Yer. 40 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yeremiya apita kwa Gedaliya

1Chauta adalankhula ndi Yeremiya pa nthaŵi imene Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo adammasula ku Rama. Adaampeza ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi am'ndende ena a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda opita nawo ku Babiloni.

2Mtsogoleriyo adatenga Yeremiya namuuza kuti, “Chauta, Mulungu wako, adanena kuti adzaononga malo ano.

3Ndipo zimenezi wazichitadi monga momwe adaanenera, chifukwa chakuti inu anthu mudachimwira Chauta, simudamumvere.

4Koma iwe Yeremiya, lero ndikukumasula maunyolo m'manjamu. Tiye ku Babiloni ngati ufuna, ndipo ndidzakusamala bwino. Koma ngati sufuna kupita, palibe kanthu. Dziko ndi lonseli monga ukuwonera, upite kumene uwona kuti nkoyenera.

5Ngati supita, ubwerere kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani amene mfumu ya ku Babiloni idaamsankha kuti akhale bwanamkubwa wa mizinda ya ku Yuda. Ukakhale ndi iyeyo pakati pa anthu, kapena upite kulikonse kumene ufuna.” Tsono mtsogoleri wa nkhondo uja adampatsa chakudya, nampatsanso mphatso, ndipo adamuuza kuti, “Ai, pita bwino!”

6Pamenepo Yeremiya adapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa. Ndipo adakhala naye pakati pa anthu otsala m'dzikomo.

Gedaliya akhala bwanamkubwa ku Yuda(2 Maf. 25.22-24)

7 2Maf. 25.22-24 Panali atsogoleri ena ankhondo amene sadadzipereke nao. Iwowo pamodzi ndi anthu ao adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idaika Gedaliya, mwana wa Ahikamu, kuti akhale bwanamkubwa wa dzikolo, aziyang'anira anthu osauka kwambiri aja, amuna, akazi ndi ana, amene sadaŵatenge ukapolo kupita nawo ku Babiloni.

8Tsono amene adapita kwa iye ku Mizipa ndi aŵa: Ismaele mwana wa Netaniya, Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti, ana aamuna a Efayi a ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa Maaka, iwowo pamodzi ndi anthu ao.

9Onsewo, Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, adaŵalonjeza molumbira kuti, “Musaope kuŵagwirira ntchito Ababiloniwo. Khalani m'dzikomu, muzimera mfumu ya ku Babiloni, ndipo zinthu zonse zidzakuyenderani bwino.

10Ine nditsalira ku Mizipa kuti ndizikuimirirani kwa Ababiloni akamabwera. Koma inu mutenge zipatso zanu, vinyo wanu, mafuta anu, ndipo muzisunge ndithu. Muzikhala m'mizinda imene mwalandayo.”

11Nawonso Ayuda a ku Mowabu, ku Amoni ndi ku Edomu ndi a ku maiko ena, adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idasiyako anthu ena ku Yuda, ndipo kuti idaŵaikira Gedaliya, mwana wa Ahikamu mdzukulu wa Safani, kuti akhale bwanamkubwa wao.

12Tsono Ayuda onsewo adabwera kuchokera ku maiko onse kumene adaabalalikira. Adabwerera ku Yuda nakadziwonetsa kwa Gedaliya ku Mizipa. Ndipo minda yao idabereka zipatso zambiri ndi vinyo wambiri.

Gedaliya aphedwa(2 Maf. 25.25-26)

13Tsiku lina Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri ankhondo amene sadadzipereke aja, adapita kwa Gedaliya ku Mizipa.

14Adamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaele, mwana wa Netaniya kuti adzakupheni?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sadaŵakhulupirire.

15Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwachinsinsi adauza Gedaliya kuti, “Loleni kuti ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniyayu, ndipo wina aliyense sadzadziŵa. Nanga inu akuphereninji ndi kulola kuti Ayuda onse okuzunguliraniŵa amwazikane, ndipo otsala a ku Yuda adzaonongedwe?”

16Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu adayankha Yohanani mwana wa Kareya kuti, “Iyai, usachite zotero. Zimene ukunena za Ismaele nzabodza.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help