1Chauta adauza Mose kuti,
2“Uza Aisraele kuti, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
3Musamachita zimene amachita anthu a ku Ejipito kumene munkakhala kuja, ndiponso musadzachite zimene amachita anthu a ku Kanani kumene ndikukufikitsaniko. Musatsate miyambo yao.
4Muzichita zimene ndikukulamulani, ndi kutsata malamulo anga ndi kuŵamvera. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
5 kuti ungaipitse dzina la Mulungu wako. Ine ndine Chauta.
22Lev. 20.13 Usagone ndi mwamuna ngati mkazi. Chimenecho ndi chinthu chonyansa.
23Eks. 22.19; Lev. 20.15, 16; Deut. 27.21 Ndipo usagone ndi nyama ndi kudziipitsa nayo, ngakhalenso mkazi aliyense asadzipereke kwa nyama kuti agone nayo, pakuti chimenecho ndi chisokonezo choopsa.
24“Musadziipitse ndi zinthu zimenezi, chifukwa mitundu ina ya anthu amene ndikuipirikitsa inu mukubwera, idadziipitsa ndi zoipa zoterezi.
25Dziko lidaipa kotero kuti ndidalanga tchimo lake, ndipo dzikolo lidasanza anthu ake okhalamo.
26Koma inuyo mutsate malamulo anga ndi kuchita zimene ndikukulamulani. Musachite chilichonse mwa zonyansazi, ngakhale inu mbadwanu kapena mlendo wokhala pakati panu.
27Pajatu anthu am'dzikomo amene adaalipo inu musanafike, ankachita zonyansa zonsezi, kotero kuti dziko lidaipitsidwa.
28Musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mukaliipitsa, monga momwe lidasanzira mtundu wa anthu umene udaalipo m'dzikomo, inu musanafike.
29Pakuti aliyense amene adzachita zonyansa zimenezi, adzachotsedwa pakati pa anthu anzake.
30Tsono mverani malamulo anga oletsa kutsata zonyansa zimene anthu ankazichita, inu musanafike. Musadziipitse nazo konse. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.