni machimo anu.”
4 chifukwa chokwatira Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndiponso chifukwa cha zoipa zina zambiri zimene ankachita.
20Pambuyo pake, kuwonjezera pa zonsezi, Herode adatsekera Yohaneyo m'ndende.
Yesu abatizidwa(Mt. 3.13-17; Mk. 1.9-11)21Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka,
22Gen. 22.2; Mas. 2.7; Yes. 42.1; Mt. 3.17; Mk. 1.11; Lk. 9.35ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi ngati la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”
Makolo a Yesu23Yesu anali ndi zaka ngati makumi atatu pamene adayamba ntchito yake ya kuphunzitsa. Anthu ankamuyesa mwana wa Yosefe, amene anali mwana wa Eli,
24mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe,
25mwana wa Matatiasi, mwana wa Amosi, mwana wa Nahumu, mwana wa Hesili, mwana wa Nagai,
26mwana wa Mahati, mwana wa Matatiasi, mwana wa Semeini, mwana wa Yoseke, mwana wa Yoda,
27mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Salatiele, mwana wa Neri,
28mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elimadama, mwana wa Ere,
29mwana wa Yose, mwana wa Eliezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi,
30mwana wa Simeoni, mwana wa Yudasi, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu,
31mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natamu, mwana wa Davide,
32mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Sala, mwana wa Nasoni,
33mwana wa Aminadabu, mwana wa Adimini, mwana wa Arini, mwana wa Hesiromu, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda,
34mwana wa Yakobe, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahoro,
35mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Ebere, mwana wa Sela,
36mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,
37mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani,
38mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, amene anali mwana wa Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.