1Munthu wokonda mwana wake amamkwapula
kaŵirikaŵiri,
kuti adzakondwerere makulidwe a mwanayo.
2Munthu wopatsa mwambo mwana wake,
adzakondwera naye,
ndipo adzamunyadira pakati pa anzake.
3Munthu wophunzitsa bwino mwana wake adani
ake adzachita naye nsanje,
ndipo iyeyo adzamnyadira pakati pa abwenzi ake.
4Ngakhale bamboyo akamwalira,
amachita ngati akali moyo,
chifukwa adasiya chithunzi chake.
5Pamene anali moyo ankakondwera akamamuwona,
ndipo pamene analikufa, sadade nkhaŵa.
6Adasiya wina woti alipsire adani ake,
ndipo wina woti aŵabwezere zabwino
abwenzi ake.
7Koma amene amasasatitsa mwana wake,
adzayenera kumanga zilonda zake zomwe,
ndipo mtima wake udzavutika akamadzamumva
akulira.
8Monga kavalo wosaphunzitsa amakhala wokanika,
momwemonso mwana wopanda mwambo amakhala
wosaweruzika.
9Sasatitsa mwana wako, ndipo adzakuopseza,
seŵera naye, ndipo adzakumvetsa zoŵaŵa.
10Usamaseka naye, mwinamwina udzalira naye,
ndiye potsiriza udzalira kuti,
“Mai, kalanga ine!”
11Usamkokomeze akali wamng'ono,
ndipo usalekerere zolakwa zake.
12Umfeŵetse khosi akali wochepa,
umkwapule akali mwana.
Ukapanda kutero, adzakhala wamphulupulu
ndi wosamvera,
ndipo adzakuvutitsa kwambiri.
13Umphunzitse mwambo mwana wako osamlekerera,
mwinamwina adzakuchititsa manyazi ndi
chipongwe chake.
Za moyo wabwino14Ndi bwino kukhala munthu wosauka
koma wa moyo wamphamvu ndi wathanzi,
kupambana kukhala munthu wolemera koma wodwaladwala.
15Moyo wabwino ndi mphamvu zipambana golide,
thupi lathanzi lipambana chuma chochuluka.
16Palibe chuma cholingana ndi moyo wabwino,
palibe zokondweretsa zoposa mtima wachimwemwe.
17Ndi bwino kufa kupambana kuzunzika pa moyo
wako wonse,
ndi bwinonso kuusa kwamuyaya kupambana kudwala
nthaŵi yaitali.
18Chakudya chabwino chopatsa munthu wosafuna kudya,
chili ngati chakudya chochiika ku manda.
19Pali phindu lanji kupereka nsembe kwa fano?
Silingathe kudya kapena kununkhiza.
Chimodzimodzinso ndi munthu amene akulangika ndi Ambuye.
20Amangochiyang'ana chakudyacho nkumabuula,
ngati munthu wofulidwa akakumbatira namwali.
Za chimwemwe ndi chisoni21 Mla. 11.9, 10 Usabindikire m'chisoni,
usachite kudzivutitsa dala.
22Mtima wachimwemwe umakhalitsa moyo munthu,
ndipo kusangalala kumachulukitsa masiku ake.
23Khala wachimwemwe, sangalatsa mtima wako,
ndipo chisoni uchipirikitsire kutali,
chifukwa chisoni chidaononga anthu ambiri,
chilibe phindu kwa aliyense.
24Nsanje ndi mkwiyo zimachepetsa moyo,
ndipo nkhaŵa imakalambitsa msanga.
25Munthu wosangalala amadya bwino,
ndipo amakondwerera chakudya chake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.