1 Yob. 35.6-8 Tsono Elifazi wa ku Temani adayankha kuti,
2“Kodi munthu nkukhala waphindu kwa Mulungu?
Iyai, munthu wanzeru amangodzipindulira yekha basi.
3Kodi Mphambe angapeze bwino
chifukwa cha kulungama kwako?
Kodi kapena Iyeyo nkupindulapo kanthu
pa makhalidwe ako angwirowo?
4Kodi nchifukwa choti umamuwopa, kuti azikudzudzula,
kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
5Kodi osati nchifukwa choti kuipa kwako nkwakukulu,
ndipo kulakwa kwako nkopanda malire?
6“Iwe unkaumiriza pachabe abale ako
kuti apereke chikole,
ndipo unkaŵalanda zovala zao,
mpaka kuŵasiya ali ndi usiŵa.
7Anthu otopa sudaŵapatse madzi akumwa,
anthu anjala udaŵamana chakudya.
8Chifukwa cha mphamvu zako udalanda dziko lalikulu,
chifukwa cha kudzikonda udakhazikika m'menemo.
9Akazi amasiye udaŵachotsa opanda kanthu,
ndipo ana amasiye udaŵapondereza.
10Nchifukwa chake misamphayi yakuzinga,
ndipo wadzidzimuka ndi mantha.
11Kuli mdima ndipo sungathe kuwona kanthu,
madzi achigumula akukumiza.
12“Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba?
Ona nyenyezi zili m'mwamba kwambirizo,
ona kutalika kwake pamene ziliripo!
13Komabe umanena kuti,
‘Kodi Mulungu amadziŵa chiyani?
Wabisika ndi mitambo, nanga angatiweruze bwanji?
14Mitambo yakuda yamzinga,
kotero kuti sangathe kuwona bwino,
pamene akuyenda pamwamba pa thambopo.’
15“Kodi iwe ukufuna kuyendabe m'njira yakale
imene anthu oipa ankayendamo?
16Iwowo adachotsedwa nthaŵi yao isanakwane,
maziko ao adakokoloka ndi madzi.
17Anthuwo ankauza Mulungu kuti,
‘Chokani pali ife pano!’
Adatinso, ‘Kodi Mphambeyo nkutichita chiyani ife?’
18Chonsecho ndi Mulungu amene adaŵalemeretsa
ndi zinthu zokoma.
Nchifukwa chake ine ndekha ndiye maganizo a anthu oipa
sindigwirizana nawo.
19Anthu abwino amaona zonse ndi kukondwa,
anthu osachimwa amangoseka, akamaona oipa akulangidwa.
20Amanena kuti, ‘Ndithudi, adani athu aonongedwa,
zimene adazisiya zaonongeka ndi moto.’
21“Iwe Yobe, uziyanjana ndi Mulungu
kuti ukhale pa mtendere, ukatero udzaona zabwino.
22Uzimvera malangizo amene Iyeyo amaphunzitsa,
uziikapo mtima pa mau ake.
23Ubwerere kwa Mphambe modzichepetsa,
uchotse zosalungama zonse
zimene zimachitika m'nyumba mwako.
24Golide wako yense umuyese wachabechabe,
ndithu, chuma chamtengowapatali uchiwone ngati dothi,
25Koma Mphambe ndiye akhale ngati golide wako,
akhale ngati siliva wako wamtengowapatali.
26Ukatero udzakondwa naye Mphambe,
Udzaikapo mtima pa Mulungu mwamtendere.
27Ukadzapemphera kwa Iye adzakumvera,
udzapereka kwa Iye zija udalumbira kuti udzaperekazi.
28Chimene wachitsimikiza kuti udzachite,
chidzachitikadi,
kuŵala kudzakuunikira pa njira zako zonse.
29Pajatu Mulungu amagwetsa onyada,
koma amapulumutsa odzichepetsa.
30Amapulumutsa munthu wopanda mlandu,
adzakupulumutsa iwenso ndi kulungama kwako.”
Yobe
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.