Gen. 50 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Maliro a Yakobe

1Pomwepo Yosefe adadzigwetsa pa mtembo wa bambo wake akulira, kwinaku akumpsompsona bambo wake.

2Tsono Yosefeyo adalamula asing'anga kuti akonze ndi mankhwala mtembo wa bambo wake, kuti usaole, ndipo iwowo adachitadi zimenezo.

3Ntchitoyo idaŵatengera masiku 40, monga kunkafunikira pa ntchito ya mtundu umenewo. Aejipito adalira maliro a Israele masiku 70.

4Yosefe atatha kulira maliro a bambo wake, adauza nduna za Farao kuti, “Chonde mundikomere mtima, Farao mukamuuze kuti,

5Gen. 47.29-31 ‘Pamene bambo wanga anali pafupi kufa, adandilumbiritsa kuti ndikamuike m'manda amene adadzikumbira m'dziko la Kanani. Motero chonde, mundilole kuti ndipite ndikaike bambo wanga, pambuyo pake ndidzabweranso.’ ”

6Farao adamuyankha kuti, “Pita ukaike atate ako monga momwe adakulumbiritsira.”

7Yosefe adapita kukaika bambo wake. Ndipo nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo, ndi anthu ena otchuka a ku Ejipito adamperekeza.

8Adapitanso ndi onse a banja lake, abale ake, ndi onse a banja la bambo wake. Ku Goseni kuja kudangotsala ana okhaokha, nkhosa zao, abusa ndi ng'ombe zao.

9Asilikali okwera pa magaleta ndi akavalo, nawonso adamperekeza. Motero chinali chinamtindi cha anthu.

10Atafika ku malo opunthira tirigu ku Atadi, kuvuma kwa Yordani, adachita mwambo waulemu wamaliro, ndipo adalira maliro kumeneko masiku asanu ndi aŵiri.

11Tsono nzika za ku Kanani zitaona kulira koteroko ku Atadi kuja, zidati, “Kulira kwa maliro kotereku ndi kwa ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adaŵatchula kuti Abele-Miziraimu, ali kuvuma kwa Yordani.

12Ana a Yakobe adachitadi monga momwe bambo wao adaaŵalamulira.

13Ntc. 7.16Adamnyamula kupita ku Kanani, nakamuika m'phanga limene linali m'munda ku Makipera, kuvuma kwa Mamure. Abrahamu adagula phangalo kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda womwewo, kuti pakhale manda.

14Yosefe ataika bambo wake m'manda, adabwerera ku Ejipito ndi abale ake aja, pamodzi ndi onse amene adamperekeza.

Yosefe aŵatsimikiziranso abale ake kuti adzaŵasamala

15Atamwalira bambo wao uja, abale ake a Yosefe adati, “Nanga tidzatani ife, Yosefe akadzayamba kudana nafe ndi kufuna kubwezera zoipa zonse zimene tidamuchita zija?”

16Motero adatumiza mau kwa Yosefe kuti, “Atate anu asanafe adanena mau akuti,

17‘Ndikumpempha Yosefe kuti akhululukire cholakwa cha abale ake chimene adamchitira.’ Pepani tsopano tikhululukireni cholakwa chimene ife, akapolo a Mulungu wa atate anu, tidachita.” Atangomva zimenezi Yosefe adayambapo kulira.

18Tsono abale ake adabwera nagwada pamaso pake. Adati, “Ife tili pamaso panu ngati akapolo anu.”

19Koma Yosefe adaŵauza kuti, “Musaope ai. Ine sindingathe kudziika m'malo mwa Mulungu.

20Inu mudaapangana kuti mundichite chiwembu, koma Mulungu adazisandutsa kuti zikhale zabwino ndipo kuti zipulumutse moyo wa anthu ambiri. Choncho onsewo ali moyo lero lino chifukwa cha zimenezo.

21Tsopano inu musade nkhaŵa. Ndidzakusamalani pamodzi ndi ana anu omwe.” Motero adaŵalimbitsa mtima naŵasangulutsa.

Kumwalira kwa Yosefe

22Yosefe adakhala ku Ejipito pamodzi ndi mbumba ya atate ake. Pamene ankamwalira nkuti ali wa zaka 110.

23Adakhala moyo mpaka kuwona adzukulu ake, ana a Efuremu. Pamene ana a Makiri mwana wa Manase adabadwa, Yosefe adaŵalandira m'banja mwake.

24Ndipo adauza abale ake aja kuti, “Patsala pang'ono kuti ndikusiyeni, koma Mulungu adzakusungani ndithu, ndipo adzakutulutsani m'dziko muno, kupita nanu ku dziko limene adaalonjeza Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.”

25Eks. 13.19; Yos. 24.32; Ahe. 11.22 Kenaka Yosefe adapempha ana a Israele kuti alumbire. Adati, “Lonjezeni kuti Mulungu akakusungani, mudzasenza mafupa anga kuchoka nawo kuno.”

26Motero Yosefe adamwalira ali wa zaka 110. Mtembo wake adaukonza ndi mankhwala, naukhazika m'bokosi ku Ejipito komweko.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help