Chiv. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mwanawankhosa amatula zimatiro zisanu ndi chimodzi

1Pambuyo pake ndidaona Mwanawankhosa uja akumatula chimodzi mwa zimatiro zisanu ndi ziŵiri zija. Ndipo ndidamva chimodzi mwa Zamoyo zinai zija chikunena ndi liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!”

2Zek. 1.8; 6.3, 6Nditayang'ana, ndidaona kavalo woyera. Wokwerapo wake anali ndi uta, ndipo adaapatsidwa chisoti chaufumu. Adatulukira ngati wogonjetsa kuchokera kumwamba, kuti akagonjetsenso ena pa dziko lapansi.

3Kenaka Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachiŵiri. Ndipo ndidamva Chamoyo chachiŵiri chija chikunena kuti, “Bwera!”

4Zek. 1.8; 6.2Pamenepo kavalo wina, wofiira, adatulukira. Wokwerapo wake adaalandira mphamvu zothira nkhondo pa dziko lapansi, kuti anthu aziphana. Choncho adampatsa lupanga lalikulu.

5 Zek. 6.2, 6 Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachitatu. Ndipo ndidamva Chamoyo chachitatu chija chikunena kuti, “Bwera!” Nditayang'ana, ndidaona kavalo wakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo m'manja.

6Tsono ndidamva ngati liwu kuchokera pakati pa Zamoyo zinai zija. Lidati, “Nsengwa imodzi ya tirigu, mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi. Ndipo nsengwa zitatu za barele, mtengo wake ndi womwewonso. Koma usaononge mitengo ya mafuta ndi ya mphesa.”

7Kenaka Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachinai. Ndipo ndidamva Chamoyo chachinai chija chikunena kuti, “Bwera!”

8Ezek. 14.21Nditayang'ana, ndidaona kavalo wotuŵa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa, ndipo Malo a anthu akufa ankamutsata pambuyo. Aŵiriwo adaalandira ulamuliro pa chimodzi mwa zigawo zinai za dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi nkhondo, njala, nthenda, ndi zilombo zolusa.

9Zitatha izi, Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu. Ndipo ndidaona kunsi kwa guwa lansembe mizimu ya anthu amene adaphedwa chifukwa cha kulalika mau a Mulungu, ndiponso chifukwa chochitira mauwo umboni wamphamvu.

10Mizimuyo idafuula mokweza mau kuti, “Ambuye, Inu ndinu Mfumu yathu yoyera ndi yoona. Mudzaŵalekerera mpaka liti osaŵaimba mlandu ndi kuŵalanga anthu aja okhala pansi pano amene adatipha?”

112Es. 4.36Apo aliyense adapatsidwa mkanjo woyera, ndipo adamva mau akuti, “Bapumulani pang'ono mpaka chitakwanira chiŵerengero chathunthu cha atumiki anzanu ndi abale anu, amene nawonso ayenera kuphedwa monga inu nomwe.”

12 Chiv. 11.13; 16.18; Yes. 13.10; Yow. 2.10, 31; 3.15; Mt. 24.29; Mk. 13.24, 25; Lk. 21.25 Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi.

13Yes. 34.4Nyenyezi zakuthambo zidagwa pansi, ngati muja zimayoyokera nkhuyu zaziŵisi, mkuyu ukamagwedezeka ndi mphepo yamkuntho.

14Chiv. 16.20Thambo lidachoka monga momwe imakulungidwira mphasa akamaiyalula. Ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zidachotsedwa m'malo mwake.

15Yes. 2.19, 21Apo mafumu a dziko lapansi, atsogoleri a dziko, akulu a ankhondo, anthu olemera, anthu amphamvu, akapolo onse ndi mfulu zonse, onsewo adakabisala m'mapanga ndi m'matanthwe am'mapiri.

16Hos. 10.8; Lk. 23.30Iwowo ankafuulira mapiri ndi matanthwewo kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira, kuti wokhala pa mpando wachifumu uja angatiwone, ndipo kuti tipulumuke ku chilango cha Mwanawankhosayo.

17Yow. 2.11; Mal. 3.2Lafikadi tsiku loopsa la mkwiyo wao, ndipo angathe kulimbapo ndani?”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help