Chiv. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Buku lino likufotokoza zimene Yesu Khristu adaulula. Mulungu adampatsa zimenezi kuti aonetse atumiki a Mulunguyo zomwe zikuyenera kudzachitika posachedwa. Khristu pofuna kudziŵitsa zinthuzo mtumiki wake Yohane, adachita kutuma mngelo wake kwa iye.

2Yohaneyo wafotokoza zonse zimene adaziwona, ndipo wachitira umboni mau a Mulungu, ndiponso zonse zimene Yesu Khristu adanena.

3Ngwodala munthu amene aŵerenga momveka mauŵa. Ngodalanso anthu amene amvera mau a m'buku limeneli loneneratu zam'tsogolo, ndi kutsata zimene zalembedwamo. Pakuti nthaŵi yoti zichitike zonsezi ili pafupi.

Yohane apereka moni kwa mipingo isanu ndi iŵiri

4 Eks. 3.14; Chiv. 4.5 Ndine, Yohane, ndikulembera mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asiya. Akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere Mulungu amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza. Ikukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere mizimu isanu ndi iŵiri yokhala patsogolo pa mpando wachifumu wa Mulungu.

5Yes. 55.4; Mas. 89.27Akukomereninso mtima ndi kukupatsani mtendere Yesu Khristu, mboni yokhulupirika, amene ali woyambirira kulandira moyo waulemerero, amenenso ali Mfumu yolamula mafumu onse a pa dziko lapansi. Iyeyo amatikonda, ndipo ndi magazi ake adatimasula ku machimo athu.

6Eks. 19.6; Chiv. 5.10Iye adatisandutsa mafumu, kuti tizitumikira Mulungu Atate ake modzipereka ngati mtundu wa ansembe. Motero Yesu Khristuyo alandire ulemerero ndi mphamvu zolamulira mpaka muyaya. Amen.

7 Dan. 7.13; Mt. 24.30; Mk. 13.26; Lk. 21.27; 1Ate. 4.17; Zek. 12.10; Yoh. 19.34, 37; Zek. 12.10; Mt. 24.30 Mvetsetsani! Akubwera pa mitambo! Aliyense adzamuwona, amene adamubaya aja nawonso adzamuwona. Ndipo anthu a mitundu yonse pansi pano adzalira chifukwa cha Iye. Nzoonadi zimenezi. Ndithudi!

8 Chiv. 22.13; Eks. 3.14 “Ine ndine Woyamba ndiponso Wotsiriza,” akutero Ambuye Mulungu, Mphambe, amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza.

Yohane aona Khristu m'masomphenya

9Ndine, Yohane, mbale wanu, ndipo ngati mnzanu wokhulupirira Yesu, ndili nanu limodzi mu ufumu wa Mulungu, komanso m'masautso ndi m'kupirira kosatepatepa. Ndidaponyedwa pa chilumba cha Patimosi, chifukwa cha kulalika mau a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni.

10Pa tsiku la Ambuye ndidaagwidwa ndi Mzimu Woyera, nkumva kumbuyo kwanga liwu lamphamvu ngati kulira kwa lipenga.

11Liwulo lidati, “Zimene ukuwonazi, uzilembe m'buku ndipo ulitumize kwa mipingo isanu ndi iŵiri iyi: wa ku Efeso, wa ku Smirina, wa ku Pergamo, wa ku Tiatira, wa ku Sardi, wa ku Filadelfiya ndi wa ku Laodikea.”

12Nditacheuka kuti ndiwone akundilankhula ndani, ndidaona ndodo zoikapo nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide.

13Dan. 7.13; Dan. 10.5 Pakati pake pa ndodo za nyalezo ndidaona wina wooneka ngati mwana wa munthu. Anali atavala mkanjo wautali, atamangira lamba wagolide pa chifuwa.

14Dan. 7.9

Dan. 10.6Tsitsi lake linali loyera ngati thonje loyera kwambiri, ngati chipale chambee; maso ake ngati malaŵi a moto;

15Ezek. 1.24; 43.2; 2Es. 6.17mapazi ake ali chezichezi ngati mkuŵa woyeretsedwa m'ng'anjo ya moto; liwu lake ngati mkokomo wa madzi ochuluka.

16M'dzanja lake lamanja adaanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri, ndipo m'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse lotulukira kunja. Nkhope yake inali yoŵala ngati dzuŵa lamasana.

17 Yes. 44.6; 48.12; 2Es. 10.30; Chiv. 2.8; 22.13 Nditamuwona, ndidagwa kumapazi kwake ngati munthu wakufa. Koma Iye adandisanjika dzanja lake lamanja nati, “Usaope. Woyamba ndiponso Wotsiriza ndine.

18Wamoyo uja ndine. Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya. Imfa ndi Malo a anthu akufa makiyi ake ali ndi Ine.

19Lemba tsono zimene waziwona, ndiye kuti zimene zikuchitika tsopano ndi zimene zidzachitike bwino lino.

20Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija zimene waziwona m'dzanja langa lamanja, ndi china chija cha ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide, tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija ndi atsogoleri a mipingo isanu ndi iŵiri; ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zija ndi mipingo isanu ndi iŵiri imene.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help