1Muyeso wonyenga umanyansa Chauta,
koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa.
2Kunyada kukaloŵa, pamafikanso manyazi,
koma pali kudzichepetsa, palinso nzeru.
3Ungwiro wa anthu olungama umaŵatsogolera,
koma makhalidwe okhota a anthu onyenga ngoononga.
4Pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu
chuma sichithandiza konse,
koma chilungamo ndiye chimapulumutsa ku imfa.
5Kulungama kwa anthu angwiro
kumaŵathandiza pa moyo wao,
koma kuipa mtima kumagwetsa mwiniwake yemweyo.
6Kulungama kwa munthu woyera mtima kumampulumutsa,
koma zilakolako zoipa
zimaŵaika mu ukapolo anthu onyenga.
7Woipa akafa, chikhulupiriro chake chimathanso,
chiyembekezo cha wosasamala za Mulungu chilibe phindu.
8Anthu a Mulungu amapulumuka ku mavuto,
koma m'malo mwake amagwamo ndi oipa mtima.
9Munthu wosalabadirako za Mulungu
amaononga mnzake ndi pakamwa pake;
munthu wochita chilungamo amapulumuka
chifukwa cha kudziŵa zinthu.
10Mulungu akamadalitsa anthu ake,
mzinda wonse umatukuka.
Oipa akaonongeka, anthu amafuula mwachimwemwe.
11Madalitso olandira anthu olungama amakweza mzinda,
koma pakamwa pa anthu oipa mtima pamapasula mzindawo.
12Wosukitsa anzake ngwopanda nzeru,
koma womvetsa zinthu amalonda pakamwa pake.
13Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi.
Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake.
14 Lun. 6.24 Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa,
koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.
15Woperekera wachilendo chigwiriro, adzapeza mavuto,
koma wodana ndi za chigwiriro, amakhala pa mtendere.
16Mkazi wa mkhalidwe wabwino amalandira ulemu,
koma amuna ankhanza amangopata chuma.
17Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino,
koma munthu wankhwidzi amadzipweteka yekha.
18Munthu woipa amalandira malipiro achabechabe,
koma wochita zolungama amalandira mphotho yeniyeni.
19Wofunitsitsa chilungamo, adzakhala moyo.
Koma wothamangira zoipa, adzafa.
20Anthu a mtima woipa amamnyansa Chauta,
koma anthu a makhalidwe abwino amamkondweretsa.
21Zoonadi, anthu oipa chilango sichidzamuphonya,
koma anthu a Mulungu adzapulumuka.
22Momwe chimaonekera chipini chagolide
chikakhala pa mpuno wa nkhumba,
ndi momwenso kumakhalira kukongola kwa mkazi wam'kamwa.
23Zimene anthu abwino amazilakalaka zimathera mwabwino,
koma zimene oipa amayembekezera
zimathera ku mkwiyo wa Mulungu.
24Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu,
komabe amanka nalemereralemerera.
Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka.
25Munthu wa mtima waufulu adzalemera,
wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.
26Anthu amatemberera munthu womana anzake chakudya,
koma amalemekeza munthu wogulitsa chakudyacho.
27Munthu wofunafuna zabwino mwakhama, amapeza zokoma,
koma wofunafuna zoipa, zidzampeza.
28Wokhulupirira chuma chake adzafota,
koma anthu a Mulungu adzaphukira ngati tsamba laliŵisi.
29Wovutitsa a m'nyumba mwake adzaloŵa m'mavuto,
chitsiru chidzasanduka kapolo wa munthu wanzeru.
30Kukhala moyo wangwiro kumapezetsa moyo,
koma kusatsata malamulo kumaononga moyo.
31 1Pet. 4.18 Anthu abwino amalandira mphotho pa dziko lapansi,
koma wochimwa ndi woipa mtima amalandira chilango.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.