Bar. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Machimo a Ayuda ndi kulapa kwao

1 , nthaŵi imene Ababiloni adalanda mzinda wa Yerusalemu ndi kuutentha.

3 2Maf. 24.8-17 Baruki adaŵerenga mau a m'bukulo pamaso pa Yekoniya mwana wa Yowakimu, mfumu ya Ayuda, pamaso pa anthu onse amene adadza kudzamva za m'bukulo.

4Adaŵaŵerenga pamaso pa akalonga ndi akazembe a banja la mfumu, akuluakulu, anthu otchuka, ndiponso ngakhale anthu wamba ndi anthu onse okhala ku Babiloni, pafupi ndi mtsinje wa Sudi.

5Atamva mauwo, anthu adalira, nasala zakudya, ndipo adapemphera kwa Ambuye.

6Adasonkhanitsa ndalama monga momwe aliyense ankathera,

7ndi kuzitumiza ku Yerusalemu kwa Yowakimu, mkulu wa ansembe, mwana wa Hilikiya, mwana wa Salumu, ndi kwa ansembe ndi kwa anthu onse amene anali nawo ku Yerusalemu.

8Nthaŵi imeneyi, tsiku lakhumi la mwezi wa Sivani, Baruki adatenga ziŵiya za ku Nyumba ya Ambuye, zimene zidaachotsedwa ku Nyumba ya Mulungu, kuti azibwezere ku dziko la Yuda. Zimenezi zinali ziŵiya zasiliva zimene adaazipangitsa Zedekiya, mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda.

9Nthaŵiyo nkuti Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, atachotsa Yekoniya ku Yerusalemu, pamodzi ndi akuluakulu a m'nyumba mwake, anthu ogwidwa pa nkhondo, akalonga ndiponso anthu wamba. Onsewo adaatengedwa kupita ku Babiloni.

Anthu a ku ukapolo alemba kalata ku Yerusalemu

10Anthuwo adanena kuti, “Tikukutumizirani ndalama zoti mugulire nyama zoperekera nsembe zootcha ndiponso nsembe zopepesera machimo. Zina mugulire lubani. Mukonzenso nsembe zatirigu ndi kuzipereka pa guwa la Ambuye Mulungu wathu.

11Mupempherere Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni ndiponso Belisazara mwana wake, kuti masiku ao pansi pano achuluke ngati akumwamba.

12Choncho Ambuye adzatipatsa mphamvu ndi kutiwunikira njira. Ndipo Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ndi Belisazara mwana wake, adzatitchinjiriza. Tidzaŵatumikira pa nthaŵi yaitali ndipo adzatikomera mtima.

13Ifenso mutipempherere kwa Ambuye, Mulungu wathu, chifukwa tidaŵachimwira. Ndipo mpaka lero lino, Ambuye sanalekebe kutikwiyira ndi kutisungira ukali.

14“Chonde liŵerengeni buku limene tikukutumiziranili, ndipo mulape machimo anu m'Nyumba ya Ambuye pa masiku a chikondwerero cha mahema ndi masiku ena opembedza.”

Kulapa machimo

15Munene kuti, “Ambuye Mulungu wathu, ngolungama. Koma ife lero manyazi atigwira. Atigwira tonsefe anthu a ku Yuda, mbadwa za ku Yerusalemu.

16Agwira mafumu athu ndi akalonga athu, ansembe athu, aneneri athu ndiponso makolo athu.

17Zatero chifukwa tonsefe tachimwira Ambuye,

18ndipo sitidaŵamvere. Sitidamvere Ambuye Mulungu wathu, sitidatsate malamulo amene Iwo adatipatsa.

19Kuyambira tsiku limene Ambuye adatulutsa makolo athu m'dziko la Ejipito mpaka lero lino, sitidamvere Ambuye Mulungu wathu ndipo sitidasamale mau ao.

20Deut. 28.15-68Nchifukwa chake mpaka lero mavuto ndi matemberero akhala akutigwera, monga momwe Ambuye adaanenera kudzera mwa Mose mtumiki wao, tsiku limene adatulutsa makolo athu ku Ejipito, kuti atipatse dziko lamwanaalirenji.

21Zoonadi, tidakana kutsata mau a Ambuye Mulungu wathu, amene adalankhula kudzera mwa aneneri amene adaŵatuma kwa ife.

22Koma aliyense adatsata zofuna za mtima wake woipa, pakutumikira milungu ina, ndi kuchita zoipa pamaso pa Ambuye Mulungu wathu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help