Mk. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kusudzulana(Mt. 19.1-12; Lk. 16.18)

1Yesu adachoka ku Kapernao, napita ku dera la ku Yudeya ndi ku dera la kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Anthu ambirimbiri adadzasonkhananso kwa Iye, ndipo monga ankazoloŵera, adayambanso kuŵaphunzitsa.

2Tsono kudafika Afarisi ena, namufunsa kuti, “Kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake?” Pomufunsa chonchi ankangofuna pomupezera chifukwa.

3Koma Yesu poyankha adati, “Kodi Mose adakulamulani zotani?”

4Deut. 24.1-4; Mt. 5.31 Iwo adati, “Mose adalola kuti munthu azilembera mkazi wake kalata yachisudzulo kenaka nkumuchotsa.”

5Yesu adati, “Mose adaakulemberani lamulo limeneli chifukwa cha kukanika kwanuku.

6Gen. 1.27; 5.2 Komatu pachiyambi paja, pamene Mulungu adalenga zonse, adaŵalenga anthu, wina wamwamuna wina wamkazi.

7Gen. 2.24 Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ndi amai, nakaphatikizana ndi mkazi wake,

8ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi. Choncho tsopano salinso aŵiri, koma thupi limodzi.

9Tsono zimene Mulungu wazilumikiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”

10Pamene adaloŵanso m'nyumba, ophunzira adamufunsanso Yesu za nkhani yomweyi.

11Mt. 5.32; 1Ako. 7.10, 11Iye adaŵauza kuti, “Aliyense amene asudzula mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo.

12Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.”

Yesu adalitsa ana(Mt. 19.13-15; Lk. 18.15-17)

13Anthu ena ankabwera ndi ana kwa Yesu kuti aŵakhudze ndi kuŵadalitsa, ophunzira ake nkumaŵazazira.

14Yesu ataona zimenezi, adakalipa naŵauza kuti, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.

15Mt. 18.3Ndithu ndikunenetsa kuti yemwe salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.”

16Atatero adayamba kuŵafungata anawo, naŵasanjika manja ndi kuŵadalitsa.

Za munthu wina wolemera(Mt. 19.16-30; Lk. 18.18-30)

17Pamene Yesu ankanyamuka kuti azipita, munthu wina adamthamangira. Adadzamugwadira namufunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?”

18Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi.

19Eks. 20.13; Deut. 5.17; Eks. 20.14; Deut. 5.18; Eks. 20.15; Deut. 5.19; Eks. 20.16; Deut. 5.20; Eks. 20.12; Deut. 5.16 Malamulo ukuŵadziŵa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.”

20Munthu uja adati, “Aphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsata kuyambira ndili mwana.”

21Yesu atamuyang'ana, adamkonda nkumuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

22Atamva zimenezo, munthu uja nkhope yake idagwa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa adaali munthu wa chuma chambiri.

23Yesu adayang'ana ophunzira ake amene adaamzungulira naŵauza kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

24Ophunzirawo adadabwa nawo kwambiri mau akeŵa. Koma Yesu adabwerezanso, adati, “Ndithu, inu ana anga, nkwapatali kukaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.

25Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wachuma akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

26Pamenepo ophunzira aja adazizwa koposa, nayamba kufunsana kuti, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?”

27Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu nkosathekadi, koma ndi Mulungu ai, nkotheka. Paja ndi Mulungu zonse nzotheka.”

28Pamenepo Petro adayamba kulankhula naye, adati, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.”

29Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ndiponso chifukwa cha Uthenga Wabwino,

30ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale: nyumba, abale, alongo, amai, ana, minda, komanso mazunzo. Ndipo kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.

31Mt. 20.16; Lk. 13.30Komatu ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsirizira, ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”

Yesu aneneratu kachitatu za kufa ndi kuuka kwake(Mt. 20.17-19; Lk. 18.31-34)

32Pamene iwo anali pa ulendo wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayenda patsogolo pa ophunzira ake. Ophunzirawo anali oda nkhaŵa kwambiri. Ndipo anthu amene ankaŵatsatira anali ndi mantha. Yesu adaŵaitaniranso pambali ophunzira khumi ndi aŵiri aja, nayamba kuŵafotokozera zimene zinalikudzamugwera.

33Adati, “Tilitu pa ulendo wa ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe. Ndipo akampereka kwa anthu akunja.

34Amenewo akamchita chipongwe, akamthira malovu, akamkwapula nkumupha. Koma patapita masiku atatu, Iye adzauka.”

Zopempha za Yakobe ndi Yohane(Mt. 20.20-28)

35Yakobe ndi Yohane, ana aja a Zebedeo, adadzauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ife timati bwanji titakupemphani kanthu, mutichitire.”

36Yesu adaŵafunsa kuti, “Inuyo mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?”

37Iwo adati, “Timafuna kuti pamene mudzakhale mu ulemerero wanu, mudzatiike wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.”

38Lk. 12.50Koma Yesu adati, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine? Kodi inu mungathe kulandira nao ubatizo wa mavuto umene ndikudzalandira Ine?”

39Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.” Apo Yesu adati, “Chabwino, chikho chimene Ine ndikudzamwacho, inunso mudzamwa nao, ndipo ubatizo umene Ine ndikudzalandirawo, inunso mudzalandira nao.

40Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Mulungu ndiye adzapereke malo ameneŵa kwa omwe Iye mwini adaŵakonzera.”

41Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima Yakobeyo ndi Yohaneyo.

42Lk. 22.25, 26Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo, naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti pakati pa anthu akunja, anthu amene amati ngolamulira, amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao.

43Mt. 23.11; Mk. 9.35; Lk. 22.26Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu.

44Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse.

45Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”

Yesu achiritsa munthu wakhungu(Mt. 20.29-34; Lk. 18.35-43)

46Yesu ndi ophunzira ake pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu adafika ku mzinda wa Yeriko. Tsono pamene ankatuluka mumzindamo, adapeza wakhungu wina wopemphapempha atakhala pansi pamphepete pa mseu. Munthuyo dzina lake anali Baratimeo, mwana wa Timeo.

47Tsono iyeyo atamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, adayamba kufuula kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.”

48Anthu ambiri adamzazira kuti akhale chete. Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.”

49Yesu adaima, nauza anthu kuti, “Tamuitanani.” Anthu aja adamuitana wakhunguyo namuuza kuti, “Limba mtima, nyamuka, akukuitana.”

50Pomwepo iye uja adadzambatuka, mwinjiro wake uko chi, kuthamangira kwa Yesu.

51Yesu adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Wakhunguyo adayankha kuti, “Mbuyanga, ndikufuna kuti ndizipenyanso.”

52Yesu adamuuza kuti, “Chabwino, ungathe kupita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthaŵi yomweyo adayambadi kupenya, nkumatsata Yesu pa ulendowo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help