1Tsiku limene Chauta adaapulumutsa Davide kwa adani ake onse ndiponso kwa Saulo,
2Davideyo adaimbira Chauta nyimbo iyi yakuti,
“Chauta ndiye thanthwe langa,
linga langa ndi mpulumutsi wanga.
3Ndiye Mulungu wanga ndi thanthwe langa
limene ndimathaŵirako.
Ndiye chishango changa,
ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga.
Ndiye linga langa ndi mpulumutsi wanga.
Ndinu amene mumandiwombola pa nkhondo.
4Ndimaitana Chauta,
amene ayenera kumtamanda,
ndipo amandipulumutsa kwa adani anga.
5“Zoŵaŵa za imfa zidandizinga,
mitsinje ya ku malo a anthu akufa idandisefukira.
6Nthambo zakumanda zidandizeŵeza,
misampha ya imfa idandikola.
7“Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga,
ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize.
Iye ali m'Nyumba mwake adamva liwu langa,
kulira kwanga kofuna chithandizo
kudamveka kwa iye.
8“Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera
ndi kuchita chivomezi.
Maziko akumwamba adagwedezeka ndi kulilima
chifukwa Chauta adaakalipa.
9M'mphuno mwake munkafuka utsi,
m'kamwa mwake munkatuluka moto woononga,
makala amoto anali laŵilaŵi
kuchokera m'kamwa momwemo.
10Adang'amba thambo natsika pansi,
mdima wabii unali ku mapazi ake.
11Adakwera pa mkerubi nauluka,
adayenda mwaliŵiro ndi mphepo.
12Mdima adausandutsa chofunda chake,
mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake.
13M'kuŵala kumene kunali pamaso pake
munkafumira makala amoto alaŵilaŵi.
14Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu,
Wopambanazonse liwu lake lidamveka.
15Adaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake.
Adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa.
16Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera,
maziko a dziko lapansi adakhala poyera,
pamene Chauta adakhuluma mokalipa,
pamene adatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwake.
17“Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira,
ndi kundivuula m'madzi ozama.
18Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu,
kwa onse amene ankadana nane;
pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine.
19Adaniwo adandithira nkhondo
pamene ndinali m'mavuto,
koma Chauta adandichirikiza.
20Adakandifikitsa ku malo amtendere,
adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane.
21“Chauta adandipatsa mphotho
molingana ndi kulungama kwanga,
adandifupa molingana ndi ungwiro wanga.
22Ine ndidatsata njira za Chauta
sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga.
23Ndidamvera malangizo ake onse,
ndipo malamulo ake sindidaŵataye.
24Ndinalibe mlandu pamaso pake,
ndinkalewa zoipa m'moyo wanga.
25Nchifukwa chake Chauta wandipatsa mphotho
molingana ndi kulungama kwanga,
monga momwe akuwonera kuti ndilibe mlandu.
26“Kwa anthu okhulupirika,
Inu Mulungu mumadziwonetsa okhulupirika,
kwa anthu aungwiro
mumadziwonetsa abwino kotheratu.
27Kwa anthu oyera mtima
mumadziwonetsa okoma mtima,
koma kwa anthu oipa mtima
mumadziwonetsa ochenjera koposa.
28Paja anthu odzichepetsa
Inu mumaŵapulumutsa,
koma anthu odzikuza mumaŵatsitsa.
29Ndithu Inu Chauta, ndinu nyale yanga,
Inu Mulungu, mumandiwunikira mu mdima.
30Ndi chithandizo chanu
ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo.
Ndi chithangato chanu, Inu Mulungu,
ndingathe kupambana.
31Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro,
mau a Chauta ndi oona.
Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
32“Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha.
Palibe thanthwe lina lothaŵirapo
koma Mulungu wathu yekha?
33Mulungu wathu ndiye linga langa lolimba,
wandichotsera zoopsa m'njira zanga.
34 Hab. 3.19 Amalimbitsa mapazi anga ngati a mbaŵala,
ndipo amandisunga bwino ku mapiri.
35Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo,
kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.
36Inu mwanditeteza
ndi chishango chanu chachipulumutso.
Mwandikweza ndi chithandizo chanu.
37Mwalimbitsa miyendo yanga kuti ndiyende bwino,
choncho mapazi anga sadaterereke.
38Ndidalondola adani anga ndi kuŵapeza,
sindidabwerere mpaka nditaŵagonjetsa.
39Ndidaŵakantha, ndidaŵagwetsa pansi,
kotero kuti sadadzukenso,
ndidaŵapondereza ndi mapazi anga.
40Paja ndinu mudandipatsa mphamvu zomenyera nkhondo,
ndinu mudandigonjetsera anthu ondiwukira.
41Inu mudapirikitsa adani anga kuti andithaŵe,
amene ankadana nane ndidaŵaononga.
42Adakuwa, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woŵapulumutsa.
Adalirira Chauta, koma sadaŵayankhe.
43Ndidaŵaperapera ngati fumbi,
ndidaŵaphwanya ndi kuŵapondereza ngati matope amumseu.
44“Mudandipulumutsa kwa anthu anga ondiwukira.
Mudandisunga kuti ndikhale wolamulira mitundu yonse.
Choncho anthu osaŵadziŵa adayamba kunditumikira.
45Anthu a maiko ena adabwera kwa ine kudzapemba;
atangomva mau anga oyamba adandimvera.
46Anthu a mitundu ina adataya mtima,
adatuluka m'malinga mwao ali njenjenje.
47“Chauta ndiwamoyo.
Litamandike thanthwe langa,
alemekezeke Mulungu wanga,
thanthwe londipulumutsa.
48Mulungu ndiye adandithandiza kuti ndilipsire,
ndi kugonjetsa anthu a mitundu ina
kuti akhale mu ulamuliro wanga.
49Ndinu amene mudandipulumutsa kwa adani anga.
Mudandikweza pamwamba pa ondiwukira,
mudandilanditsa kwa anthu ankhanza.
50 Aro. 15.9 “Chifukwa cha zimenezi ndidzakuyamikani Inu Chauta,
pakati pa mitundu ya anthu,
ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
51Mulungu amathandiza mfumu yake
kuti izipambana nthaŵi ndi nthaŵi.
Amaonetsa chikondi chake chosasinthika
kwa wodzozedwa wake,
ndiye kuti kwa Davide
ndi kwa zidzukulu zake mpaka muyaya.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.