1Abale, chimene ndimakhumbitsa ndi mtima wanga wonse, ndipo chimene ndimapempha Mulungu, ndi chakuti Aisraele apulumuke.
2Ndikuŵachitira umboni kuti ndi achangudi pa zinthu za Mulungu, koma changu chake sadachimvetse bwino m'mene chiyenera kukhalira.
3Sadziŵa chilungamo chochokera kwa Mulungu, koma adayesa kupezeka kuti ngolungama pamaso pake mwa njira yaoyao, osagonjera chilungamo chochokera kwa Mulungu.
4Khristu adafikitsa Malamulo a Mose ku mapherezero, kotero kuti aliyense wokhulupirira, amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.
Chipulumutso nchokhalira onse5 Lev. 18.5 Kunena za chilungamo chimene chimapezeka pakumvera Malamulo, Mose adalemba kuti, “Munthu wochita zimene Malamulo amanena, adzakhala ndi moyo pakuzichita.”
6Deut. 30.12-14 Koma kunena za chilungamo chimene chimapezeka pakukhulupirira, akuti, “Mumtima mwako usanene kuti, ‘Ndani adzakwera Kumwamba?’ ” (Ndiye kuti kukamuuza Khristu kuti atitsikire ife.)
7“Usanenenso kuti, ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (Ndiye kuti kukamubwezera Khristu kuchokera ku dziko la anthu akufa.)
8Koma nanga akuti chiyani? Akuti,
“Mau sali nawe kutali,
ali pakamwa pako, ndiponso mumtima mwako.”
(Ameneŵa ndiwo mau a chikhulupiriro amene timaŵalalika.)
9Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
10Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka.
11Yes. 28.16 Paja Malembo akuti, “Munthu aliyense wokhulupirira Iye, sadzachita manyazi.”
12Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa mooloŵa manja onse otama dzina lake mopemba.
13Yow. 2.32 Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
14Kodi anthu angatame Mulungu bwanji mopemba ngati sadamkhulupirire? Ndipo angamkhulupirire bwanji ngati sadamve za Iye? Ndipo angamve za Iye bwanji ngati palibe wina wolalika?
15Yes. 52.7 Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti,
“Nchokondweretsa zedi
kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”
16 Yes. 53.1 Koma si onse amene adalandira Uthenga Wabwinowo. Ndi monga mneneri Yesaya anenera kuti, “Ambuye, ndani adakhulupirira zimene tidalalika?”
17Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
18 Mas. 19.4 Koma ntafunsa: kodi ndiye kuti Aisraele sadaŵamve mauwo? Iyai, kumva adamva ndithu. Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti,
“Liwu lao lidamveka pa dziko lonse lapansi,
mau ao adafika mpaka ku malekezero a dziko.”
19 Deut. 32.21 Ntafunsanso: monga nkuti Aisraele sadaŵamvetse mauwo? Mose ndiye woyamba kuyankhapo. Iye adati,
“Ndidzakuchititsani kaduka
ndi mtundu umene suli mtundu weniweni,
ndidzakukwiyitsani ndi mtundu wa anthu opusa.”
20 Yes. 65.1 Ndipo Yesaya adaanena molimba mtima kuti,
“Adandipeza anthu amene sanali kundifunafuna.
Ndidaŵaonekera anthu amene sankafunsa za Ine.”
21 Yes. 65.2 Koma za Aisraele adati, “Tsiku lonse ndidatambalitsa manja anga kwa mtundu wa anthu osandimvera ndi ondiwukira Ine.”
Za chifundo cha Mulungu chochitira AisraeleWho We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.