2 Mbi. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kukonzekera za kumanga Nyumba ya Chauta(1 Maf. 5.1-18)

1Tsono Solomoni adatsimikiza zoti amange nyumba yopembedzeramo Chauta ndiponso nyumba yaufumu ya iye mwini.

2Tsono adalemba anthu 70,000 osenza katundu, anthu 80,000 okakumba miyala ku dziko lamapiri, ndiponso akapitao 3,600, oyang'anira anthuwo.

3Adatumiza mau kwa Hiramu mfumu ya ku Tiro, adati, “Monga momwe munkachitira ndi Davide bambo wanga, pomamtumizira mitengo ya mkungudza, kuti amangire nyumba yake yoti azikhalamo, muchitenso momwemo ndi ine.

4Ineyo ndikufuna kuti ndimangire nyumba Chauta, Mulungu wanga, ndipo kuti ndiipereke kwa Iye, kuti ikhale yoperekeramo zofukiza za fungo lonunkhira bwino pamaso pa Mulungu, ndi yoperekeramo kosalekeza buledi wopatulika. M'nyumbamo aziperekeramonso nsembe zopsereza m'maŵa ndi madzulo, pa masiku a sabata, pa masiku okhala mwezi ndi pa masiku achikondwerero a Chauta, Mulungu wathu, potsata malamulo okhalira Aisraele mpaka muyaya.

5Nyumba imene ndimangeyo idzakhala yaikulu, pakuti Mulungu wathu ndi wamkulu kupambana milungu yonse.

61Maf. 8.27; 2Mbi. 6.18 Koma ndani angathe kummangira nyumba, poti ku mlengalenga ngakhale kumwambamwamba sikungathe kumkwanira Iye? Kodi ine ndinenso yani kuti ndingammangire nyumba, osati kamalo chabe koti nkumafukizapo lubani pamaso pa Mulungu?

7Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso wodziŵa kuzokota. Akhale pamodzi ndi anthu aluso amene ali ndi ine ku Yuda ndi ku Yerusalemu amene Davide bambo wanga adandipatsa.

8Munditumizirenso mitengo ya mkungudza, mitengo ya mlombwa ndiponso matabwa ambaŵa a ku Lebanoni, poti ndikudziŵa kuti anyamata anu amadziŵa kudula mitengo ku Lebanoni. Ndipo anyamata anga adzakhala pamodzi ndi anyamata anu,

9kuti andidulire mitengo yochuluka, popeza kuti nyumba imene ndimangeyo idzakhala yaikulu ndi yochititsa kaso.

10Anyamata anu odzadula mitengowo ndidzaŵapatsa tirigu wopunthapuntha wokwanira matani 2,000, barele wokwanira matani 2,000, vinyo wa malitara 440,000, ndiponso mafuta a malitara 440,000.”

11Tsono Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adayankha Solomoni pomulembera kalata yonena kuti, “Chifukwa chakuti Chauta amakonda anthu ake, wakuika iweyo kuti ukhale mfumu yao.”

12Adatinso, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, amene adapatsa mfumu Davide mwana wanzeru, waluntha, ndi womvetsa zinthu bwino, woti amange nyumba ya Chauta ndiponso nyumba yaufumu ya iye mwini wake.

13“Ndatuma mmisiri wanzeru, womvetsa, dzina lake Huramuabi,

14amene mai wake ndi wa ku Dani, ndipo bambo wake anali wa ku Tiro. Iyeyo ndi wodziŵa bwino ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, miyala, ndi matabwa, ndiponso nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso bafuta wosalala. Angathe kuchitanso ntchito zonse zozokota, ndi ntchito ina iliyonse imene mungampatse kuti achite pamodzi ndi anthu anu aluso, anthu aluso a mbuyanga Davide bambo wanu.

15Nchifukwa chake tsono, tirigu, barele, mafuta ndi vinyo zimene mbuyanga wanena, azitumize kwa anyamata antchitowo.

16Tsono ife tidzadula mtengo uliwonse wa ku Lebanoni umene mungaufune, ndipo tidzakutumizirani mitengoyo poimanga pamodzi ndi kuiyandamitsa pa nyanja mpaka ku Yopa, kuti inuyo muitenge ndi kupita nayo ku Yerusalemu.”

Ntchito yomanga Nyumba ya Chauta iyambika(1 Maf. 6.1-38)

17Choncho Solomoni adaŵerenga alendo onse amene anali m'dziko lonse la Israele, monga momwe bambo wake Davide adaaŵaŵerengera kale. Ndipo padapezeka anthu okwanira 153,600.

18Adapatula anthu 70,000 kuti akhale amtengatenga, ndipo anthu 80,000 kuti akhale okumba miyala ku mapiri. Tsono anthu 3,600 adaŵaika kuti akhale akapitao ogwiritsa anthu ntchito.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help