1Tsopano ndiyankhe zimene mudandifunsa m'kalata yanu. Nkwabwino kuti munthu asakwatire,
2koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.
3Mwamuna azipereka kwa mkazi wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mkazi wake, momwemonso mkazi azipereka kwa mwamuna wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mwamuna wake.
4Mkazi thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mwamuna wake yemwe. Momwemonso mwamuna thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mkazi wake yemwe.
5Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.
6Pamene ndikunena zimenezi, sindikuchita mokulamulani ai, koma mokulolani chabe.
7Kwenikweni ndikadakonda kuti anthu onse akhale ngati ine, koma Mulungu adapatsa munthu aliyense mphatso yakeyake, wina mphatso yakuti, winanso yakuti.
8Kwa amene sali pa banja, ndiponso kwa azimai amasiye, mau anga ndi aŵa: Nkwabwino kuti iwo akhalebe paokha choncho ngati ineyo.
9Koma ngati sangathe kudziletsa, aloŵe m'banja, pakuti nkwabwino kuloŵa m'banja kupambana kupsa ndi moto wa zilakolako.
10 Mt. 5.32; 19.9; Mk. 10.11, 12; Lk. 16.18 Kwa anthu am'banja lamulo langa, limenetu kwenikweni ndi lochokera kwa Ambuye, ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake.
11Koma ngati amuleka, akhale wosakwatiwanso, kapena ayanjane nayenso mwamuna wakeyo. Chimodzimodzinso mwamuna asasudzule mkazi wake.
12Kwa ena mau anga, osati a Ambuye ai, ndi aŵa: Ngati mkhristu ali ndi mkazi wachikunja, ndipo mkaziyo avomera kukhala naye, mwamunayo asathetse ukwatiwo.
13Momwemonso ngati mkhristu wamkazi ali ndi mwamuna wachikunja, ndipo mwamunayo avomera kukhala naye, mkaziyo asathetse ukwatiwo.
14Pakuti mwamuna wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mkazi wakeyo. Nayenso mkazi wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mwamuna wakeyo. Pakadapanda apo, bwenzi ana anu atakhala akunja, koma monga zilirimu, ndi ana a Mulungu.
15Koma ngati wakunja uja afuna kuleka mkhristu, amuleke. Zikatero, ndiye kuti mkhristu wamwamunayo kapena wamkaziyo ali ndi ufulu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale ndi moyo wamtendere.
16Kodi iwe, mkazi wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzampulumutsa mwamuna wako? Kapenanso iwe, mwamuna wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzapulumutsa mkazi wako?
Za kuitanidwa ndi Mulungu17Aliyense atsate moyo umene Ambuye adamkonzera, moyo umene Mulungu adamuitanira. Ndizo zimene ndimaŵalamula anthu onse amumpingo.
181Am. 1.15Ngati wina Mulungu adamuitana ali woumbalidwa, asavutike nkubisa kuumbala kwakeko. Chimodzimodzi ngati wina adamuitana ali wosaumbalidwa, asaumbalidwe.
19Kuumbala si kanthu ai, kusaumbala si kanthunso. Kanthu nkutsata malamulo a Mulungu.
20Aliyense angokhala monga momwe analiri pamene Mulungu adamuitana.
21Kodi unali kapolo pamene Mulungu adakuitana? Usavutike nazo. Komanso ngati upeza mwai woti ulandire ufulu, uugwiritse ntchito mwaiwo.
22Pakuti munthu amene anali kapolo pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi mfulu ya Ambuye. Momwemonso amene anali mfulu pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi kapolo wa Khristu.
23Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono musasanduke akapolo a anthu.
24Abale, aliyense angokhala pamaso pa Mulungu monga momwe analiri pamene Mulunguyo adamuitana.
Ayankha mafunso ena okhudza za ukwati25Kunena za amene sali pa banja, ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye. Koma ndikuuzani maganizo anga, ngati munthu amene Ambuye adandichitira chifundo kuti ndikhale wokhulupirika.
26Chifukwa cha masautso a nthaŵi ino, ndiyesa nkwabwino kuti munthu akhale monga momwe aliri.
27Kodi ndiwe wapabanja? Usayese kuthetsa banja lako. Kodi ndiwe wopanda banja? Usayese kupeza banja.
28Komabe ngati ukwatira, sukuchimwa ai. Ndipo ngati namwali akwatiwa, sakuchimwa ai. Komabe oloŵa m'banja adzakumana ndi zovuta m'moyo wao, ndipo pano ndingofuna kukupewetsani zovutazo.
29Chimene ndikukuuzani, abale, nchakuti nthaŵi yachepa. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale monga ngati sadakwatire.
30Amene akulira, akhale monga ngati sakulira, amene akukondwa, akhale monga ngati sakukondwa, amene akugula zinthu, akhale monga ngati sali nazo zinthuzo.
31Ndipo amene akugwiritsa ntchito zinthu zapansipano, zisaŵagwire mtima zinthuzo. Pakuti dziko lino lapansi, monga liliri tsopanomu, likupita.
32Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye.
33Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake.
34Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake.
35Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati kuti ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye.
36Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai.
37Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino.
38Ndiye kuti, munthu wokwatira namwali amene adamtomera, akuchita bwino, koma woleka osamkwatira, akuchita bwino koposa.
39Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu.
40Koma m'mene ndikuganizira ine, adzakhala wokondwa koposa ngati akhala wosakwatiwanso. Ndipo ndikuyesa inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.