1Ndidaonanso zinthu zina m'masomphenya: ndidaona chikalata chofutukula chikuuluka.
2Mngelo uja adandifunsa kuti “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Chikalata chofutukula chikuuluka, muutali mwake mamita asanu ndi anai, muufupi mwake mamita anai ndi hafu.”
3Tsono adandiwuza kuti, “Pamenepo palembedwa temberero limene lidzagwera dziko lonse lapansi. Aliyense wakuba adzachotsedwa m'dziko potsata zimene zalembedwa mbali iyi, ndipo aliyense wolumbira zabodza nayenso adzachotsedwa potsata zimene zalembedwa mbali inai.
4Chauta Wamphamvuzonse wanena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza m'nyumba ya munthu wakuba ndi m'nyumba ya munthu wolumbira zabodza potchula dzina langa. Lidzakhala m'nyumbamo mpaka kuiwonongeratu, mitengo yake ndi miyala yake yomwe.’ ”
Mkazi m'gondolo5Pambuyo pake mngelo amene ankalankhula nane uja adabwera, nandiwuza kuti, “Upenyetsetse, uwone chinthu chikubwerachi.”
6Ndidafunsa kuti, “Kodi nchiyani?” Iye adati, “Chimenechi ndi gondolo loyesera, ndipo likutanthauza uchimo wa anthu m'dziko lonse.”
7Chovundikira chake chinali chamtovu, ndipo chitatukuka, ndidaona mkazi atakhala tsonga m'gondolomo.
8Mngeloyo adati, “Ameneyu akutanthauza kuipa konse.” Atatero adakankhira mkaziyo m'gondolo muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.
9Nditayang'ananso, ndidaona akazi aŵiri okhala ndi mapiko onga a kakoŵa. Akaziwo ankabwera chouluka ndi mphepo. Adanyamula gondolo lija, kupita nalo pakati pa dziko lapansi ndi mlengalenga.
10Tsono ndidafunsa mngelo amene ankalankhula nane kuti, “Nanganso gondololi akupita nalo kuti?” Iye adandiyankha kuti,
11“Akupita nalo ku dziko la Sinara kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzakhazikamo gondololo pa phaka lake.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.