1 Gen. 1.26-28 Luntha linkasunga munthu woyamba,
tate wa mtundu wa anthu,
pamene anali yekha, Mulungu atamulenga.
Munthuyo atachimwa, luntha lidamupulumutsa,
2ndipo lidamupatsa mphamvu
zolamulira zolengedwa zonse.
3 Gen. 4.8-13 Koma pamene wina wosalungama
adasiyana ndi luntha mwaukali,
adaonongeka chifukwa cha kupha
mbale wake mwachipseramtima.
4 Gen. 7.1—8.22 Pamene dziko lino lapansi lidaamira m'madzi
chifukwa cha iyeyo,
luntha lidaapulumutsa dzikolo
poongolera olungama aja
pa mtengo wachabechabe.
5 Gen. 11.1-9; 12.1-3; 22.1-19 Pamene mitundu ya anthu idasokonezeka
itapangana kuti ichite choipa,
luntha lidapatulapo munthu
amene anali wolungama,
nkumusunga wopanda cholakwa pamaso pa Mulungu.
Lidamulimbitsanso kuti angafooke
ndi chisoni chomvera mwana wake.
6 Gen. 19.1-29 Luntha lidapulumutsanso munthu wina wolungama
pamene anthu oipa adaonongeka.
Iyeyo adathaŵa moto umene udagwa pa mizinda isanu ija.
7Mboni ya kuipa kwao ndi nthaka youma
imene sileka kufuka utsi,
imene mbeu zake zimabereka zipatso zimene sizipsa.
Ndipo chipilala chamchere chili pompo chikhalire,
ngati chikumbutso cha mtima wosakhulupirira.
8Anthuwo atasiyana ndi luntha,
sadathenso kuzindikira zabwino,
koma adasiyira amoyo mbiri ya kupenga kwao,
kuti zolakwa zao zizikumbukika nthaŵi zonse.
9Koma luntha lidapulumutsa atumiki ake
m'zovuta zao.
10 Gen. 27.43; 28.10-22; 32.24-30 Munthu wolungama uja amene ankathaŵa
ukali wa mbale wake,
lidamuwongolera pa njira zolungama.
Lidamuwonetsa ufumu wa Mulungu
ndi kumudziŵitsa zinthu zoyera.
Lidamupambanitsa pa ntchito zake zoŵaŵa
ndipo lidachulukitsa phindu la ntchito zake.
11Lidamutchinjiriza pakati pa anthu
ofuna kumchenjerera,
ndipo lidamulemeretsa.
12Lidamuteteza kwa adani ake,
ndipo lidamupulumutsa pakati pa anthu
ofuna kumutchera misampha.
Lidamupambanitsa pa ndeu yolimbana koopsa,
kuti aphunzire kuti kutumikira Mulungu
kumalimbitsa munthu kupambana zonse.
13 Gen. 37.12-36; 39.1-23; 41.37-44 Munthu wina wolungama atagulitsidwa
luntha silidamusiye,
lidamutchinjiriza kuti asachimwe.
Lidaloŵa naye ndi m'ndende momwe.
14Silidamusiye ali m'maunyolo,
koma lidamupatsa ndodo yaufumu
ndi mphamvu zolamulira
eni ake ovuta a dzikolo.
Anthu amene ankamuneneza,
lidaŵatsutsa kuti ndi abodza,
kenaka lidamupatsa ulemu wamuyaya.
Mulungu alezera mtima Ejipito15 Eks. 1.1—15.21 Luntha lidapulumutsa
anthu oyera mtima ndi osachimwa
kwa mtundu wa anthu oŵazunza.
16Lidaloŵa mu mtima wa mtumiki wa Ambuye,
ndipo lidachita zizindikiro ndi zozizwitsa
polimbana ndi mafumu oopsa.
17Anthu oyera mtima lidaŵapatsa malipiro
a ntchito zao zoŵaŵa,
lidaŵaongolera pa njira yodabwitsa.
Masana linali ngati mthunzi wao,
usiku linali ngati chilangali
choŵala ngati nyenyezi.
18Lidaŵaolotsa Nyanja Yofiira,
ndi kuŵapititsa pakati pa madzi ozama.
19Lidamiza adani ao pansi pa nyanja,
kenaka nkuŵavuulira ku mtunda.
20Motero anthu olungama adafunkha chuma
cha anthu osamva aja.
Adaimbira dzina lanu loyera Inu Ambuye,
onse ndi mtima umodzi
adatamanda dzanja lanu loŵateteza.
21Luntha lidatsekula pakamwa
pa anthu osalankhula,
lidamasula lilime la ana akhanda.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.