Num. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za malamulo a nsembe

1Chauta adauza Mose kuti,

2“Uza Aisraele kuti, ‘Mukadzaloŵa m'dziko limene ndidzakupatsenilo,

3mwina muzidzapereka ng'ombe kapena nkhosa kwa Chauta kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, kapena yopsereza, kapena yopembedzera, kuti mukwaniritse zimene mudalonjeza molumbira. Mwina mudzazipereka kuti zikhale nsembe yaufulu kapena nsembe yopereka pa nthaŵi ya zikondwerero zosankhidwa, kuti zikhale nsembe zotulutsa fungo lokomera Chauta.

4Tsono amene adzabwere ndi zoperekayo, adzapereke kwa Chauta chopereka cha chakudya, cholemera kilogaramu limodzi, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi.

5Adzaperekenso vinyo wa chopereka cha chakumwa wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense, kuwonjezera pa nsembe yopsereza kapena pa nsembe yopembedzera.

6Ikakhala nkhosa yamphongo, muzipereka chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu aŵiri, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi ndi theka.

7Pachopereka cha chakumwa, mudzapereka vinyo wokwanira lita limodzi ndi theka, kuti ikhale nsembe yotulutsa fungo lokomera Chauta.

8Pamene mupereka ng'ombe yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yopsereza kapena nsembe yopembedzera, kapena kuti zichitikedi zimene mudalumbira, kapena kuti ikhale nsembe yachiyanjano,

9muperekere kumodzi ndi ng'ombeyo chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta okwanira malita aŵiri.

10Pachopereka cha chakumwa mupereke vinyo wokwanira malita aŵiri, kuti ikhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.’

11“Umu ndimo m'mene zidzachitikire ndi ng'ombe yamphongo iliyonse, kapena nkhosa yamphongo, kapena mwanawankhosa aliyense kapena mwanawambuzi.

12Zingachuluke chotani nyama zoperekedwazo, muchite choncho ndi nyama iliyonse, mpaka zonse kutha.

13Mbadwa zonse zizichita motero pamene zikupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.

14Ngati ndi mlendo amene akhala pakati panu, kapena wina aliyense amene akhala pakati panu pa mibadwo yanu yonse, ndipo afuna kupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta, azichita monga momwe muchitira inu.

15Kunena za msonkhano wonse, pakhale lamulo limodzi lokha kwa inu ndi kwa alendo amene akhale pakati panu, lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse. Monga momwe muliri inu, alendonso ali momwemo pamaso pa Chauta.

16Lev. 24.22 Kwa inu ndi kwa mlendo wokhala pakati panu, pakhale lamulo limodzi ndi mwambo umodzi wokha.”

17Chauta adauza Mose kuti,

18“Uza Aisraele kuti, ‘Mukadzaloŵa m'dziko m'mene ndidzakufikitsani,

19ndipo mukamadzadya buledi wam'dzikolo, mudzapereke nsembe kwa Chauta.

20Pa buledi wanu woyamba, mudzaperekeko mmodzi kuti adzakhale nsembe. Mudzampereke monga momwe mumaperekera zopereka za popunthira tirigu.

21Muzidzapereka motero kwa Chauta buledi mmodzi mwa buledi wanu woyamba pa mibadwo yanu yonse.’

22“Koma mwina mutha kulakwa mosadziŵa, osasunga malamulo onse amene Chauta adauza Mose,

23ndi zonse zimene adakulamulani kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Chauta adapereka lamulo mpaka m'tsogolo mwake pa mibadwo yanu yonse.

24Ngati cholakwacho chidachitika mosadziŵa, mpingo womwe osazindikira, pamenepo mpingo wonsewo upereke mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Apereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chakumwa, potsata zimene ndidakulamulani. Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo.

25Wansembe achite mwambo wopepesera machimo a mpingo wonse wa Aisraele ndipo anthuwo adzakhululukidwa, chifukwa choti adalakwa mosadziŵa. Tsono atabwera ndi zopereka zao ngati nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, ndiponso ngati nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta, kuti azimpepesa pa cholakwa chao chija,

26mpingo wonse wa Aisraele udzakhululukidwa pamodzi ndi mlendo yemwe amene akhala pakati pao, poti anthu onse adalakwa mosadziŵa.

27 Lev. 4.27-31 “Ngati munthu mmodzi alakwa mosadziŵa, apereke mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo.

28Motero wansembe amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta munthu wolakwa mosadziŵayo. Akalakwa choncho mosadziŵa, amchitire mwambo wopepesera machimo, ndipo adzakhululukidwa.

29Mukhale ndi lamulo limodzi pa munthu aliyense amene alakwa mosadziŵa, pa mbadwa iliyonse pakati pa Aisraele ndi pa mlendo amene akhala pakati pao.

30Koma munthu amene achimwa dala, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, wanyoza Chauta, ndipo munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.

31Popeza kuti wanyoza mau a Chauta ndipo waphwanya lamulo la Chauta, amchotseretu munthu ameneyo, tchimo lake lidzamkangamira.”

Munthu wonyoza tsiku la Sabata

32Pamene Aisraele anali m'chipululu muja, adapeza munthu akutola nkhuni pa tsiku la Sabata.

33Amene adapeza munthuyo akutola nkhuni, adabwera naye kwa Mose ndi Aroni ndi kwa mpingo wonse.

34Iwo adamponya m'ndende chifukwa choti sankadziŵa bwino zoti amchite.

35Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Munthuyo aphedwe. Mpingo wonse umponye miyala kunja kwa mahema.”

36Pomwepo mpingo udamtulutsira kunja kwa mahema munthuyo ndi kumupha pomponya miyala, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.

Malamulo a mphonje zapazovala

37Chauta adauza Mose kuti,

38Deut. 22.12 “Lankhula ndi Aisraele, ndipo uŵauze kuti pa mibadwo yao yonse azisokerera mphonje pa ngodya za zovala, ndipo pa mphonje ya ngodya iliyonse asokerepo chingwe chobiriŵira.

39Mphonje imeneyo muzidzaiyang'ana ndi kumakumbukira malamulo onse a Chauta, kuti muziŵamvera, ndipo musamatsatenso zilakolako zokhota za mtima wanu kapena za maso anu zimene munkazitsata.

40Choncho mudzakumbukira ndi kugwiritsa ntchito malamulo anga onse, mudzakhala oyera mtima pamaso pa Mulungu wanu.

41Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help