Mas. 94 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu woweruza onse

1Inu Chauta, ndinu Mulungu wolipsira,

Inu Mulungu wolanga, dziwonetseni.

2Dzambatukani, Inu Muweruzi wa dziko lapansi,

apatseni anthu onyada zoŵayenerera.

3Inu Chauta, kodi anthu oipa adzadzitamabe mpaka liti?

4Amalankhula modzikuza

ndipo amanyadira zoipa zao.

5Amatswanya anthu anu, Inu Chauta,

amazunza anthu anu osankhidwa.

6Amapha akazi amasiye

ndi alendo okhala nawo m'dziko mwao,

amaphanso ana amasiye.

7Kenaka amati,

“Chauta sakuwona, Mulungu wa Yakobe sakuzidziŵa.”

8Mvetsani anthu opusa kwambirinu.

Zitsiru inu, mudzakhala ndi nzeru liti?

9Kodi amene adalenga makutu, sangathe kumva?

Kodi amene adapanga maso, sangathe kupenya?

10Kodi wolangiza mitundu ya anthu, sangathe kulanga?

Kodi wophunzitsa anthu onse, alibe nzeru?

11 1Ako. 3.20 Chauta amadziŵa maganizo a anthu

kuti ndi mpweya chabe.

12Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza,

amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu.

13Mumampumitsa pa nthaŵi yamavuto,

mpaka woipa ataloŵa m'dzenje.

14Chauta sadzaŵataya anthu ake,

sadzaŵasiya okha osankhidwa ake.

15Chilungamo chidzaŵabwereranso kwa anthu ake,

ndipo onse oongoka mtima adzachitsata.

16Ndani amalimba mtima

kuti andimenyere nkhondo ndi anthu oipa?

Ndani amaimira mbali yanga,

kuti alimbane ndi anthu ochita zoipa?

17Chauta akadapanda kundithandiza,

bwenzi posachedwa nditapita ku dziko lazii.

18Pamene ndinkaganiza kuti,

“Phazi langa likuterereka,”

nkuti chikondi chanu chosasinthika chikundichirikiza.

19Pamene nkhaŵa zikundichulukira,

Inu mumasangalatsa mtima wanga.

20Kodi angathe kugwirizana nanu olamulira oipa,

amene amapotoza malamulo anu olungama?

21Amagwirizana kuti aononge anthu osalakwa,

nagamula kuti opanda mlandu aphedwe.

22Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza,

Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.

23Adzaŵalanga chifukwa cha machimo ao,

adzaŵaononga chifukwa cha kuipa kwao,

zoonadi, Chauta, Mulungu wathu,

ndiye amene adzaŵafafanize.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help