Yob. 35 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Elihu adaonjeza kuti,

2“Kodi mukuganiza kuti mukukhoza:

Kunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu?’

3Kapena kufunsa kuti,

‘Kodi kuchimwa kwanga ubwino wake ndi wotani?

Nanga ndikadapindulanji ndikadaleka kuchimwa?’

4Ndidzakuyankhani inuyo

ndi abwenzi anu omwe.

5Muyang'ane kumwamba,

ndipo muwone mitambo imene ili kutali ndi inuyi.

6 Yob. 22.2, 3 Kodi mukamachimwa,

ndiye kuti mukumchita Mulungu chiyani?

Mukamachulukitsa machimo anu, kodi mumamvuta bwanji?

7Kodi mukati ndinu wosalakwa,

ndiye kuti mukumpindulira chiyani?

Kodi angathe kulandiranji kwa inu?

8Kuipa kwanu kumangovuta anthu anzanu,

chimodzimodzinso ntchito zanu zabwino

zimangopindulira anzanu basi.

9“Anthu akufuula chifukwa cha kuzunzidwa.

Akupempha chithandizo

chifukwa anthu amphamvu akuŵavula.

10Koma palibe wonena kuti,

‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga,

amene amatithandiza ngakhale pakati pa mdima wa mavuto,

11amenenso amatiphunzitsa kupambana nyama zam'dziko

ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zouluka.’

12Ena amaitana Mulungu koma Iye saŵayankha,

chifukwa cha kunyada ndi kuipa kwa anthuwo.

13Ndithudi, Mulungu saamva kupempha kopanda pake,

Mphambe sasamalako zimenezo.

14“Inu aYobe, mukunena kuti simungathe kupenya Mulungu,

komabe mlandu wanu adzauzenga ndiye,

ndipo mukudikira kuti augamule.

15Ndiye tsono, popeza kuti

ukali wake sukupereka chilango,

ndipo akuchita ngati sasamalako

kwambiri zochita zoipa za anthu,

16inu aYobe mumangolankhula zopandapake,

mukungochulukitsa mau opanda nzeru.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help