1 Ako. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zimene mtumwi ayenera kulandira

1Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi suja ine ndidamuwona Yesu Ambuye athu? Kodi suja inu ndinu zipatso za ntchito yanga yogwirira Ambuye?

2Ngakhaletu ena sandiyesa mtumwi, koma kwa inu ndine mtumwi ndithu, pakuti moyo wanu wachikhristu ndi umboni wakuti ndinedi mtumwi.

3Zimene ndimaŵayankha ofufuza za ine ndi izi:

4Kodi si koyenerera kwa ife kumalandira chakudya ndi chakumwa?

5Kodi si koyenerera kwa ife kuti ŵaakazi azitsagana nafe pa maulendo athu, monga zikuchitikira ndi atumwi ena ngakhalenso abale a Ambuye ndiponso Kefa.

6Kodi ine ndi Barnabasi, ndife tokha oyenera kugwira ntchito zamanja kuti tizidzipezera tokha zotisoŵa.

7Kodi alipo msilikali womadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi alipo munthu wobzala mpesa, koma osadyako zipatso zake? Kodi alipo munthu wokhala ndi ziŵeto, koma osamwako mkaka wake?

8Kodi zimene ndikunenazi ndi nzeru za anthu chabe? Suja Malamulo a Mose amanena zomwezi?

9 Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota.

26Nchifukwa chake ndimathamanga monga munthu wodziŵa kumene walinga. Ndiponso ndikamachita mpikisano womenyana, sindichita ngati munthu amene angomenya mophonya.

27Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help